-
“Yesu . . . Anawakonda Mpaka pa Mapeto a Moyo Wake”‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
-
-
9 Pa tsiku limene anaphedwa, Yesu anasonyeza m’njira yapadera kwambiri kuti amadera nkhawa moyo wauzimu wa otsatira ake. Taganizirani mmene zinthu zinalili pa nthawiyo. Yesu anali atapachikidwa pamtengo ndipo ankamva ululu wosaneneka. Kuti athe kupuma bwinobwino, ayenera kuti ankafunika kudziwongola. N’zoonekeratu kuti zimenezi zinachititsa kuti amve ululu kwambiri chifukwa chakuti kulemera kwa thupi lake kunkachititsa kuti mabala a misomali m’mapazi ake aziwonjezeka kukula. Ankamvanso ululu chifukwa msana wake, womwe unali ndi mabala okhaokha, unkakhula mtengowo. Choncho ziyenera kuti zinali zovuta ndi zopweteka kwambiri kuti alankhule chifukwa ankafunika kukoka mpweya wambiri. Komabe Yesu asanafe, ananena mawu osonyeza kuti ankawakonda kwambiri mayi ake, Mariya. Yesu ataona Mariya ndi mtumwi Yohane ataima chapafupi, analankhula ndi mayi akewo momveka bwino moti anthu amene anaima pafupi anamva. Iye anati: “Mayi, kuyambira lero, uyu akhala mwana wanu.” Kenako anauza Yohane kuti: “Kuyambira lero awa akhala mayi ako.” (Yohane 19:26, 27) Yesu ankadziwa kuti mtumwi wokhulupirikayu adzasamalira Mariya mwauzimu komanso adzamupatsa zinthu zina zofunikira pa moyo wake.b
-
-
“Yesu . . . Anawakonda Mpaka pa Mapeto a Moyo Wake”‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
-
-
b Zikuoneka kuti pa nthawiyi, Mariya anali wamasiye ndipo ana ake ena anali asanakhale ophunzira a Yesu.—Yohane 7:5.
-