Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kuyankha Omuyimba Mlandu
NDISABATA Yesu akuchiritsa mwamuna wina amene wakhala wodwala kwa zaka 38. Koma atsogoleri achipembedzo Achiyuda akumuimba mlandu wakuswa Sabata. Yesu akuyankha kuti: “Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, inenso ndigwira ntchito.” Mosasamaia kanthu za zodzinenera za Afarisi, ntchito ya Yesu siiri pakati pa zoletsedwa ndi lamulo la Sabata. Ntchito yake ya kulalikira ndi kuchiritsa iri gawo lochokera kwa Mulungu, ndipo, motsatira chitsanzo cha Mulungu, iye akupitirizabe kuichita tsiku lirilonse. Komabe, yankho lake likupangitsa Ayuda kukhaladi okwiya kwambiri koposa poyamba, ndipo akufunafuna kumupha. Chifukwa ninji?
Chiri chifukwa chakuti tsopano sikokha kuti iwo amakhulupirira kuti Yesu akuswa Sabata, koma akulingalira kuti kudzinenera kwake kukhala Mwana weniweni wa Mulungu ndiko mwano. Komabe, Yesu sakuchita mantha ndipo akupitirizabe kuyankha za unansi wake woyanjidwa ndi Mulungu. “Atate akonda Mwana,” iye akutero, “ndipo anamuwonetsa zonse azichita yekha.”“
Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo,” Yesu akupitiriza kutero, “momwemonso, Mwana apatsa moyo iwo amene iye afuna.” Ndithudi, Mwanayo akuukitsa kale akufa mwanjira yauzimu! “lye wakumva mawu anga, ndikukhulupirira iye amene anandituma ine,” Yesu akutero, “wachokera ku imfa, nalowa m’moyo.” Inde, iye akupitirizabe kuti: “Ikudza nthawi, ndipo iripo tsopano, imene akufa adzamva mawu a [Mwana wa Mulungu; ndipo akumva adzakhala ndi moyo.”
Ngakhale kuli kwakuti kufikira panthawi ino panalibe cholembedwa chakuti Yesu anali ataukitsa kwenikweni munthu aliyense kwa akufa, iye akuuza omuimba mlandu kuti chiukiriro chenicheni chotero cha akufa chidzachitika. “Musazizwe ndi ichi,” iye akutero, “kuti ikudza nthawi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira.”
Mwachiwonekere kufikira panthawi ino Yesu anali asanalongosole konse poyera motero mbali yake yofunika m’chifuno cha Mulungu mwanjira yomvekera bwino ndi yotsimikizirika. Komabe otsutsa Yesuwo ali ndi zambiri kuposa kuchitira kwake umboni za zinthu izi. ‘Munatuma anthu kwa Yohane,’ Yesu akuwakumbutsa, ‘ndipo iye anachitira umboni chowonadi.’
Zaka ziwiri zokha izi zisanachitike, Yohane Mbatizi anauza atsogoleri achipembedzo Achiyuda amenewa za lye wakudza pambuyo pake. Akumawakumbutsa za ulemu umene iwo anali nawo poyamba ponena za Yohane woikidwa m’ndende panthawiyo, Yesu amati: “Inu munafuna kukondwera m’kuunika kwake kanthawi.” Yesu akuwakumbutsa izi ncholinga cha kuwathandiza, inde, kuwapulumutsa. Komabe, iye sakudalira paumboni wa Yohane.
“Ntchito zomwezo ndizichita [kuphatikizapo chozizwitsa chimene anali atangochita kumene], zindichitira umboni kuti Atate anandituma ine.” Koma kuwonjezera pa zimenezo, Yesu akupitirizabe kuti: “Atate wonditumayo, iyeyu wandichitira ine umboni.” Mwachitsanzo, Mulungu anachitira umboni za Yesu, paubatizo, akumati: “Uyu ndiye Mwana wanga, wokondedwa.”
Kwenikweni, oimba mlandu Yesu alibe chodzikhululukira cha kumkanira. Malemba enieniwo amene iwo akudzinenera kuti amawasanthula amamchitira umboni! “Pakuti mukadakhulupirira Mose, mukadakhulupirira ine,” Yesu akumaliza, “pakuti iyeyu analemba za ine. Koma ngati simukhulupirira malembo a iyeyu, mudzakhulupirira bwanji mawu anga?” Yohane 5:17-47; 1:19-27; Mateyu 3:17.
◆ Kodi nchifukwa ninji ntchito ya Yesu siri kuswedwa kwa Sabata?
◆ Kodi ndimotani mmene Yesu akulongosolera mbali yake yofunika m’chifuno cha Mulungu?
◆ Kutsimikizira kuti iye ali Mwana wa Mulungu, kodi ndikuumboni wayani kumene Yesu akusonyako?