Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Inuyo Mumamvera Ndani—Mulungu Kapena Anthu?
    Nsanja ya Olonda—2005 | December 15
    • 7. Kodi n’chifukwa chiyani ntchito yolalikira inawakwiyitsa ansembe aakulu?

      7 Atumwi atatsimikiza kuti sasiya kulalikira, ansembe aakulu anakwiya. Ena mwa ansembewo, ndi Kayafa yemwe, anali Asaduki, ndipo sanali kukhulupirira kuti akufa adzauka. (Machitidwe 4:1, 2; 5:17) Koma atumwiwo analimbikira kunena kuti Yesu anauka kwa akufa. Chinanso, ena mwa ansembe aakulu anali atayesetsa kuchita zotheka kuti akuluakulu a Roma awakonde. Atapatsidwa mpata wosankha Yesu kukhala mfumu yawo pozenga mlandu wa Yesuyo, ansembe aakulu anafika mpaka pofuula kuti: “Tilibe Mfumu koma Kaisara.” (Yohane 19:15)a Sikuti atumwiwo anali kungonena motsimikiza kuti Yesu anauka kwa akufa, komanso anali kuphunzitsa kuti kupatulapo dzina la Yesu, “palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Machitidwe 2:36; 4:12) Ansembe anali kuopa kuti ngati anthu ayamba kuyang’ana kwa Yesu amene anauka kwa akufa kukhala Mtsogoleri wawo, ndiye kuti Aroma adzabwera ndipo atsogoleri a Chiyudawo angataye ‘malo awo ndi mtundu wawo.’​—Yohane 11:48.

  • Kodi Inuyo Mumamvera Ndani—Mulungu Kapena Anthu?
    Nsanja ya Olonda—2005 | December 15
    • a “Kaisara” amene ansembe aakulu anavomereza pamaso pa anthu nthawi imeneyo anali Tiberiyo, Mfumu ya Roma imene anthu anaida kwambiri, ndipo iye anali mthira kuwiri ndi wambanda. Tiberiyo anali kudziwikanso monga munthu wokonda zachiwerewere zonyansa.​—Danieli 11:15, 21.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena