Chenjerani ndi Kugwiritsira Ntchito Molakwika Mphamvu
“Kuwopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi mkamwa mokhota, ndizida.”—MIYAMBO 8:13.
1. Kodi ndiiti imene iri njira imodzi mwa imene mtima wa munthu wopanda ungwiro umadzisonyeza kukhala wonyenga?
MOSAKAIKIRA kugwiritsiridwa ntchito molakwa kwadyera kwamphamvu kuli pakati panjira zoipa zimene Yehova Mulungu amada. Mawu ake amatipatsa uphungu wotsutsa chikhoterero chimenechi cha anthu opanda ungwiro, chifukwa chakuti amazindikira mtima wa munthu. Timawerenga kuti: “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndiwosachiritsika, ndani angathe kuudziwa? Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa impso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwanjira zake, monga zipatso zantchito zake.”—Yeremiya 17:9, 10.
2. Kodi mphamvu iri ndi chikhoterero cha chiyani kwa okhala nao?
2 Moyenerera Mawu a Mulungu amatichenjeza kuti tisagwiritsire ntchito molakwa mphamvu. Pali chikhoterero chotero cha kugwiritsira ntchito molakwa kapena mosayenera mphamvu kotero kuti katswiri wina Wachingelezi ananena kuti: “Mphamvu imaipitsa, ndipo mphamvu yotheratu imaipitsa kotheratu.” Iye ananenanso kuti: “Pakati pa zochititsa zonse zimene zimaipitsa ndi kululuza anthu, mphamvu ndi chochititsa chanthawi zonse koposa ndi chosonkhezera koposa.” Ndithudi, sikuti mphamvu iri kwenikweni ndi chisonkhezero choluluza, monga momwe tawonera m’nkhani yapita, koma pali upandu wakutero.
3. Kodi ndimikhalidwe yotani ya zochita za anthu mmene mphamvu ingagwiritsiridwe ntchito molakwa, ndipo chifukwa ninji izi zingachitike?
3 Kodi ndani amene afunikira kuchenjera ndikugwiritsira ntchito mphamvu molakwa? Pafupifupi munthu aliyense! Pafupifupi muunansi uliwonse waumunthu muli mikhalidwe kumene munthu mmodzi ali wapamwamba pa ena chifukwa cha chuma, kuphunzira, nyonga yakuthupi, malo antchito, kukongola kwakuthupi, ndi zina zotero. Pamene kupambanako kuli kokulirapo, chiveso cha kukugwiritsira ntchito mwadyera chimakhalanso chokulirapo. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti “Ndingaliro yamtima wa munthu iri yoipa kuyambira paunyamata wake.” (Genesis 8:21) Inde, mtima wamunthu wopanda ungwiro uli “wonyenga,” wonamiza, kapena wozimbaitsa ndi wokhala ndi chikhoterero cha mphulupulu.—Yeremiya 17:9.
Akulu Achikristu
4. Kodi ndiuphungu wabwino kwambiri wotani umene Yetero anapereka kwa Mose, wosonyeza kudziwa mayeso amene amayenderana ndi kulandira mphamvu ndi ulamuliro?
4 Choyamba, talingalirani, akulu, oyang’anira am’mpingo Wachikristu. Pamene tilingalira za ziyeneretso zawo, tingathe kukumbukira mawu a Yetero kwa Mose onena za kusankhidwa kwa amuna oyang’anira zikwi, mazana, makumi asanu, ndi makumi akuti: “Iwe dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna amtima, akuwopa Mulungu, amuna owona, akudana nalo phindu lachinyengo.” (Eksodo 18:21) Anthu amtundu wotere akatha kuikiziridwa uyang’aniro. Iwo sakanagwiritsira ntchito molakwa mapindu amene amadza ndi malo antchito auyang’aniro, chifukwa chakuti kuwopa Mulungu kumatanthauza kuda choipa. Amuna otero ‘akadanadi nalo phindu lachinyengo’ mmalo mwakulifunafuna kapena kulikonda.
5. Kodi nchifukwa ninji uphungu wa pa 1 Petro 5: 2, 3 uli woyenerera kwambiri, ndipo kodi ungagwiritsiridwe ntchito motani?
5 Mtumwi Petro anali kuzindikira ngozi yakugwiritsiridwa ntchito molakwa kwamphamvu kochitidwa ndi akulu, ndipo motero tikumpeza akupatsa uphungu mumpingo Wachikristu kuti: “Wetani gulu la Mulungu liri mwa inu, ndikuliyang’anira, osati mokangamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phi ndu lonyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo audindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.” (1 Petro 5:2, 3 Kuweta gulu la Mulungu kaamba ka phindu lonyenga kukakhala kugwiritsira ntchito mphamvu mosayenera. Mofananamo, kuchita umbuye pa gulu lankhosa kungakhale kugwiritsira ntchito mwadyera mphamvu yamunthuwe. Mwachitsanzo, mkulu angakhale ndi malingaliro otsimikizirika onena za minene banja lake liyenera kuvalira. Koma afunikira kukhala wosamala kuti sakuyesa kukakamiza malingaliro ake pa gulu lankhosa; kutero kukakhala kuchita umbuye pa iwo.
6. Kodi chibale (nepotism) nchiyani, kodi ndimotani mmene akulu angakhalire ndi liwongo lake?
6 Kusiyapo ngati akuluwo ali osamala, angakhale ndi liwongo la kuchita chibale (nepotism), chimene chingakhalenso kugwiritsira ntchito molakwa mphamvu. Chibale? Inde, liwuli likuchokera ku Chilatini, lotanthauza “asuwani.” Linagwiritsiridwa ntchito chifukwa cha chizolowezi chotchuka cha apapa ndi akuluakulu ena atchalitchi cha kupereka mapindu achipembedzo ndi zinthu zakuthupi kwa achibale awo ndipo makamaka kwa ana a abale awo kapena a alongo awo. Papa Nicholas III anadziwikadi kukhala “bambo wa apapa ochita chibale.” Kusiyapo ngati akulu Achikristu ali osamala kwambiri, iwo mosadziwa angasonkhezeredwe ndi zomangira zabanja mmalo mwa malamulo amakhalidwe abwino auzimu. Mkulu wina analingalira mwamphamvu kwambiri kuti mwana wake ayenera kuvomerezedwa kukhala woyang’anira ngakhale kuti akulu ena onse sanavomereze. Kunachitika kuti atateyo anasamukira kumpingo wina. Zaka zingapo pambuyo pake mwanayo anali asanakhalebe mkulu. Mwachiwonekere, atateyo anali ndi chisonkhezero chaubale mwa iye.
7, 8. Kodi nzitsanzo zotani zimene zimasonyeza kuti kuchita chibale kungakhaledi ngozi kwa akulu?
7 Kugwiritsiridwa ntchito molakwa kwa mphamvu kwina mu mpangidwe wachibale kumawonekera pamene akulu amalephera kuchitapo kanthu pa cholakwa cha achibale awo. (Yerekezerani ndi 1 Samueli 2:2-25, 30-35. ) Zaka zochepekera zapitazo panali mkhalidwe womvetsa chisoni wa cholakwa m’mipingo ina chapakati pa United States. Osati kale kwambiri mkhalidwewu unabuka m’mipingo ina yaku Ulaya. Achichepere ambiri anaphatikizidwa m’kuchita dama lachigololo, kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala, ndi zina zotero. Unyinji wa amenewa unali ana aakulu, amene mwachiwonekere ena a iwo analekerera khalidwe loipa la ana awo. Pamene maumboni anaululika, unyinji wa akulu otero unachotsedwa paukulu chifukwa cha kugwiritsira ntchito kwawo molakwa mwawi wawo monga akulu, kapena kunena molunjika kwambiri, chifukwa cha kulephera kwawo kugwiritsira ntchito mphamvu yawo moyenera.
8 Nthawi zina pamawonekera kukhala chikhoterero pankhaniyi pamene mkulu kapena mtumiki wotumikira atsogoza kutenga mbali kwa omvetsera m’nkhani zina pa misonkhano. Afunikira kukhala wosamala kupewa tsankhu. Mamembala abanja lake angagwirizanike pamfundoyi mwa kukhala amaso kupereka ndemanga pamene ena akulephera kuyankha ndi kusakhala olakalaka koposa kupereka ndemanga pamene ena ambiri ali chitukulire mikono kuti ayankhe.
Oimira Oyendayenda
9. Kodi nchifukwa ninji kugwiritsira ntchito molakwa mphamvu kumadziwika monga chisimoni (chiphuphu), ndipo chifukwa ninji chimatchedwa motero?
9 Akristu okhala ndi malo antchito auyang’aniro, makamaka oimira oyendayenda aWatch Tower Society, ayenera kukhala osamala kuti sakukhala ndi liwongo, ladala kapena losakhala ladala, la chimene chimadziwika kukhala chiphuphu chisimoni. Liwulo lachokera kwa Simon wotchulidwa pa Machitidwe 8: 9-24, amene analonjeza kupereka ndalama kwa atumwi monga mphatso kuti akhoze kumpatsa mzimu woyera mwa kumuika manja kwawo. Luka akulemba kuti: “Petro anati kwa iye, Ndalama yako itaike nawe, chifukwa unalingalira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama. Ulibe gawo kapena cholandira ndi mawu awa; pakuti mtima wako suuli wolunjika pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake lapa choipa chako ichi, pemphera Ambuye kuti kapena akukhululukire iwe cholingilira chamtima wako.” Chimenechi chinalinso chizolowezi chotchuka pakati pa akuluakulu a Tchalitchi cha Roma Katolika m’zaka zonse zapita. Bukhu lina la nazonse likusimba kuti “upandu uwu unafikira kukhala wotchuka kwambiri m’Tchalitchi mkati mwa zaka za zana la 11 ndi 12.”
10, 11. Kodi ndimotani mmene akulu angakhalire mikhole ya msampha wachasimoni?
10 Kodi atumiki a Yehova angachimwe motani pamfundoyi? Kusiyapo ngati ali osamala kwambiri, iwo angathe kukhala ndi chikhoterero cha kuvomereza mkulu kukhala ndi mbali pa programu ya msonkhano wadera kapena wachigawo chifukwa cha kuchereza kwabwino kwambiriko kapena mphatso zachifundo zolandiridwa kuchokera kwa iye. Kwenikweni, pakhala zochitika zowerengeka pa zimene mkulu anapereka mphatso zachifundo ndipo panthawi imodzimodziyo analankhula za kuthekera kwa kulandira mwawi wina wapadera. Mwachiwonekere anthu otero sanali okhutira ndi kudzisungira monga ‘aang’onong’ono,’ kusiira mzimu woyera kusonkhezera awo okhala m’malo antchito auyang’aniro kusamalira maikidwe ateokratiki. (Luka 9:48) Pansi pamikhalidwe imeneyo mphatso zotero zakanidwa, motero kupereka chitsanzo chabwino kwambiri cha kusagwiritsira ntchito molakwa mphatso ya mphamvu. Zochitika zotere zonsezo zimasonyeza mmene akulu okhala ndi mphamvu ayenera kukhalira osamala kuti apewe liwongo lachisimoni!
11 Ndiponso, nthawi zina kungakhale kofunika kwa minisitala woyendayenda kupereka uphungu wamphamvu kwa mkulu. Koma ngati minisitala woyendayendayo wakhala akulandira mphatso mobwerezabwereza kwa mkulu ameneyo kapena anacherezedwapo naye, angakupeze kukhala kovuta kumpatsa uphungu wolunjika. Kodi malingaliro adyera adzamlepheretsa kusenza mathayo ake akupereka uphungu wofunikawo? Kodi iye adzaika zinthu zauzimu za abale ake patsogolo pa mapindu a iyemwini akuthupi? Inde, kodi iye adzafunafuna kukondweretsa Mulungu kapena anthu?—Agalatiya 1:10.
Banja
12. Kodi nchifukwa ninji amuna ayenera kukhala maso kugwiritsira ntchito mphamvu moyenera?
12 Mkati mwa banja mulinso kufunikira kwakuti chiwalo chirichonse chikhale chosamala kuwopera kuti chingagwiritsire ntchito molakwa ulamuliro kapena mphamvu. Mwamuna, chifukwa cha kukhala kwake mutu, kapena chifukwa cha kukhala kwake wanyonga yakuthupi yokulirapo, kapena chifukwa chakuti ndiye wopezera chakudya banjalo, angachite mwanjira yankhalwe, yaphunzo, ndi yosasonyeza kukoma mtima. Paulo anagogomezera mwamphamvu kuti akazi ayenera kukhala ogonjera kwa amuna awo. Panthawi imodzimodziyo iye akuuza amuna kuti akonde akazi awo monga matupi a iwo eni ndi kukhala ofunitsitsa kuwafera, monga momwedi Kristu anafera mpingo Wachikristu. (Aefeso 5: 25-33) Uphungu wotero uyenera kuchita monga chitetezo pa kugwiritsira ntchito molakwa kwa mwamunayo mphamvu yake kapena ulamuliro. Mtumwi Petro atatha kupereka uphungu kwa akazi kuti akhale ogonjera amuna awo, akulangiza amuna kuti: “Amuna inu khalani nawo monga mwachidziwitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso olowa nyumba pamodzi wachisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.” Inde, amuna ayenera kukhala osamala kugwiritsira ntchito mphamvu zawo moyenera ngati afuna kukhala ndi unansi wabwino ndi Yehova Mulungu.—1 Petro 3:7.
13. (a) Kodi nchikhoterero chaukazi chotani chimene amuna nthawi zina amadyera masuku pamutu? (b) Kodi ndimotani mmene akazi adyera agwiritsirira ntchito molakwa mphamvu, akumaswa chilangizo chiti Chamalemba?
13 Kwawonedwa kuti mwamuna kapena mkazi wokhala ndi chikondi kwambiri amalimidwa pamsana ndi wosakonda kwambiriyo. Mukuwonekera kukhala mlingo wachowonadi m’zimenezo. Kwakukulukulu, akazi, amakonda kwambiri kuposa amuna awo—chikondi chiri chofunika kwambiri kwa iwo—ndipo amuna ambiri amadyera masuku pamutu mkhalidwe umenewo, Kumbali ina, akazi adziwika kukhala osonyeza mphwayi popereka mangawa aukwati pamene zikhumbo zawo zadodometsedwa. Kwenikweni, akazi ena akaniratu kupereka mangawa aukwati. Nzachisoni kunena kuti, nthawi zina izi zawonjezera kukuchita chigololo kwa mwamunayo. Kulephera konseku kulabadira uphungu wa Paulo pa 1 Akorinto 7:3-5 mofananamo ndiko kugwiritsira ntchito mphamvu molakwa kwadyera.
14. Kodi pali umboni wotani wakuti makolo ena amagwiritsira ntchito molakwa mphamvu yawo pa ana awo?
14 Chenicheni chakuti ana ayenera kumvera makolo awo m’chigwirizano ndi Ambuye chimapereka kwa makolo awo, makamaka atate awo, mphamvu pa iwo. Komabe kodi iwo adzagwiritsira ntchito motani mphamvuyo? Mwankhalwe, mwaphunzo, mosakoma mtima kodi? Atate audziko ambiri, ndi amayi ena, amachita zimenezo kumene, akumachititsa kuwanda kwa “funde la kuchitiridwa nkhalwe kwa ana.” Mogwirizana ndi kunena kwa World Health, January/February 1984, “ana ochitiridwa nkhalwe akupezeka m’zitaganya zonse,” ndipo “kukuwonekera ngati kuti lerolino ana owonjezerekawonjezereka akuchitiridwa nkhanza, kudyeredwa masuku pamutu, kuchitiridwa nkhalwe kapena kunyanyalidwa, ndipo palibe mbali yadziko imene ikusiyidwa.” Lipoti lina likusimba kuti m’United States kuchitira nkhalwe ana kwawirikiza kuposa nthawi ziwiri m’zaka khumi zapitazo. Ndithudi zonsezi ndizo kugwiritsira ntchito mphamvu molakwa. Ngakhale kholo Lachikristu limene silikanalingalira kuchitira mwana nkhalwe mopambanitsa lingakhale ndi liwongo la kuchitira mwana nkhalwe. Mungathe kuwona chimene iko kuli muuphungu wa Paulo wakuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” “Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.”—Aefeso 6:4; Akolose 3:21.
15, 16. Kodi ndimotani mmene ana angakhalire ndi liwongo la kugwiritsira ntchito molakwa mphamvu, kukumafunikiritsa chiyani kwa makolo?
15 Mulimonse mmene kungawonekerere kukhala kwachilendo poyamba, ana enieniwo angakhalenso ndi liwongo lakugwiritsira ntchito mphamvu molakwa. Zingatero motani? Ana angathe kuchititsa makolo awo kuchita motsutsana ndi chiweruzo chawo chabwino kwambiricho chifukwa cha chikondi chimene makolo awo ali nacho pa iwo. Mwanayo, podziwa kuti afunikira kupamanthidwa, angalire momvetsa chisoni kotero kuti amake amalephera kupereka chilango chofunikiracho chopamantha. Ntchemberembaya ina imene imapeza chipambano muukatswiri wosunga ndalama za anthu ikudzitamandira m’luso lake lakuchita ndi osungitsawo, ikumati, “Akazi amabadwa motero. Idzani mudzawone mwana wanga wamkazi mmene amachitira kwa atate wake.”
16 Mogwirizana ndi kunena kwa ripoti limodzi la nyuzipepala “pali kuwonjezereka kochititsa mantha m’chiŵrengero cha ‘ana okonda kulamulira’ m’North America amene amalamulira ndi kuyendetsa miyoyo ya makolo awo.” Komabe, njira yothetsera siikudalira pa kupatsa anawo uphungu, koma makolo. Makolo ayenera kusonyeza mkhalidwe wogwirizana kwa ana awo. Achichepere amafulumira kuwona kusagwirizana ndi kuchititsa kholo limodzi kutsutsana ndi linzake kuti apeze zimene afuna. Makolo ayeneranso kukhala osagonjera pa chimene chiri cholungama, panthawi imodzimodziyo nthawi zonse kutsimikizira ana awo kuti amawakonda. Monga morn we Yehova amachitira, makolo Achikristu amapereka uphungu chifukwa chachikondi.—Ahebri 12:5, 6.
Maunansi Ena
17. Kodi ndimotani mmene mungakhalire kugwiritsiridwa ntchito molakwa kwa mphamvu muunansi wa wolembedwa ntchito ndi wolemba ntchito?
17 Maunansi a olemba ntchito ndi olembedwa ntchito nawonso amapereka ziyeso za kugwiritsira ntchito molakwa mphamvu. Pokhala ndi zimenezi m’maganizo, Paulo anapereka uphungu kwa eni akapolo, amene mwapang’ono amalingana ndi olemba ntchito amakono, oyang’anira, mabwana: ‘Ambuye inu, chitirani . . . zomwezo iwowa, nimuleke kuwawopsa; podziwa kuti Ambuye wawo ndi wanu ali m’mwamba, ndipo palibe tsankhu kwa iye.’ (Aefeso 6:9; Akolose 4:1) Akristu amene ali ndi uyang’aniro m’nkhani zadziko ayenera kukhala osamala kuti asagwiritsire ntchito mphamvu yawo molakwa. Boazi wakale angatchulidwe kuti anali ndi unansi wabwino kwambiri ndi antchito ake.—Rute 2:4.
18. Kodi nchisamaliro chotani chimene abale ndi alongo osakwatirana ayenera kusonyeza kotero kuti asakhale ndi liwongo la kugwiritsira ntchito molakwa mphamvu?
18 Kungotchula mbali imodzi yokha mu imene Akristu ayenera kuchenjera ndi kugwiritsira ntchito molakwa mphamvu, pali nkhani ya kukopedwa m’zakugonana. Chibadwa chenichenicho cha alongo achichepere chimakhotereretsa ambiri a iwo kufuna kukwatidwa ndi kubala ana. Monga chotulukapo, nthawi zina abale angakupeze kukhala kosavuta kukopedwa ndi chikondi cha alongo. Ndithudi kumeneku ndiko kugwiritsira ntchito molakwa mphamvu. Paulo anapatsa uphungu Timoteo wakuti: “Chitira akazi aakulu ngati amayi, akazi aang’ono ngati alongo, m’kuyera mtima konse.’ Kumbali ina, akazi Achikristu akupatsidwa uphungu wa ‘kuvala chovala chosawola chamzimu wofatsa ndi wachete.’ Kaya ali okwatiwa kapena mbeta, ayeneranso kukhala osamala kusonyeza “mayendedwe oyera.”—1 Timoteo 2:9; 5:2; 1 Petro 3:2.
19. Kuwonjezera pa kusonyeza nzeru, chiweruzo cholungama, ndi chikondi, kodi ndikugwiritsiridwa ntchito kwa mkhalidwe wina wotani kumene tiyenera kudera nkhawa?
19 Pali zambiri zimene zanenedwa m’mabukhu athu olongosola Baibulo ponena za kutsogozedwa ndi nzeru ya Mulungu kwa Akristu, ponena za kusonyeza chiweruzo cholungama m’zochita zawo zonse, ndi ponena za kusonkhezeredwa ndi chikondi chopanda mpeni kumphasa, a·gaʹpe. Zapamwambapazi, zimasonyeza kuti atumiki onse a Yehova ayeneranso kukhala odera nkhawa ndi ukoma, mkhalidwe, kapena kukhala ndi mphamvu. Sayenera konse kuigwiritsira ntchito molakwa, koma nthawi zonse kuigwiritsira ntchito moyenera. Ndithudi Mawu a Mulungu amavumbula nzeru ya Mulungu muuphungu umene amapereka pamfundozi. Mwakulabadira uphungu wotero mosamalitsa, tidzadzetsa ulemu padzina la Yehova, tidzakhala dalitso kwa ena, ndipo tidzapeza chiyanjo cha Mulungu.
Kodi Ndiuphungu Wotani Umene Mukukumbukira?
◻ Kodi kunganenedwe motani kuti tiri ndi chikhoterero chachibadwa cha kugwiritsira ntchito molakwa mphamvu?
◻ Kodi nchifukwa ninji akulu ayenera kukhala osamala kuti sakugwiritsira ntchito molakwa mphamvu yawo?
◻ Kodi ndimnjira zotani m’zimene amuna ndi akazi sayenera kugwiritsira ntchito molakwa mphamvu yawo muunansi wawo kwa wina ndi mnzake?
◻ Kodi onse awiri makolo ndi ana ayenera kupewa chiyani ponena za kugwiritsira ntchito molakwa mphamvu m’maunansi awo?
[Chithunzi patsamba 13]
Simoni anayesa kugwiritsira ntchito chuma kusonkhezera Petro—kodi tingaphunzirenji kuchokera ku chochitika chimenechi?
[Chithunzi patsamba 15]
Kodi mwana wanu amagwiritsira ntchito mphamvu molakwa kukulamulirani?