PHUNZIRO 17
Kodi Yesu Ali Ndi Makhalidwe Otani?
Tikamaphunzira zimene Yesu ananena ndi kuchita ali padziko lapansi, timapeza makhalidwe abwino kwambiri amene amachititsa kuti tizimukonda ndiponso kuti tizikonda Atate wake Yehova. Kodi ena mwa makhalidwe abwino kwambiri amene Yesu ali nawo ndi ati? Nanga tingamutsanzire bwanji?
1. Kodi Yesu amafanana ndi Atate wake m’njira ziti?
Kwa zaka mabiliyoni ambiri, Yesu anakhala kumwamba ndi Atate wake wachikondi. Kwa nthawi yonseyi, iye ankaona komanso kuphunzira zinthu zambiri kuchokera kwa Atate wake. Choncho iye amaganiza, kukhudzika ndi kuchita zinthu ngati Atate wake. (Werengani Yohane 5:19.) Ndipotu Yesu amatsanzira makhalidwe abwino amene Atate wake ali nawo. Mpake ananena kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yohane 14:9) Mukamaphunzira makhalidwe a Yesu, mudzatha kumudziwa bwino Yehova. Mwachitsanzo, chifundo chomwe Yesu ankasonyeza anthu ndi umboni wakuti Yehova amakuderani nkhawa mukamavutika.
2. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti amakonda Yehova?
Yesu anati: “Kuti dziko lidziwe kuti ndimakonda Atate, ndikuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Atatewo anandilamula.” (Yohane 14:31) Yesu ali padziko lapansi, anasonyeza kuti amakonda kwambiri Atate wake powamvera ngakhale pamene zinali zovuta kuchita zimenezi. Iye ankakonda kulankhula zokhudza Atate wake ndipo ankathandiza anthu ena kuti nawonso ayambe kukonda Mulungu.—Yohane 14:23.
3. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti amakonda anthu?
Baibulo limasonyeza kuti Yesu amasangalala kwambiri ndi “mtundu wa anthu.” (Miyambo 8:31) Iye anasonyeza kuti amakonda anthu powalimbikitsa ndi kuwathandiza mosanyinyirika. Zodabwitsa zimene anachita zinkasonyeza kuti ali ndi mphamvu komanso zinkasonyeza kuti ndi wachifundo. (Maliko 1:40-42) Iye ankathandiza anthu mokoma mtima komanso mosakondera. Zomwe ankalankhula zinkatonthoza anthu a mtima wabwino amene ankamumvetsera komanso kuwathandiza kukhala ndi chiyembekezo. Yesu analolera kuvutika komanso kufa chifukwa amakonda anthu onse. Koma iye amakonda kwambiri anthu amene amakonda zimene ankaphunzitsa.—Werengani Yohane 15:13, 14.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti mudziwe zambiri zokhudza makhalidwe a Yesu ndipo onani zimene mungachite kuti muzimutsanzira pa nkhani yosonyeza chikondi ndi kukhala opatsa.
4. Yesu amakonda Atate wake
Zimene Yesu ankachita zimatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tizikonda Mulungu. Werengani Luka 6:12 ndi Yohane 15:10 komanso 17:26. Mukawerenga lemba lililonse, kambiranani funso ili:
Potengera chitsanzo cha Yesu, tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yehova?
Yesu ankakonda Atate wake akumwamba ndipo nthawi zambiri ankalankhula nawo m’pemphero
5. Yesu amaganizira anthu ovutika
Yesu ankaganizira kwambiri zofuna za anthu ena kuposa zofuna zake. Ankayesetsa kugwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zake pothandiza anthu. Iye ankachita zimenezi ngakhale atatopa. Werengani Maliko 6:30-44, kenako mukambirane mafunso awa:
Munkhaniyi, kodi Yesu anachita zinthu ziti posonyeza kuti amaganizira ena?—Onani vesi 31, 34, 41 ndi 42.
Kodi ndi khalidwe liti limene linachititsa kuti Yesu athandize anthuwo?—Onani vesi 34.
Popeza kuti Yesu amatsanzira makhalidwe a Yehova, kodi zimenezi zikukuphunzitsani chiyani zokhudza Yehova?
Kodi ndi zinthu ziti zimene tingachite potsanzira Yesu pa nkhani yoganizira ena?
6. Yesu ndi wopatsa
Ngakhale kuti Yesu analibe zinthu zambiri zakuthupi, ankakonda kugawira ena zimene anali nazo. Iye amafuna kuti nafenso tizikhala opatsa. Werengani Machitidwe 20:35, kenako mukambirane funso ili:
Mogwirizana ndi zimene Yesu ananena, tizichita chiyani kuti tizikhala osangalala?
Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:
Kodi tingasonyeze bwanji mtima wopatsa ngakhale titakhala kuti tilibe zinthu zambiri?
Kodi mukudziwa?
Baibulo limatiphunzitsa kuti tizipemphera kwa Yehova m’dzina la Yesu. (Werengani Yohane 16:23, 24.) Tikamapemphera m’dzina la Yesu, timasonyeza kuti timayamikira zimene Yesu anachita potithandiza kuti Mulungu akhale mnzathu.
ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Mulungu analemberatu zoti tizikumana ndi mavuto.”
Popeza kuti Yesu amatsanzira makhalidwe a Atate wake, kodi zimene ankachita zimasonyeza bwanji kuti si Yehova amene amachititsa kuti tizivutika?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Yesu amakonda Yehova komanso amakonda anthu. Popeza kuti Yesu amatengera makhalidwe a Atate wake, mukadziwa zambiri zokhudza Yesu mudzamudziwanso bwino Yehova.
Kubwereza
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yehova ngati mmene Yesu ankachitira?
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda anthu ngati mmene Yesu ankachitira?
Ndi khalidwe liti la Yesu limene limakusangalatsani kwambiri?
ONANI ZINANSO
Onani ena mwa makhalidwe a Yesu omwe tingatsanzire.
“Kuti Mutsanzire Yesu Muyenera . . .” (Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo, tsamba 317)
Onani chifukwa chake tiyenera kupemphera kudzera m’dzina la Yesu.
“N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupemphera M’dzina la Yesu?” (Nsanja ya Olonda, February 1, 2008)
Kodi Baibulo limanena chilichonse chokhudza mmene Yesu ankaonekera?
Kodi tikuphunzirapo chiyani tikaona mmene Yesu ankachitira zinthu ndi akazi?
“Mulungu Amafuna Kuti Akazi Azilemekezedwa” (Nsanja ya Olonda, September 1, 2012)