Anachita Chifuniro cha Yehova
Yesu Atumiza Ophunzira 70
MUNALI m’nyengo ya phukuto ya mu 32 C.E. Panali patangotsala miyezi isanu ndi umodzi yokha kuti Yesu afe. Choncho, pofuna kufulumiza ntchito yolalikira ndiponso kupititsa patsogolo maphunziro a ena mwa otsatira ake, iye anasankha ophunzira 70 “nawatuma iwo aŵiriaŵiri pamaso pake [“patsogolo pake,” NW] kumudzi uliwonse, ndi malo alionse kumene ati afikeko mwini.”—Luka 10:1.a
Yesu anatumiza ophunzira ake “patsogolo pake,” pofuna kuti anthu akhale atasankhiratu kuti kaya anali ogwirizana ndi Mesiya kapena otsutsana naye pamene Yesu iye mwini adzafikako pambuyo pake. Koma kodi nchifukwa ninji anawatumiza “aŵiriaŵiri”? Mwachionekere, cholinga chake chinali chakuti azilimbikitsana pamene akumana ndi chitsutso.
Pogogomezera kuti ntchito yawo yolalikirayo inafunikira kuchitidwa mofulumira, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Dzinthu dzichuluka, koma antchito achepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe antchito kukututa kwake.” (Luka 10:2) Kufanizira ntchitoyi ndi kututa kunali koyenerera, popeza kuti kututa mochedwa kungawonongetse mbewu zofunika. Mofananamo, ngati ophunzirawo akanachedwa kuchita ntchito yolalikirayo, miyoyo yamtengo wapatali ikanatayika!—Ezekieli 33:6.
Atumiki Osachenjenetsedwa
Yesu anauzanso ophunzira akewo kuti: “Musanyamule thumba la ndalama kapena thumba la kamba, kapena nsapato; nimusalankhule [“ndipo musakupatire,” NW] munthu panjira.” (Luka 10:4) Panali mwambo wakuti wapaulendo sayenera kutenga thumba la ndalama ndi la kamba lokha ayi koma ayeneranso kutenga nsapato zapadera, popeza anadziŵa kuti kuphazi kwa nsapatozo kungabooke nthaŵi iliyonse ndiponso mwina zingwe zomangira zingaduke. Koma ophunzira a Yesu anauzidwa kuti asadere nkhaŵa zinthu zimenezo. M’malo mwake, iwo anayenera kukhala ndi chidaliro chakuti Yehova adzawasamalira mwa Aisrayeli anzawo, amene anali ndi mwambo wochereza alendo.
Koma kodi nchifukwa ninji Yesu anauza ophunzira ake kuti asakupatire aliyense polonjerana? Kodi iwo anayenera kukhala amsunamo, kapena amwano? Kutalitali! Mawu achigiriki akuti a·spaʹzo·mai, otanthauza kukupatira polonjerana, angatanthauze zambiri kuposa mawu aulemu chabe akuti “moni” kapena kuti “muli bwanji?” Angaphatikizeponso kupsompsonana kwamwambo, kukupatirana, ndi makambitsirano aatali amene anali kuchitika pamene mabwenzi aŵiri akumana. Wothirira ndemanga wina anati: “Malonje a pakati pa anthu a Kummaŵa sanangophatikizapo kuŵerama pang’ono kapena kupereka moni wa chanza monga momwe timachitira ife, koma anali kuphatikizaponso kukupatirana mobwerezabwereza, ndi kuŵerama, ndiponso ngakhale kugunditsa nkhope pansi. Zinthu zonsezi zinali kudya nthaŵi yambiri.” (Yerekezerani ndi 2 Mafumu 4:29.) Choncho, Yesu anathandiza otsatira ake kuti apeŵe zochenjenetsa zosafunikira kwenikweni zimenezi ngakhale kuti unali mwambo wawo.
Pomalizira pake, Yesu anauza ophunzira akewo kuti pamene aloŵa m’nyumba nalandiridwa, ‘m’nyumba momwemo akhale, ndi kudya ndi kumwa za kwawo.’ Koma pamene aloŵa m’mudzi ndipo sanalandiridwe bwino, iwo anayenera ‘kutuluka ku makwalala ake nanena, lingakhale fumbi lochokera kumudzi kwanu, lomamatika kumapazi athu, tilisansira pa inu.’ (Luka 10:7, 10, 11) Kusansa kapena kukunkhumula fumbi la kumapazi kunali kusonyeza kuti ophunzirawo anali kuchoka mwamtendere m’nyumba kapena m’mudzi umene sunawalandirewo, opanda mlandu pa zotsatirapo zilizonse zimene zidzachokera kwa Mulungu m’kupita kwa nthaŵi. Koma awo amene analandira ophunzira a Yesu mwachikondi anayembekezera kulandira madalitso. Yesu anauza atumwi ake nthaŵi inayake kuti: “Iye wakulandira inu, andilandira Ine, ndi wakundilandira Ine, amlandira iye amene ananditumiza Ine. Ndipo amene aliyense adzamwetsa mmodzi wa aang’ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.”—Mateyu 10:40, 42.
Maphunziro kwa Ife
Ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi kupanga ophunzira tsopano ikuchitika ndi Mboni za Yehova zoposa 5,000,000 padziko lonse lapansi. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Iwo amadziŵa kuti uthenga wawo ngwofunika kwambiri. Choncho, iwo amagwiritsira ntchito bwino nthaŵi yawo, kupeŵa zochenjenetsa zimene zingawalepheretse kupereka chisamaliro chachikulu ku ntchito yawo yofunika kwambiri imeneyi.
Mboni za Yehova zimayesetsa kusonyeza chikondi kwa anthu onse amene akumana nawo. Komabe, iwo sachedwa ndi nkhani zanthabwala, kapena kuloŵa m’mikangano yokhudza zinthu zatsiku ndi tsiku kapena zoyesayesa zosaphula kanthu za dzikoli kuti athetse chisalungamo. (Yohane 17:16) M’malo mwake, iwo amasumika makambitsirano awo pa yankho lokha limene lidzathetseratu mavuto a anthu—Ufumu wa Mulungu.
Nthaŵi zambiri, Mboni za Yehova zimagwira ntchito zili aŵiriaŵiri. Kodi munthu atamagwira ntchitoyo yekha sangachite zinthu zochulukirapo? Mwinamwake. Ngakhale zili motero, Akristu lerolino amazindikira kuti kugwira ntchito mothandizana ndi wokhulupirira mnzawo kumakhala kopindulitsa. Kumawathandiza kukhala ndi chitetezo chokwanira pamene achitira umboni m’madera oopsa. Kugwira ntchito ndi mnzawo kumapangitsanso kuti atsopano apindule ndi luso la ofalitsa ozoloŵera a uthenga wabwino. Kunena zoona, onse aŵiriwo amalimbikitsana.—Miyambo 27:17.
Mosakayika konse, ntchito yolalikira ndiyo ntchito yofuna changu chachikulu koposa imene ikuchitika mu “masiku otsiriza” ano. (2 Timoteo 3:1) Mboni za Yehova zili zosangalala kuti zili ndi chichirikizo cha ubale wadziko lonse umene umawathandiza kugwirira ntchito “pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha uthenga wabwino.”—Afilipi 1:27.
[Mawu a M’munsi]
a Mabaibulo ena ndi zolembedwa zakale zachigiriki zimanena kuti Yesu anatuma ophunzira “makumi asanu ndi aŵiri mphambu aŵiri.” Komabe, pali umboni wokwanira wolembedwa wochirikiza “makumi asanu ndi aŵiri.” Kusiyana kumeneku kwa kaŵerengedwe sikuyenera kusokoneza mfundo yaikulu, yakuti Yesu anatumiza gulu lalikulu la ophunzira ake kukalalikira.