Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Yohane
    Nsanja ya Olonda—2008 | April 15
    • 19:11​—Polankhula ndi Pilato za munthu amene anamupereka, kodi Yesu anali kunena za Yudasi Isikariyoti? Yesu sanali kulankhula za Yudasi yekha kapena munthu wina wake, koma zikuoneka kuti anali kulankhula za anthu onse omwe anakhudzidwa ndi tchimo lomupha. Ena mwa anthu amenewa anali Yudasi, “ansembe aakulu ndi Bungwe Lalikulu lonse la Ayuda” ndiponso “anthu” amene ananyengereredwa kuti apemphe kumasulidwa kwa Baraba.​—Mat. 26:59-65; 27:1, 2, 20-22.

  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Yohane
    Nsanja ya Olonda—2008 | April 15
    • 21:15, 19. Petulo anafunsidwa ngati anakonda Yesu kuposa “izi,” kutanthauza nsomba zinali pomwepo. Motero apa Yesu anatsindika kufunika koti Petulo asankhe kutsatira Yesuyo kwa moyo wake wonse, m’malo mwa ntchito yake ya usodzi. Popeza taona nkhani za m’Mauthenga Abwino, tisasiye kukonda Yesu kwambiri kuposa china chilichonse chimene tingakopeke nacho. Inde, tiyeni tipitirize kumutsatira ndi mtima wonse.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena