Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1988 | September 1
    • Dziŵani chimene Baibulo likunena, ndi chimene ilo kwenikweni silinena: “Koma pali thamanda m’Yerusalemu pa chipata cha nkhosa lotchedwa mu Chihebri Betesda, liri ndi makumbi asanu. Mmenemo munagona khamu lalikulu la anthu odwala, akhungu, opunduka miyendo, opuwala.​—Koma panali munthu wina apo ali nkudwala kwake zaka makumi atatu kudza zisanu ndi zitatu. Yesu pa kuwona ameneyu ali kugona, ndipo anadziŵa kuti anatha nthaŵi yaikulu pamenepo, ananena naye: ‘Ufuna kuchiritsidwa kodi?’ Wodwalayo anayankha: ‘Ambuye, ndiribe wondivika ine m’thamanda paliponse madzi avundulidwa; koma mmene ndirinkudza ine wina atsika ndisanatsike ine.’ Yesu ananena naye: ‘Tawuka, yalula mphasa yako nuyende.’ Ndipo pomwepo munthuyo anachira, nayalula mphasa yake nayenda.”​—Yohane 5:2-9.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1988 | September 1
    • Onani mzera wodukizawo m’kugwidwa mawu kwa pamwambapo kwa Yohane 5:2-9. MaBaibulo ena amaphatikiza ndime yowonjezereka yomwe imatchedwa Yohane 5:4. Kuwonjezera kumeneko kumanena chinachake chonga ichi: “Pakuti mngelo wa Ambuye ankabwera pa thamandapo nthaŵi ndi nthaŵi ndi kuvundula madzi; woyambirira kupitamo pambuyo pa kuvundulidwa kwa madziwo anakhala wa umoyo kuchokera ku matenda aliwonse amene anakanthidwa nawo.”

      Ngakhale kuli tero, unyinji wa maBaibulo amakono, kuphatikizapo New World Translation of the Holy Scriptures, amasiya ndime imeneyi. Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti m’kuthekera kulikonse iyo sinali mu Uthenga Wabwino wa Yohane. Mawu a m’munsi mu The Jerusalem Bible amawona kuti “mboni zabwino koposa” zimasiya ndime imeneyi. “Mboni zabwino koposa” zotanthauzidwa zinali mamanusikripiti achikale a Chigriki, monga ngati Codex Sinaiticus ndi Vatican 1209 (zonse ziŵiri za mzana la 4 C.E.), ndi malembedwe oyambirira a Syriac ndi Latin. Pambuyo pa kutchula ‘kusoweka kwa versi 4 kuchokera ku malemba a munusikripiti abwino koposa,’ The Expositor’s Bible Commentary ikuwonjezera kuti: “Iyo mwachisawawa imalingaliridwa kukhala kutembenuza komwe kunalowetsedwamo kulongosola kuvundulidwa kwa pa kanthaŵi kwa madzi, kumene anthu anakulingalira kukhala magwero othekera a kuchiritsa.”

      Chotero Baibulo silimanena kwenikweni kuti mngelo wochokera kwa Mulungu anapanga zoziwitsa pa thamanda la Betesda. Chabwino, kodi kuchiritsa kozizwitsa kunawoneka pamene madziwo anali ovundulidwa? Palibe wina aliyense lerolino amene anganene motsimikizirika. Mwinamwake mwa njira ina yake mwambo unakulitsidwa kuti anthu odwala kapena opunduka anachiritsidwa pamenepo. Ngati nkhani za kuchiritsidwa koyerekezeredwako zafalitsidwa, anthu osowa chochita oyembekezera kuchiritsidwa angayambe kusonkhana kumeneko. Tikudziŵa kuti ichi chachitika ku malo osiyanasiyana m’nthaŵi yathu, ngakhale pamene palibe umboni wolembedwa wa kuchiritsa kwa umulungu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena