-
Mmene Dipo LimatipulumutsiraNsanja ya Olonda—2010 | August 15
-
-
Tikhoza Kupulumutsidwa ku Mkwiyo wa Mulungu
4, 5. N’chiyani chikusonyeza kuti mkwiyo wa Mulungu wakhala uli pa dongosolo lino la zinthu lomwe ndi loipa?
4 Baibulo ndiponso zimene zakhala zikuchitika zimasonyezeratu kuti kuchokera pa nthawi imene Adamu anachimwa, mkwiyo wa Mulungu ‘wakhala’ uli pa anthu. (Yoh. 3:36) Umboni wa zimenezi ndi wakuti palibe munthu amene safa. Ulamuliro wa Satana wotsutsana ndi Mulungu, walephera kuteteza anthu ku mavuto amene akuwonjezeka, ndipo palibe boma la anthu limene lakwanitsa kupereka zinthu zofunika pa moyo wa nzika zake. (1 Yoh. 5:19) N’chifukwa chake anthu akuvutikabe ndi nkhondo, chiwawa ndi umphawi.
-
-
Mmene Dipo LimatipulumutsiraNsanja ya Olonda—2010 | August 15
-
-
7 Mtumwi Paulo ananena kuti Yesu “akutipulumutsa ife ku mkwiyo ukubwerawo.” (1 Ates. 1:10) Pamapeto pake, Mulungu adzasonyeza mkwiyo wake mwa kuwonongeratu anthu osalapa. (2 Ates. 1:6-9) Kodi ndani adzapulumuke? Baibulo limati: “Iye wokhulupirira mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha; wosamvera Mwanayo sadzauona moyowu, koma mkwiyo wa Mulungu udzakhalabe pa iye.” (Yoh. 3:36) Inde, anthu onse a moyo amene amakhulupirira Yesu ndiponso dipo adzapulumuka pa tsiku lomaliza limene Mulungu adzasonyeza mkwiyo wake mwa kuwononga dongosolo lino la zinthu.
-