Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 7/1 tsamba 32
  • Kukongola Kumene Sikumafwifwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukongola Kumene Sikumafwifwa
  • Nsanja ya Olonda—1993
Nsanja ya Olonda—1993
w93 7/1 tsamba 32

Kukongola Kumene Sikumafwifwa

“KUKONGOLA kumazimiririka; kukongola kumatha,” anatero wolemba ndakatulo Walter De la Mare. Zimaterodi kwa maluŵa okongola a cactus osonyezedwa panopa. Ulemerero wake umafwifwa mofulumira.

Mtumwi Wachikristu Yakobo analemba kuti: “Pakuti [munthu wolemera] adzapita monga duŵa la udzu. Pakuti latuluka dzuŵa ndi kutentha kwake, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duŵa lake, ndi ukoma wa maonekedwe ake waonongeka; koteronso wachuma adzafota m’mayendedwe ake.”​—Yakobo 1:10, 11.

M’dziko lino losadalirika, chuma chingazimiririkedi patsiku limodzi. Ndiponso, munthu wolemera​—mofanana ndi wina aliyense​—‘amakhala kwakanthaŵi, monga duŵa.’ (Yobu 14:1, 2) Yesu anasimba fanizo la mwamuna amene anadzitanganitsa kwambiri ndi kukundika chuma kotero kuti apumule ndi kusangalala. Koma pamene anaganiza kuti wapeza zonse zimene anafuna zomkondweretsa m’moyo wake, iye anafa. Yesu anachenjeza kuti: “Atero iye wakudziunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.”​—Luka 12:16-21.

“Chuma cha kwa Mulungu.” Kodi Yesu anatanthauzanji ndi mawuŵa? Munthu wachuma mwanjirayi ali ndi ‘chuma kumwamba’​—dzina labwino ndi Mulungu. Chuma chimenecho sichimafwifwa konse. (Mateyu 6:20; Ahebri 6:10) Mmalo mofanana ndi duŵa limene limanyala, munthu woteroyo amayerekezeredwa m’Baibulo ndi mtengo, umene masamba ake samafota. Ndipo, tikutsimikiziridwa kuti, “zonse azichita apindula nazo.”​—Salmo 1:1-3, 6.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena