-
Kodi Mukudziwa?Nsanja ya Olonda—2010 | January 1
-
-
Kodi cholembapo chathabwa chotchulidwa pa Luka 1:63 chinali chiyani?
▪ Uthenga Wabwino wa Luka umanena kuti anzake a Zekariya anam’funsa kuti anene dzina limene am’patse mwana wake yemwe anali atangobadwa kumene. Zekariya “anapempha cholembapo chathabwa ndipo analemba kuti: ‘Dzina lake ndi Yohane.’” (Luka 1:63) Zolembapo zoterezi zinali zopangidwa ndi timatabwa tomwe ankatilumikiza pamodzi kenako n’kupaka phula la njuchi pamwamba pake kuti pakhale posalala. Kenako, munthu ankatha kulembapo pogwiritsa ntchito kathabwa kosongoka. Komanso anthu ankatha kufufuta zomwe alembazo kuti alembepo zina.
Buku lina linati: “Zojambula za ku Pompeii, ziboliboli zochokera m’madera osiyanasiyana m’dziko la Roma ndiponso zinthu zina zimene zinafukulidwa m’madera osiyanasiyana ku Egypt mpaka ku Hadrian’s Wall [kumpoto kwa dziko la Britain], zimasonyeza kuti anthu ankagwiritsa ntchito kwambiri zolembapo za matabwa zimenezi.” (Reading and Writing in the Time of Jesus) Anthu monga ochita malonda, ogwira ntchito za boma ndipo mwinanso Akhristu a m’nthawi ya atumwi, ankagwiritsa ntchito zolembapo zoterezi.
-
-
Kodi Mukudziwa?Nsanja ya Olonda—2010 | January 1
-
-
[Chithunzi patsamba 11]
Thabwa Lolembapo la Mwana wa Sukulu la m’ma 100 C.E.
[Mawu a Chithunzi]
By permission of the British Library
-