Maphunziro m’Nthaŵi za m’Baibulo
“Muziwaphunzitsa ana anu.”—DEUTERONOMO 11:19.
1. Kodi nchiyani chimasonyeza kuti Yehova amafuna atumiki ake kukhala ophunzira?
YEHOVA ndiye Mphunzitsi Wamkulu. Iye sanasiyepo atumiki ake mumkhalidwe waumbuli. Wakhala ali wofunitsitsa kugaŵana nawo chidziŵitso. Amawaphunzitsa chifuno chake ndi njira zake. Kwa zaka zikwi zosawerengeka Mwana wake wobadwa yekha anali naye, mosalekeza akumaphunzira monga “mmisiri” wa Mulungu. (Miyambo 8:30) Pamene anali pa dziko lapansi Yesu ananena kuti: “Koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.” (Yohane 8:28) Ponena za Mulungu monga Mphunzitsi Wosayerekezeka, Elihu anafunsa kuti: “Mphunzitsi wakunga iye ndani?” (Yobu 36:22) Mneneri Yesaya analankhula za Yehova kukhala monga “Mlangizi Wamkulu” wa anthu Ake ndipo analosera kuti: “Ndipo ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.” (Yesaya 30:20, NW; 54:13) Mosakaikira, Yehova amafunadi kuti zolengedwa zake zaluntha zikhale ndi chidziŵitso ndi zophunzira bwino.
Maphunziro a Makolo Akale
2, 3. (a) Kodi ndimotani mmene makolo akale okhulupirika anawonera maphunziro a ana awo, ndipo kodi ndimalangizo otani amene Yehova anapereka kwa Abrahamu? (b) Kodi malangizo akuphunzitsa mbadwa za Abrahamu anali ndichifuno chachikulu chotani?
2 Chofunikira china chachikulu cha mutu wabanja m’nthaŵi za makolo akale chinali kuphunzitsa ana ake ndi apanyumba ake. Kwa atumiki a Mulungu kuphunzitsa ana awo kunali thayo lachipembedzo. Yehova ananena za mtumiki wake Abrahamu kuti: “Chifukwa ndamdziŵa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye.”—Genesis 18:19.
3 Mawu aumulungu ameneŵa amasonyeza kuti Yehova amalingalira maphunziro kukhala ofunika kwambiri. Mulungu anafuna Abrahamu, Isake, ndi Yakobo kuphunzitsa apanyumba pawo m’njira Zake za chilungamo ndi chiweruziro kotero kuti mibadwo ya mtsogolo ikakhale yoyenerera kusunga njira ya Yehova. Motero, Yehova akakwaniritsa lonjezo lake lonena za mbewu ya Abrahamu ndi kudalitsa “mitundu yonse ya dziko lapansi.”—Genesis 18:18; 22:17, 18.
Dongosolo la Maphunziro m’Israyeli
4, 5. (a) Kodi chinasiyanitsa maphunziro a Aisrayeli ndi a mitundu ina nchiyani? (b) Kodi nkusiyana kwina kofunika kotani kofotokozedwa mu Encyclopaedia Judaica, ndipo mosakaikira nchiyani chinapangitsa kusiyanako?
4 Encyclopaedia Judaica imati: “Baibulo ndilo magwero aakulu akumvetsetsa njira ya maphunziro m’Israyeli wakale.” Yehova anagwiritsira ntchito Mose monga mphunzitsi woyamba waumunthu wa Israyeli. (Deuteronomo 1:3, 5; 4:5) Mose analankhula mawu amene anaperekedwa kwa iye ndi Yehova. (Eksodo 24:3) Chotero, kwenikweni, Mulungu anali Mphunzitsi woyambirira wa Israyeli. Zimenezi zinasiyanitsa maphunziro a Israyeli ndi a mitundu ina.
5 Bukhu limodzimodzilo limati: “Maphunziro apamwamba kapena kuphunzira m’mabukhu mu Mesopotamiya ndi Igupto kunali kwa mwambo ndi kolekezera kwa gulu la alembi, zimene zikuwonekera kuti sizinali zotero mu Israyeli. Mosakaikira kusiyana kunali chifukwa cha kalembedwe ka alifabeti kosavutirapo kogwiritsiridwa ntchito ndi Ahebri . . . Kufunika kwa kalembedwe ka alifabeti kaamba ka mbiri ya maphunziro sikuyenera kunyalanyazidwa. Kunathetsa miyambo yakukhala ndi alembi amwambo a Igupto, Mesopotamiya, ndi Kanani wa m’zaka za chikwi chachiŵiri. Kukhala wodziŵa kuŵerenga ndi kulemba sikunalinso chinthu chozindikiritsa ndi kupatulikitsa munthu monga wa kagulu ka alembi ndi ansembe aukatswiri, okhala ndi chidziŵitso m’zolembedwa zovuta kumvetsetsa za zilembo za zizindikiro ndi za zithunzi.”
6. Kodi ndiumboni uti wa Baibulo umene ulipo wakuti kuyambira pachiyambi pa mbiri yawo, Aisrayeli anali anthu odziŵa kuŵerenga ndi kulemba?
6 Baibulo limapereka umboni wakuti Aisrayeli anali anthu okhoza kuŵerenga ndi kulemba. Ngakhale asanaloŵe mu Dziko Lolonjezedwa, anauzidwa kulemba malamulo a Yehova pa mphuthu zanyumba zawo ndi pa zipata zawo. (Deuteronomo 6:1, 9; 11:20; 27:1-3) Pamene kuli kwakuti lamulo limeneli mosakaikira linali lophiphiritsira, likanakhala lopanda tanthauzo kwa Mwisrayeli ngati sanadziŵe kuŵerenga ndi kulemba. Malemba onga ngati Yoswa 18:9 ndi Oweruza 8:14 amasonyeza kuti ena anadziŵa kalekale kulemba kuwonjezera pa atsogoleri onga ngati Mose ndi Yoswa ufumu wa mfumu imodzi usanakhazikitsidwe mu Israyeli.—Eksodo 34:27; Yoswa 24:26.
Njira Zophunzitsira
7. (a) Malinga ndi Malemba, kodi ndani anapereka maphunziro oyambirira kwa ana Achiisrayeli? (b) Kodi katswiri wa Baibulo Wachifalansa akupereka chidziŵitso chotani?
7 Mu Israyeli, ana anaphunzitsidwa kuyambira pamsinkhu waung’ono kwambiri ndi onse aŵiri atate ndi amayi. (Deuteronomo 11:18, 19; Miyambo 1:8; 31:26) Mu Dictionnaire de la Bible la Chifalansa, katswiri wa Baibulo E. Mangenot analemba kuti: “Atangoyamba kumene kulankhula, mwana anaphunzira ndime zochepa za Chilamulo. Amayi wake anabwereza vesi; pamene analidziŵa, anamupatsa vesi lina. Pambuyo pake, lemba lolembedwa la mavesi amene anakhoza kuwatchula pamtima anapatsidwa kwa anawo. Motero, anaphunzitsidwa kuŵerenga, ndipo pamene anakula, anapitiriza malangizo awo achipembedzo mwa kuŵerenga ndi kusinkhasinkha pa lamulo la Ambuye.”
8. (a) Kodi ndinjira yaikulu yophunzitsira yotani imene inagwiritsidwa ntchito mu Israyeli, koma ndi mfundo yofunika yotani? (b) Kodi nzothandiza kukumbukira zotani zimene zinagwiritsidwa ntchito?
8 Zimenezi zikusonyeza kuti njira yakuphunzitsa yaikulu yogwiritsidwa ntchito inali yakuloŵeza zinthu pamtima. Zinthu zophunziridwa ponena za malamulo a Yehova ndi zochita zake ndi anthu ake zinafunikira kuloŵa mu mtima. (Deuteronomo 6:6, 7) Zinafunikira kulingaliridwa. (Salmo 77:11, 12) Kuthandiza achichepere ndi akulu kuloŵeza, njira zosiyanasiyana zolowezera zinagwiritsidwa ntchito. Zimenezi zinaphatikizapo malembo a alifabeti, mavesi otsatizana m’salmo oyamba ndi chilembo chosiyana, mu ndandanda ya alifabeti (monga ngati Miyambo 31:10-31, NW); mawu oyamba ndi chilembo chofanana kapena akamvekedwe kofanana; ndi kagwiritsiridwe ka ziŵerengelo, monga zotchulidwa m’theka lomalizira la Miyambo chaputala 30. Mokondweretsa, Kalenda ya Gezer, imodzi ya zitsanzo zakale kwambiri za zolembedwa Zachihebri, imalingaliridwa ndi akatswiri ena kukhala zolembedwa zoloŵeza za mwana wa sukulu.
Maphunziro
9. (a) Kodi mbali yofunika ya programu ya maphunziro a ana Aisrayeli inali yotani? (b) Kodi nazonse wa Baibulo ananenanji za kuphunzitsa kochitidwa mogwirizana ndi mapwando apachaka?
9 Maphunziro mu Israyeli sanali olekezera pakuphunzira kuŵerenga ndi kulemba. Phunziro lina lofunika lophunzitsidwa linali mbiri yakale. Kuphunzira zochita za Yehova zodabwitsa m’chiyanjo cha anthu ake kunali mbali yofunika kwambiri ya maphunziro. Zochitika za m’mbiri yakale zimenezi zinayenera kuphunzitsidwa ku mbadwo ndi mbadwo. (Deuteronomo 4:9, 10; Salmo 78:1-7) Chikondwerero cha mapwando apachaka chinapereka mwaŵi wabwino kwa mutu wabanja kuphunzitsa ana ake. (Eksodo 13:14; Levitiko 23:37-43) Mogwirizana ndi zimenezi The International Standard Bible Encyclopedia imasimba kuti: “Mwa malangizo a atate m’nyumba ndi kulongosola kufunika kwa mapwando, ana Achihebri anaphunzitsidwa za mmene Mulungu anadzisonyezera Iyemwini kwa iwo m’nthaŵi zakale, za mmene anafunikira kukhalira ndi moyo m’nthaŵi imeneyo, ndi za malonjezo a Mulungu ponena za mtsogolo mwa anthu Ake.”
10. Kodi ndimaphunziro akuchita zinthu otani amene anaperekedwa kwa asungwana? kwa anyamata?
10 Chiphunzitso chamakolo chinaphatikizapo kulangiza kuchita zinthu moyenerera. Atsikana anaphunzitsidwa maluso apanyumba. Chaputala chomaliza cha Miyambo chimasonyeza kuti amenewa anali ambiri ndi osiyanasiyana; anaphatikizapo kupota ulusi, kuomba nsalu, kuphika, kugula ndi kugulitsa, ndi ntchito zina zapanyumba. Anyamata anaphunzitsidwa ntchito za atate wawo, kaya inali yaulimi kapena malonda kapena ntchito yaumisiri. Mkupita kwanthaŵi arabi Achiyuda mozoloŵera anali kumati: “Uyo amene saphunzitsa mwana wake wamwamuna ntchito yofunikira akumlera kukhala mbala.”
11. Kodi nchiyani chimasonyeza chifuno chachikulu cha maphunziro mu Israyeli, ndipo kodi zimenezo ziri ndi phunziro lotani kwa achichepere lerolino?
11 Kuzama kwauzimu kwa njira zophunzitsira zogwiritsidwa ntchito mu Israyeli nkowonekeratu m’bukhu lonse la Miyambo. Kumasonyeza kuti chifuno chinali cha kuphunzitsa “achibwana” zinthu zapamwamba zonga nzeru, mwambo, kumvetsetsa, chidziŵitso, chiweruzo, kuchenjeza, kudziŵa, ndi kulingalira—zonsezi “m’kuwopa Yehova.” (Miyambo 1:1-7; 2:1-14) Kumagogomezera zolinga zimene ziyenera kusonkhezera mtumiki wa Mulungu lerolino kuwongolera maphunziro ake.
Ansembe, Alevi, ndi Aneneri
12. Kodi ndani kusiyapo makolo amene anatenga mbali kuphunzitsa anthu a Israyeli, ndipo kodi tanthauzo lalikulu la liwu Lachihebri lotembenuzidwa “chilamulo” nlotani?
12 Pamene kuli kwakuti maphunziro oyambirira anali kuperekedwa ndi makolo, Yehova anaphunzitsanso anthu ake mwa ansembe, Alevi osakhala ansembe, ndi aneneri. M’madalitso ake omalizira pa fuko la Levi, Mose ananena kuti: “Adzaphunzitsa Yakobo maweruzo anu, ndi Israyeli chilamulo chanu.” (Deuteronomo 33:8, 10) Mfundo yofunika kudziŵa ndiyo yakuti, liwu lakuti “chilamulo” mu Chihebri (toh·rahʹ) linatengedwa ku magwero amene mneni wake amatanthauza “kusonyeza,” “kuphunzitsa,” “kulangiza.” Encyclopaedia Judaica imati: “Chotero tanthauzo la liwulo [torah] ndilo ‘kuphunzitsa,’ ‘chiphunzitso,’ kapena ‘chilangizo.’”
13. Kodi nchifukwa chiyani Chilamulo cha Israyeli chinali chosiyana ndi madongosolo amalamulo a mitundu ina?
13 Zimenezinso zinasiyanitsa Aisrayeli kwa mitundu ina ndipo ngakhale kwa mitundu yamakono. Maboma alerolino ali ndi mipambo ya malamulo amene anthu ochuluka amangodziŵa ochepa okha. Pamene anthu alakwira lamulo, ayenera kulipira maloya ndalama zambiri kuti awatetezere. Sukulu za malamulo ziri za akatswiri okha. Komabe mu Israyeli Chilamulo chinali njira ya Mulungu yakuuzira anthu ake mmene anawafunira iwo kuti ampembedzere ndi kukhala ndi moyo mogwirizana ndi chifuno chake. Mosiyana ndi mipambo ina ya malamulo, chinaphatikizapo chikondi cha pa Mulungu ndi mnansi. (Levitiko 19:18; Deuteronomo 6:5) Chilamulo sichinali konse bukhu la malamulo osagwira mtima. Linapereka chiphunzitso, maphunziro, ndi chilangizo m’njira ya moyo imene inafunikira kuphunziridwa.
14. Kodi nchifukwa chimodzi chiti chimene Yehova anakanira unsembe wa Alevi? (Malaki 2:7, 8)
14 Panthaŵi zina, ansembe ndi Alevi anakwaniritsa mathayo awo akuphunzitsa anthu. Koma kaŵirikaŵiri, ansembe ananyalanyaza ntchito yawo yakuphunzitsa mtundu. Kusoŵeka kwa maphunziro m’Chilamulo cha Mulungu kumeneku kunali kudzakhala ndi zotulukapo zowopsa kwa onse aŵiri ansembe ndi anthu. Mu zaka za zana za chisanu ndi chitatu B.C.E., Yehova analosera kuti: “Anthu anga aonongeka chifukwa cha kusadziŵa; popeza unakana kudziŵa, inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga; popeza waiŵala chilamulo cha Mulungu wako, inenso ndidzaiŵala ana ako.”—Hoseya 4:6.
15. (a) Kuwonjezera pa ansembe, kodi Yehova anaika ndani monga aphunzitsi mu Israyeli, ndipo kodi katswiri wa Baibulo analemba chiyani ponena za thayo lawo monga aphunzitsi? (b) Kodi pomalizira chinachitika nchiyani kwa Israyeli ndi Yuda chifukwa chakukana chidziŵitso cha Yehova ndi njira zake?
15 Kuwonjezera pa ansembe, Yehova anaika aneneri monga aphunzitsi. Timaŵerenga kuti: “Yehova anachitira umboni Israyeli ndi Yuda mwa dzanja la mneneri aliyense, ndi mlauli aliyense, ndi kuti, bwererani kuleka ntchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa chilamulo chonse ndinachilamulira makolo anu, ndi kuchitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri.” (2 Mafumu 17:13) Ponena za ntchito ya aneneri monga aphunzitsi, katswiri wa Baibulo Wachifalansa Roland de Vaux analemba kuti: “Anenerinso anali ndi thayo la kulangiza anthu; imeneyi inali mbali ya ntchito yawo yakuneneratu za mtsogolo. Ndipo ulosi wouziridwa unaika ulamuliro wa mawu a Mulungu pakulalikira kwawo. Kuli kowonekeratu kuti mu ufumuwo aneneri anali aphunzitsi achipembedzo ndi amakhalidwe kwa anthu; ndipo, tingawonjeze kuti, anali aphunzitsi abwino kwambiri, ngati sanalinso olabadiridwa koposa.” Mwa kusoŵeka chiphunzitso choyenerera cha ansembe ndi Alevi pamodzi ndi kulephera kulabadira aneneri a Yehova, Aisrayeli anasiya njira za Yehova. Asamariya anagwa kwa Asuri mu 740 B.C.E., ndipo Yerusalemu ndi kachisi wake anawonongedwa ndi Ababulo mu 607 B.C.E.
Maphunziro Mkati ndi Pambuyo pa Ukapolo
16, 17. (a) Kodi ndiprogramu yamaphunziro yotani imene inakakamiziridwa pa Danieli ndi anzake atatu? (b) Kodi chinawakhozetsa nchiyani kuchita maphunziro Achibabulo komabe kukhala okhulupirikabe kwa Yehova?
16 Pafupifupi zaka khumi Yerusalemu asanawonongedwe, Mfumu Yoyakini ndi gulu la akalonga ndi nduna anatengeredwa kumka ku Babulo ndi Mfumu Nebukadinezara. (2 Mafumu 24:15) Pakati pawo panali Danieli ndi nduna zina zitatu zachichepere. (Danieli 1:3, 6) Nebukadinezara analamulira kuti onse anayi anayenera kupatsidwa kosi ya maphunziro kwa zaka zitatu “kuti awaphunzitse m’mabukhu, ndi manenedwe a Akasidi.” Ndiponso, anapatsidwa “gawo la chakudya cha mfumu tsiku ndi tsiku, ndi la vinyo wakumwa iye.” (Danieli 1:4, 5) Zimenezi zinali zaupandu kwambiri kaamba ka zifukwa zambiri. Mwachiwonekere, programu ya malangizo sinali kokha kosi ya zaka zitatu ya chilankhulidwe. Liwulo “Akasidi” m’ndimeyi likulingaliridwa ndi ena kukhala likusonya, “osati Ababulo monga anthu, koma monga gulu la anthu ophunzira.” (The Soncino Books of the Bible) Mu ndemanga zake pa bukhu la Danieli, C. F. Keil anati: “Danieli ndi anzakewo anali kukaphunzitsidwa nzeru za ansembe a Akasidi ndi amuna ophunzira, zimene zinaphunzitsidwa m’masukulu a Ababulo.” Kupatsidwa kwawo chakudya cha chifumu kunawaika paupandu wakuswa lamulo la ziletso pachakudya loperekedwa ndi Chilamulo cha Mose. Kodi iwo anachita motani?
17 Monga wolankhulira wa nduna zachichepere za Chiyuda zinayizo, Danieli anafotokoza momvekera kuyambira pachiyambi kuti iwo sakadya kapena kumwa zolakwira chikumbumtima chawo. (Danieli 1:8, 11-13) Yehova anadalitsa kaimidwe kolimba kameneka ndi kufewetsa mtima wa woyang’anira Wachibabulo. (Danieli 1:9, 14-16) Ponena za maphunziro awo, zochitika zotsatirapo mmiyoyo ya achichepere anayi Achihebri onsewo zinasonyeza kuti mosakaikira maphunziro awo a zaka zitatu mu mkhalidwe wa Babulo sanawachititse kuchoka pa unansi wawo ndi Yehova ndi kulambira kwake koyera. (Danieli, chaputala 3 ndi 6) Yehova anawatheketsa kutuluka opanda banga m’programu ya zaka zitatu yokakamiza imeneyi m’maphunziro apamwamba a ku Babulo. “Koma anyamata ameneŵa anayi, Mulungu anawapatsa chidziŵitso ndi luntha la m’mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Danieli anali nalo luntha la m’masomphenya ndi maloto onse. Ndipo m’mawu ali onse anzeru ndi aluntha, amene mfumu inawafunsira, inawapeza akuposa alembi ndi openda onse muufumu wake wonse.”—Danieli 1:17, 20.
18. Kodi ndiprogramu iti yamaphunziro imene inachitidwa mu Yuda pambuyo pa ukapolo wa Babulo?
18 Pambuyo pa ukapolo wa ku Babulo, ntchito yaikulu yakuphunzitsa inachitidwa ndi Ezara, wansembe amene, “adaikiratu mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita, ndi kuphunzitsa m’Israyeli malemba ndi maweruzo.” (Ezara 7:10) Anathandizidwa ndi Alevi okhulupirika, amene “anadziŵitsa anthu chilamulocho.” (Nehemiya 8:7) Ezara anali katswiri wa Baibulo ndi “mlembi waluntha.” (Ezara 7:6) Munali m’tsiku lake kuti alembi anakhala otchuka monga gulu.
Masukulu Achirabi
19. Kodi ndikagulu ka aphunzitsi kotani kamene kanakhalapo mu Israyeli panthaŵi imene Yesu anadza kudziko lapansi, ndipo kodi mpazifukwa zazikulu ziti zimene iye ndi ophunzira ake sanaloŵe maphunziro apamwamba Achiyuda?
19 Panthaŵi imene Yesu anawonekera padziko lapansi, alembi anakhala kagulu ka aphunzitsi aluntha, okhulupirira kwambiri miyambo koposa ziphunzitso zowona za Mawu a Mulungu. Iwo anakonda kutchulidwa “Rabi,” limene linafikira kukhala dzina laulemu lotanthauza “Mbuye Wolemekezeka (koposa).” (Mateyu 23:6, 7, NW, mawu amtsinde) M’Malemba Achikristu Achigiriki, alembi kaŵirikaŵiri amagwirizanitsidwa ndi Afarisi, amene ena a iwo anali aphunzitsi a Chilamulo. (Machitidwe 5:34) Yesu anatsutsa magulu onse aŵiri opangitsa mawu a Mulungu kukhala opanda phindu chifukwa cha miyambo yawo ndi “kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.” (Mateyu 15:1, 6, 9) Mposadabwitsa kuti Yesu ngakhale ochuluka a ophunzira ake sanaphunzire m’masukulu achirabi.—Yohane 7:14, 15; Machitidwe 4:13; 22:3.
20. Kodi kupenda maphunziro a m’nthaŵi za m’Baibulo kumeneku kwatisonyezanji, ndipo kodi nchiyani chimasonyeza kuti atumiki a Yehova amafunikira maphunziro?
20 Kupenda kumeneku kwa maphunziro m’nthaŵi za m’Baibulo kwasonyeza kuti Yehova ndiye Mlangizi Wamkulu wa anthu ake. Kupyolera mwa Mose, Mulungu analinganiza dongosolo labwino la maphunziro mu Israyeli. Koma pambuyo pa nthaŵi yaitali, dongosolo la maphunziro apamwamba Achiyuda linayambitsidwa limene linaphunzitsa zinthu zosiyana ndi Mawu a Mulungu. Ngakhale kuti Yesu sanapite ku masukulu otero Achiyuda, iye anali Mphunzitsi wosayerekezereka. (Mateyu 7:28, 29; 23:8; Yohane 13:13) Iye analamuliranso ophunzira ake kuphunzitsa, kufikira ku mapeto a dongosolo la zinthu. (Mateyu 28:19, 20) Kuti achite zimenezi anafunikira kukhala aphunzitsi abwino ndipo mwachiwonekere akafunikira maphunziro. Chotero kodi ndimotani mmene Akristu owona ayenera kuwawonera maphunziro lerolino? Funso limeneli lidzapendedwa m’nkhani yathu yotsatira.
Kuyesa Chikumbukiro
◻ Kodi nchifukwa chiyani tingakhale otsimikizira kuti Yehova ali wokondweretsedwa m’maphunziro a atumiki ake?
◻ Kodi maphunziro a Israyeli anali osiyana m’mbali ziti ndi maphunziro a mitundu ina?
◻ Kodi ana Achiisrayeli analandira maphunziro otani?
◻ Kodi anagwiritsira ntchito njira zophunzitsira zotani mu Israyeli?
◻ Kodi nchifukwa ninji Yesu ndi ophunzira ake sanapite ku masukulu Achiyuda a maphunziro apamwamba?
[Chithunzi patsamba 14]
Maphunziro okakamiza mu Babulo sanapambutse Danieli ndi atsamwali ake kwa Yehova