Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Misozi Inasinthira ku Chikondwerero Chachikulu
PAMENE Yairo awona mkazi yemwe anali ndi nthenda yachikhalire akuchiritsidwa, chidaliro chake mu mphamvu zozizwitsa za Yesu mosakaikira chikuwonjezeka. Kumayambiriro kwa tsikulo, Yesu anali atafunsidwa ndi Yairo kupita ndi kuthandiza mwana wake wa mkazi wa zaka 12, yemwe anali pafupi kufa. Koma pamene iwo anali panjira yopita kunyumba ya Yairo, kumene kuli kapena kufupi ndi Kapernao, mkazi yemwe wangokhudza chabe chofunda cha Yesu wachiritsidwa.
Panthawiyo, ngakhale kuli tero, chimene Yairo akuwopa kwambiri chichitika. Pamene Yesu adakali kulankhula ndi mkaziyo, amuna ena afika ndipo mwakachetechete auza Yairo: ‘‘Mwana wako wafa; uvutiranjinso mphunzitsi?“
Iri yokhumudwitsa chotani nanga mbiriyo! Tangolingalirani: Munthuyu, yemwe amalamulira ulemu waukulu mu mudzi, tsopano ali wopanda thandizo kotheratu pamene akudziwa za imfa ya mwana wake wamkazi. Yesu, ngakhale kuli tero, amvera kukambitsiranako. Chotero, kutembenukira kwa Yairo, iye akunena molimbikitsa: “Usaope, khulupirira kokha.”
Yesu akutsagana ndi munthu wachisoni ameneyu kunyumba yake. Pamene iwo afika, akupeza khamu lalikulu likulira ndi kukuwa. Khamu la anthu lasonkhana, ndipo akudzimenya okha chifukwa cha chisoni. Pamene Yesu alowa mkati, iye akufunsa: “Mubuma ndi kulira bwanji? Mwana sanafe, koma ali m’tulo.”
Pamene amva ichi, anthuwo ayamba kuseka pwepwete kwa Yesu chifukwa akudziwa kuti mwanayo wafa ndithu. Yesu, ngakhale kuli tero, akunena kuti iye wangogona kokha, ndi cholinga chofuna kusonyeza kuti, ndi mphamvu yake yopatsidwa ndi Mulungu, anthu angabweretsedwe kuchoka ku imfa mosavuta monga mmene iwo angadzutsidwire kuchoka m’tulo tofa nato.
Yesu tsopano akulamulira onse kuti atuluke kusiyapo kokha Petro, Yohane, Yakobo, ndi amayi ndi atate a msungwana wakufayo. lye kenaka akutenga asanu amenewa ndi iye kumene msungwana wachichepereyo anali kugona. Akugwira dzanja lake, Yesu akuti: “Talita koumi,“ limene, pamene litatembenuzidwa, limatanthauza: “Buthu, ndinena ndi iwe, Uka!“ Ndipo mwamsanga msungwanayo auka ndi kuyamba kuyendayenda! Chochitikacho chinadabwitsa kwambiri makolo ake ndi chikondwerero chachikulukulu.
Pambuyo pa kuwachenjeza kuti mwanayo ayenera kupatsidwa china chake kuti adye, Yesu akulamulira Yairo ndi mkazi wake kusauza aliyense za chomwe chachitika. Koma mosasamala kanthu za zimene Yesu wanena, nkhani ponena za icho ifalikira mu gawo lonse. Uku kuli kuukitsa kwachiwiri kumene Yesu wakupanga. Mateyu 9:18-26; Marko 5:35-43; Luka 8:41-56.
◆ Kodi ndi mbiri yotani imene Yairo walandira, ndipo kodi ndimotani mmene Yesu akumulimbikitsira iye?
◆ Kodi mkhalidwe uii wotani pamene iwo afika kunyumba ya Yairo?
◆ Kodi nchifukwa ninji Yesu akunena kuti mwana wakufayo ali kokha m’tulo?
◆ Kodi ndi asanu ati amene ali ndi Yesu omwe achitira umboni kuukitsidwaku?