Lamulo la Makhalidwe Abwino—Kodi Nchifukwa Ninji Lidakagwirabe Ntchito?
GOLIDI woyengeka samafwifwa, chotero zokometsera zagolidi zimawonedwa kukhala za mtengo wapatali ndi zaphindu. M’malo motaya zinthu zagolidi zowonongeka, akatswiri a chipala amakonzanso chitsulo cha mtengocho kuti apange ntchito yatsopano ya manja chifukwa chakuti golidi amasunga phindu lake.
Mofananamo, ngakhale kuti Yesu analongosola Lamulo la Makhalidwe Abwino zaka zikwi ziŵiri zapitazo, phindu lake silinazimiririkebe. Mwa kusanthula, kapena kupenda zifukwa za kugwira ntchito kwake, tingamvetsetse bwino lomwe phindu lake kwa ife lerolino.
Pamene Yesu anatipatsa Lamulo la Makhalidwe Abwino lakuti, “zinthu zirizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero,” iye anawonjezera kuti: “Pakuti ichi ndicho chilamulo ndi aneneri.” (Mateyu 7:12) Kodi ndimotani mmene ophunzira a Yesu ndi ena omvetsera kwa iye anamvetsetsera zimenezi?
‘Chimene Chilamulo ndi Aneneri Chimatanthauza’
“Chilamulo” chinalozera ku zolembedwa zoyambirira zimene zinapanga mabukhu asanu oyambirira a Baibulo, Genesis mpaka Deuteronomo. Amene amavumbula chifuno cha Yehova cha kubweretsa mbewu yomwe ikachotsa kuipa. (Genesis 3:15) Chophatikizidwa m’mabukhu a Baibulo oyambirirawo chinali Chilamulo, kapena mpambo wa malamulo, amene Yehova anapereka mu 1513 B.C.E. ku mtundu wa Israyeli kupyolera mwa Mose monga nkhoswe pa Phiri la Sinai.
Chilamulo chaumulungu chinalekanitsa Israyeli ndi mitundu ina yachikunja yowazinga, ndipo Aisrayeli sanaloledwe kuchita chirichonse chimene chikaswa kaimidwe kawo koyanjidwa pamaso pa Yehova. Iwo anali chuma chake kotheratu ndipo anayenera kukhalabe choncho kuti alandire madalitso ake. (Eksodo 19:5; Deuteronomo 10:12, 13) Koma kuwonjezera ku mathayo awo kwa Mulungu, Chilamulo cha Mose chinapereka kwa Aisrayeli thayo lakuchita zabwino kwa alendo ogonera mu Israyeli. Mwachitsanzo, icho chinanena kuti: “Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m’dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m’dziko la Aigupto; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.” (Levitiko 19:34) Mkati mwa nyengo ya mafumu mu Israyeli, alendo ogonera anasangalala ndi mwaŵi wambiri, wonga ngati kutenga mbali m’kumanga kachisi wa Mulungu m’Yerusalemu.—1 Mbiri 22:2.
Chilamulo choperekedwa kwa Israyeli chinaletsa chigololo, kupha, kuba ndi kusirira. Zoletsa zimenezi, limodzi ndi “lamulo lina lirilonse,” zingamangike pamodzi mu mfundo yakuti, “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe wekha.” Mtumwi Paulo anawonjezera kuti: “Chikondano sichichitira mnzake choipa; chotero chikondanocho chiri chokwanitsa lamulo.”—Aroma 13:9, 10.
Ngati Chilamulo chinayala maziko enieni a Lamulo la Makhalidwe Abwino, bwanji ponena za “Aneneri”?
Mabukhu aulosi a Malemba Achihebri mofananamo amatsimikizira kugwira ntchito kwa Lamulo la Makhalidwe Abwino. Iwo amasonyeza Yehova kukhala Mulungu yemwe amakwaniritsa chifuno chake mokhulupirika. Iye amadalitsa atumiki ake okhulupirika amene, ngakhale kuti ngwopanda ungwiro, amayesera kuchita chifuniro chake ndi kusonyeza kulapa kwenikweni pa kachitidwe kawo kopanduka. “Sambani, dziyeretseni; chotsani machitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kuchita zoipa; phunzirani kuchita zabwino; funani chiweruzo; thandizani osautsidwa; weruzirani ana amasiye, munenere akazi amasiye.”—Yesaya 1:16, 17.
Pamene anthu a Mulungu anachita zabwino kwa ena ndi kwa Mulungu, pamenepo Yehova anaŵatsimikizira chirikizo lake. “Atero Yehova, Sungani inu chiweruziro, ndi kuchita chilungamo; . . . Wodala munthu amene achita ichi, ndi mwana wa munthu amene agwira zolimba ichi.”—Yesaya 56:1, 2.
Kristu Akutsogoza Mpingo Wake
Kristu anadzakwaniritsa Chilamulo ndi Aneneri, ndipo chiyambire nthaŵi yake, chifuno chosatha cha Yehova chapitirizabe patsogolo. (Mateyu 5:17; Aefeso 3:10, 11, 17-19) Chilamulo chakale cha Mose chaloŵedwa m’malo ndi pangano latsopano, lomwe limaphatikizapo ponse paŵiri Ayuda ndi Akristu odzozedwa Amitundu. (Yeremiya 31:31-34) Mosasamala kanthu za izo, mpingo Wachikristu wa tsiku lathu ukutsatirabe Lamulo la Makhalidwe Abwino. Ndipo nachi chifukwa chowonjezereka cha kuvomerezera kugwira ntchito kwa lamulolo: Kristu ndiye Mutu wokangalika wa mpingo Wachikristu wamakono. Iye sanasinthe malangizo ake. Chilangizo chake chowuziridwa chidakali chabwino.
Asanachoke pa dziko lapansili, Yesu analamula otsatira ake kupanga ophunzira a anthu amitundu yonse ndi kuwaphunzitsa kuti “asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” Langizo limenelo linaphatikizapo Lamulo la Makhalidwe Abwino. Yesu anatsimikizira ophunzira ake kuti: “Onani, ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.”—Mateyu 28:19, 20.
Monga momwe zalembedwera pa Luka 6:31, Yesu analamula kuti: “Monga mufuna inu kuti anthu adzakuchitirani inu, muwachitire iwo motero inu momwe.” Ndi chitsanzo chabwino chotani nanga chimene Yesu anakhazikitsa nkukhala woyamba kuchitira ena zabwino!
Mu nthaŵi ya utumiki wake wapadziko lapansi, Yesu anawona mosamalitsa zimene anthu anayenera kuzipirira, ndipo anaŵamvera chisoni. Mkati mwa umodzi wa maulendo ake olalikira, iye anawona makamu ndipo anaŵamvera chifundo. Komabe kuposa zimenezo, iye anapanga makonzedwe a kuŵathandiza. Motani? Mwa kulinganiza ndawala yaikulu yolalikira imene inapereka ophunzira ake ku nyumba za anthu. Monga momwe iye analamulira kuti: “Ndipo m’mzinda uliwonse kapena m’mudzi, mukalowamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo; ndipo bakhalani komweko kufikira mutulukamo.” Kunena kuti ntchito imeneyi inali ndi chirikizo ndi dalitso la Atate wake kukuwoneka bwino lomwe m’mawu owonjezereka a Yesu akuti: “Iye wakulandira inu, andilandira ine, ndi wakundilandira ine, amlandira iye amene ananditumiza ine. . . . Ndipo amene aliyense adzamwetsa mmodzi wa ang’ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.”—Mateyu 9:36–10:42.
Nsonga yakuti Lamulo la Makhalidwe Abwino limatanthauza m’chitidwe wa kuchitira ena ikuwoneka m’lingaliro la Yesu pa chochitika china: “Ndipo ngati muwakonda iwo akukondana ndi inu, mudzalandira chiyamiko chotani? pakuti ochimwa omwe akonda iwo akukondana nawo. Koma takondanani nawo adani anu, ndi kuwachitira zabwino . . . ndipo mphotho yanu idzakhala yaikulu.” (Luka 6:32, 33, 35) Chifukwa chake, kusungabe Lamulo la Makhalidwe Abwino logwiradi ntchito kudzatifulumiza kukhala oyamba kuchitira zabwino anthu amene sitimaŵadziŵa mwaumwini.
Lidakali Laphindu, Lidakagwirabe Ntchito
Mwinamwake chitsimikiziro chotheratu chakuti Lamulo la Makhalidwe Abwino lidakagwirabe ntchito chimachokera ku zokumana nazo zenizeni za awo omwe amalitsatira. Akristu amene amadzisunga iwo eni tsiku lirilonse mogwirizana ndi malamulo a Mulungu amapeza chimwemwe chokulira ndipo, kaŵirikaŵiri, madalitso osayembekezereka. Mwa kukhala waulemu ndi wachifundo kwa antchito a pa chipatala cha mankhwala chomwe anapitako, mkazi mmodzi Wachikristu anapeza kuti anapindula mwa njira imene anesi ndi adokotala anampatsira chisamaliro chapadera chaumwini.
Mboni za Yehova zodziloŵetsa m’kumanga kofulumira kwa maprojekiti a Nyumba Zaufumu zingatsimikizirenso kugwira ntchito kwa Lamulo la Makhalidwe Abwinolo. Kuchezera mokoma mtima anthu okhala pafupi ndi malo omangapowo kuŵadziŵitsa za zimene zakonzekeretsedwa kaŵirikaŵiri kumakhala ndi chivomerezo chabwino. Anthu omwe kalelo anatsutsa Mboni pambuyo pake amawona kuti izo zimachita zabwino kwa anansi awo, ndipo amawona ndi maso njira imene anthu a Mulungu amagwirizanirana m’ntchito yawo. Monga chotulukapo, ena adzipereka kuthandiza kumangako, kaya mwachindunji kapena mwa kupereka zinthu zopezeka.—Yerekezani ndi Zekariya 8:23.
Pamene Mboni ya ku Iran yokhala mu London, Ingalande, inagula zakudya m’sitolo, mwini sitolo anamtonza iye chifukwa chokhala mlendo. Mosakhumudwitsidwa, Mboniyo mokoma mtima ndi mochenjera inalongosola kuti, monga mmodzi wa Mboni za Yehova, iye analibe malingaliro oipa kulinga kwa anthu a mitundu ina. M’malomwake, iye anachezera onse okhala m’mudzimo ndi uthenga wa Baibulo. Chotulukapo chake? Mwini sitoloyo anawonjezera zakudya zina pa zomwe Mboniyo inazigula.
Ndithudi, Lamulo la Makhalidwe Abwino siliri lolekezera ku machitidwe ochepera otero a kukoma mtima. Mowonadi, chisonyezero chake chokulira chiri ubwino umene Mboni za Yehova zimachita dziko lonse mwa kuchezera nyumba za anansi awo mokhazikika ndi uthenga wa mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu.
Kukhala Mogwirizana ndi Lamulo la Makhalidwe Abwino
Kugwiritsira ntchito Lamulo la Makhalidwe Abwino kumatanthauza kupereka chisamaliro chanu kwa ena. Iko kuli chitsogozo cha kuchitira ena. Mudzafunikira kufunafuna nthaŵi za kuchita zabwino kwa okuzingani. Khalani waubwenzi ndi wodera nkhaŵa, kukhala ndi chikondwerero chaumwini mwa iwo! (Afilipi 2:4) Mwakuchita tero, mudzatuta madalitso olemerera. Mudzakhala mukutsatira langizo la Yesu lakuti: “Muwalitse inu kuwunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuwona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wakumwamba.” (Mateyu 5:16) Pambuyo pake, Yehova adzakhala Wopereka Mphotho wanu pamene mumfunafuna mowona mtima ndi kukhala ndi moyo tsiku ndi tsiku mogwirizana ndi Lamulo la Makhalidwe Abwino.—Ahebri 11:6.