Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Anakhudza Chovala Chake
MBIRI ya kubwerera kwa Yesu kuchokera ku Dakapolis ifika ku Kapernao, ndipo khamu lalikuiu lisonkhana pafupi ndi nyanja kumuchingamira iye. Mosakaikira iwo amva kuti iye anatontholetsa mafunde ndi kuchiritsa munthu wogwidwa ndi ziwanda. Tsopano, pamene iye akufika ku gombe, iwo akusonkhana mozungulira iye, mofunitsitsa ndi kuyembekeza.
Mmodzi wa awo amene ali wodera nkhawa kuwona Yesu ali Yairo, nduna yoyang’anira ya sunagoge. lye akugwa pamapazi a Yesu ndi kumpempha mobwerezabwereza: “Kamwana kanga kabuthu kuli mkutsirizika. Ndikupemphani Inu mufikeko muyike manja anu paiko kuti kapulumuke ndi kukhala ndi moyo.” Popeza iye ali mwana wake yekha ndipo ali ndi zaka 12 zokha. Mwanayo ali wapadera kwa Yairo.
Yesu akuvomereza ndipo, motsatizidwa ndi khamu akunyamuka kupita kunyumba ya Yairo. Tingalingalire chikondwerero cha anthuwo pamene akuyembekezera chozizwitsa china. Koma chisamaliro cha mkazi mmodzi mu khamulo chikulunjikitsidwa pa vuto lake lalikuiu koposa.
Kwa zaka 12 mkazi ameneyo wakhala akuvutika ndi kutayikiridwa kwa mwazi. lye wakhala akuwona dokotala mmodzi pambuyo pa mzake, kuwononga ndalama zake zonse kaamba ka thandizo. Koma sanathandizidwe; mmalo mwake, vuto lake likungoyipirayipirabe.
Monga mmene mwinamwake mungayamikirire pambali pa kumufooketsa iye kwambiri vuto lake liri lojejemetsa ndi lochititsa manyazi. Munthu mwachisawawa samalankhula poyera ponena za vuto loterolo. Ndiponso, pansi pa Chilamulo cha Mose kukha kwa mwazi kunampangitsa mkazi kukhala wodetsedwa, ndipo aliyense wokhudza iye kapena zovala zake zodetsedwa ndi mwazi anafunikira kusamba ndi kukhala wodetsedwa kufikira madzulo.
Mkaziyo wamva zozizwitsa za Yesu ndipo tsopano wafunafuna kupeza iye. Nchiyang’aniro cha kudetsedwa kwake iye akupanga kudutsa kwake kupyola mukhamulo kosawoneka monga mmene kungathekere, akumanena kwa iyemwini: “Ngati ndikakhudza ngakhale zovala zake ndidzapulumutsidwa.” Pamene iye achita choncho, mwamsanga iye akuzindikira kuti kukha kwake kwa mwazi kwaphwa!
“Ndani anakhudza zovala zanga?” Ndimotani nanga mmene mawu amenewo a Yesu anamuchititsira mantha iye! Kodi akanadziwa bwanji? ‘Mphunzitsi,’ Petro akupembedzera, ‘muwona kuti khamu likukanikiza inu, ndipo munena, “Kodi wandikhudza ndani?”’
“Akuwunguzaunguza kaamba ka mkaziyo, Yesu akulongosola: “Wina wake wandikhudza popeza ndinazindikira kuti mphamvu inatuluka mwa ine”. Indedi, sikunali kukhudza chabe, popeza kuchiritsa komwe kunatulukapo kunatulutsa mphamvu ya Yesu. Kuwona kuti sakanatha kupulumuka kuzindikiridwa, mkaziyo afika ndi kugwa pamaso pa Yesu wamantha ndi kunjenjemera. Pamaso pa anthu onse, iye akunena chowonadi ponena za matenda ake ndi ndimotani mmene iye wangochiritsidwa kumene.
Wofulumizidwa ndi kulapa kwake, Yesu mwachikondi akumutonthoza iye: “Mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakupulumutsa. Muka m’mtendere, nukhale wochira chivutiko chako.” Chiri chabwino chotani nanga kudziwa kuti Amene Mulungu wamusankha kukhala wolamulira wa dziko lapansi ali wachifundo, munthu wokoma mtima, amene ponse pawiri amasamalira kaamba ka anthu ake ndiponso ali ndi mphamvu ya kuwanthandiza iwo! Mateyu 9:18-22; Marko 5:21-34; Luka 8:40-48; Levitiko 15:25-27.
◆ Kodi Yairo ndi ndani, ndipo kodi nchifukwa ninji wafika kwa Yesu?
◆ Kodi ndi vuto lotani limene mkazi mmodzi ali nalo, ndipo kodi nchifukwa ninji kufika kwa Yesu kaamba ka thandizo kuli kovuta kwa iye?
◆ Kodi ndimotani mmene mkaziyo wachiritsidwira, ndipo ndimotani mmene Yesu akumutonthozera iye?