-
Nkhani ya Msamariya Imatithandiza Kudziwa Mnzathu WeniweniYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
Inde, chifukwa Yesu anamuuza kuti: “Wayankha molondola. ‘Uzichita zimenezo, ndipo udzapeza moyo.” Koma nkhaniyi siinathere pomwepo. Munthuyo ankangofuna “kudzionetsa kuti ndi wolungama” choncho sankafuna kuti Yesu angomuuza yankho lolondola. Ankafuna kuti zimene Yesu angamuyankhe zisonyeze kuti maganizo ake ndi olondola n’cholinga choti aoneke kuti ankachita zinthu mwachilungamo ndi anthu ena. Ndiyeno anafunsa Yesu kuti: “Nanga mnzanga amene ndikuyenera kumukonda ndani kwenikweni?” (Luka 10:28, 29) Yankho la funsoli silinali lophweka. N’chifukwa chiyani tikutero?
Tikutero chifukwa Ayuda ankakhulupirira kuti mawu akuti “mnzanga” ankatanthauza munthu yekhayo amene ankasunga miyambo yachiyuda. Ndipo n’kutheka kuti ankaganiza kuti ndi zimene mawu opezeka pa Levitiko 19:18 ankatanthauza. Ayuda ankanena kuti kugwirizana ndi anthu omwe sanali Ayuda “n’kosaloleka.” (Machitidwe 10:28) Choncho munthu ameneyu ankadziona kuti ndi wolungama chifukwa chochitira chifundo Ayuda anzake ndipo mwina ophunzira ena a Yesu analinso ndi maganizo amenewa. Anthuwa ankaona kuti akhoza kuchitira nkhanza munthu yemwe sanali Myuda ndipo ankadzikhululukira ponena kuti munthuyo si ‘mnzawo.’
-
-
Nkhani ya Msamariya Imatithandiza Kudziwa Mnzathu WeniweniYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
Imeneyi inali njira yabwino kwambiri yophunzitsira. Ngati Yesu akanangouza munthuyo kuti azionanso anthu ena omwe sanali Ayuda kuti ndi anzake, munthuyo komanso Ayuda ena amene ankamvetsera sakanavomereza zimenezi. Koma chifukwa chakuti Yesu ananena fanizo losavuta kumva komanso anafotokoza zinthu zomwe anthuwo ankazidziwa bwino, zinali zosavuta kuti anthuwo adziwe kuti mnzawo weniweni anali ndani. Choncho tinganene kuti mnzathu weniweni ndi munthu amene amatikonda komanso kutichitira chifundo mogwirizana ndi zimene Malemba amanena.
-