Mutu 2
Mfundo Yaikulu ya M’Baibulo
Kumasulira Malemba Kwa nthawi yaitali, ophunzira Baibulo oona mtima akhala asakumvetsa zinsinsi za m’buku la Chivumbulutso. Koma Mulungu amadikira nthawi yoyenera kuti aulule zinsinsi zimenezo. Kodi akuziulula motani, anayamba liti ndiponso akuululira ndani? Mzimu wa Mulungu wokha ndi umene ungaulule zinsinsizo pa nthawi yake yoyenera. (Chivumbulutso 1:3) Zinsinsi zopatulikazo zikuululidwa kwa akapolo okhulupirika a Mulungu padziko lapansi kuti akhale olimba mtima polengeza za ziweruzo zake. (Mateyu 13:10, 11) Tikudziwa kuti n’zotheka kuti mwina malemba ena sitinawafotokoze molondola kwambiri m’buku lino. Tikugwirizana ndi mawu amene Yosefe analankhula kale, akuti: “Kodi Mulungu sindiye amamasulira” zinsinsi? (Genesis 40:8) Komabe, tikukhulupirira kwambiri kuti mfundo za m’buku lino zikugwirizana ndi Baibulo lonse, ndipo zikusonyeza mmene zochitika m’dzikoli masiku ano zakwaniritsira ulosi wa Mulungu mochititsa chidwi.
1. Kodi cholinga chachikulu cha Yehova n’chiyani?
MWAMBI wina wa m’Baibulo umati: “Mapeto a chinthu amakhala bwino kuposa chiyambi chake.” (Mlaliki 7:8) M’buku la Chivumbulutso timawerenga mmene Yehova adzakwaniritsire cholinga chake chachikulu chomwe ndi kuyeretsa dzina lake m’chilengedwe chonse. Mulungu ananena mobwerezabwereza kudzera mwa mneneri wake wina m’mbuyomo kuti: “Adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”—Ezekieli 25:17; 38:23.
2. Kodi buku la Chivumbulutso ndiponso mabuku ena oyambirira a m’Baibulo angatithandize kudziwa zinthu zosangalatsa ziti?
2 Mabuku oyambirira a m’Baibulo akufotokoza mmene nkhani zosiyanasiyana zinayambira, ndipo buku la Chivumbulutso limasonyeza mmene nkhanizo zidzathere. Kuphunzira nkhani zimenezi mozama kungatithandize kumvetsa nkhani zina zikuluzikulu komanso kukhala ndi chithunzi chabwino cha zolinga za Mulungu. Kuchita zimenezi n’kosangalatsa kwambiri. Komanso zingatithandize kuti tichite zinthu zonse zofunikira kuti tidzasangalale ndi zinthu zabwino zimene zili m’tsogolo. (Salimo 145:16, 20) Panopa tingachite bwino kukambirana chiyambi cha nkhani zonse za m’Baibulo ndiponso mfundo yake yaikulu, kuti tidziwe nkhani yaikulu kwambiri imene ikukhudza anthu tonsefe. Tidziwanso zimene Mulungu wakonza pofuna kuthetsa nkhaniyo. Mulungu watifotokozera zinthu zimenezi momveka bwino.
3. Kodi ndi ulosi uti wa m’buku la Genesis umene pagona mfundo yaikulu ya m’Baibulo lonse, kuphatikizapo nkhani za m’buku la Chivumbulutso?
3 Buku la Genesis, lomwe ndi loyambirira m’Baibulo, limatiuza za “chiyambi” ndipo limafotokoza zinthu zimene Mulungu analenga. Bukuli limafotokozanso kuti Mulungu analenga munthu, yemwe ndi cholengedwa chapadera pa zolengedwa zonse za padziko lapansi. M’buku la Genesis mulinso ulosi woyambirira umene Mulungu ananena yekha zaka 6,000 zapitazo m’munda wa Edeni. Mulungu ananena ulosiwu Satana atagwiritsira ntchito njoka ponyenga mkazi woyambirira, Hava. Kenako mkaziyo anakopa mwamuna wake Adamu kuti nayenso aphwanye lamulo la Yehova podya chipatso cha “mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa.” Poweruza banja lochimwalo, Mulungu anauza njokayo kuti: “Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake. Mbewu ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza chidendene.” (Genesis 1:1; 2:17; 3:1-6, 14, 15) Mfundo yaikulu ya m’Baibulo lonse, kuphatikizapo nkhani za m’buku la Chivumbulutso, yagona pa ulosi umenewu.
4. (a) Kodi chinachitika n’chiyani kwa makolo athu oyamba Mulungu atanena ulosi woyambirira? (b) Kodi pali mafunso otani okhudza ulosi woyambirira, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kudziwa mayankho ake?
4 Mulungu atangonena ulosi umenewu, nthawi yomweyo anathamangitsa makolo athu oyambirirawo m’munda wa Edeni. Iwo analibenso chiyembekezo chilichonse chokhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso. Yehova anawathamangitsira kunja kwa munda wa Edeni, kumalo amene kunalibe chilichonse, ndipo anayamba kukhala moyo wovutika. Mulungu anawaweruza kuti adzafa, ndipo ana onse amene anabereka anali ochimwa. (Genesis 3:23–4:1; Aroma 5:12) Koma kodi ulosi umene Mulungu ananena m’munda wa Edeni ukutanthauza chiyani? Kodi ndani amene ulosiwu ukuwakhudza? Nanga ukugwirizana bwanji ndi nkhani za m’buku la Chivumbulutso? Kodi uli ndi uthenga wotani kwa ife masiku ano? Kuti tipeze mpumulo ku mavuto amene anayamba chifukwa cha uchimo umene unachititsa Yehova kunena ulosi umenewu, tiyenera kudziwa mayankho a mafunso amenewa.
Kodi “Njoka” Ndiponso “Mkazi” Ndani?
5. Njoka itanyenga Hava, kodi panayambika nkhani ziti zokhudza ulamuliro wa Mulungu ndiponso dzina lake, nanga nkhani zimenezi zidzathetsedwa bwanji?
5 Ponena ulosi wa pa Genesis 3:15, Mulungu ankalankhula ndi njoka imene inanamiza Hava. Njokayo inamunamiza kuti saafa akapanda kumvera Mulungu, koma adzakhala wodziimira payekha, ngati Mulungu. Pamenepa njokayo inalankhula ngati kuti Yehova ndi wabodza komanso kuti anthu zinthu zingawayendere bwino kwambiri ngati atakana ulamuliro wa Mulungu, yemwe amalamulira zinthu zonse. (Genesis 3:1-5) Ulamuliro wa Yehova unatsutsidwa ndipo dzina lake labwino linaipitsidwa. Buku la Chivumbulutso limafotokoza mmene Yehova, Woweruza wachilungamo, adzagwiritsire ntchito Ufumu wa Mwana wake, Yesu Khristu, posonyeza kuti Mulunguyo ndi woyenera kulamulira komanso poyeretsa dzina lake.—Chivumbulutso 12:10; 14:7.
6. Kodi buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti ndani amene analankhula kwa Hava kudzera mwa njoka?
6 Kodi mawu akuti “njoka” amene akutchulidwa mu ulosiwu akutanthauza njoka yeniyeni? Ayi. Buku la Chivumbulutso limatiuza za mngelo wina woipa kwambiri amene analankhula kudzera mwa njoka ija. Mngelo woipayu ndiye “chinjokacho . . . , njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” Chinjoka chimenechi n’chimene ‘chinanamiza Hava ndi chinyengo chake.’—Chivumbulutso 12:9; 2 Akorinto 11:3.
7. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti mkazi wotchulidwa pa Genesis 3:15 akuimira zolengedwa zauzimu?
7 Lemba la Genesis 3:15 limanenanso za “mkazi.” Kodi mkazi ameneyu ndi Hava? N’kutheka kuti Havayo anaganiza kuti akunena za iyeyo. (Yerekezerani ndi Genesis 4:1) Komatu zinali zosatheka kuti Hava ndi Satana akhale pa udani wosatha chifukwa Hava anamwalira kalekale ndipo tsopano patha zaka zoposa 5,000. Komanso popeza kuti Njoka imene Yehova analankhula nayo inali mngelo woipa, ndiye kuti mkazi ameneyunso ayenera kuimira gulu la zolengedwa zauzimu. Lemba la Chivumbulutso 12:1, 2 likutsimikizira zimenezi chifukwa limasonyeza kuti mkazi wophiphiritsira ameneyu akuimira mbali yakumwamba ya gulu la Yehova, yomwe yapangidwa ndi zolengedwa zauzimu.—Onaninso Yesaya 54:1, 5, 13.
Mbewu Ziwiri Zodana
8. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita chidwi kwambiri ndi zimene zifotokozedwe zokhudza mbewu ziwiri zotchulidwa mu ulosi wa pa Genesis 3:15?
8 Lemba la Genesis 3:15 limatchulanso mbewu ziwiri. Tiyenera kuchita chidwi kwambiri ndi mbewu zimenezi chifukwa zikukhudza nkhani yaikulu ya amene ali woyenera kulamulira dzikoli. Nkhani imeneyi ikukhudza aliyense wa ife, mwana kapena wamkulu. Kodi inuyo mungakonde kukhala kumbali ya mbewu iti?
9. Kodi mbewu ya Njoka ikuphatikizapo ndani?
9 Poyamba, ulosiwu ukutchula za mbewu ya Njoka. Kodi mbewu imeneyi n’chiyani? Ikuphatikizapo angelo amene anagwirizana ndi Satana pogalukira Mulungu ndipo kenako “anaponyedwa naye limodzi” kudziko lapansi. (Chivumbulutso 12:9) Popeza kuti Satana, amene amatchedwanso kuti Belezebule, ndi “wolamulira ziwanda,” n’zoonekeratu kuti ziwandazo zapanga gulu lake losaoneka.—Maliko 3:22; Aefeso 6:12.
10. Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti anthu enanso ali mbali ya mbewu ya Satana?
10 Komanso pa nthawi ina, Yesu anauza atsogoleri achipembedzo achiyuda kuti: “Inu ndinu ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo mukufuna kuchita zokhumba za atate wanu.” (Yohane 8:44) Potsutsa Yesu, Mwana wa Mulungu, atsogoleri achipembedzo amenewa anasonyeza kuti nawonso ndi ana a Satana. Iwo anali mbali ya mbewu ya Satana ndipo ankatumikira atate wawo wophiphiritsayu. Kwa zaka zambiri anthu enanso ochuluka asonyeza kuti ndi ana a Satana. Achita zimenezi mwa kuchita zofuna za Satanayo, makamaka potsutsa ndi kuzunza ophunzira a Yesu. Tinganene kuti anthu onsewa ndi amene apanga gulu looneka la Satana padziko lapansi.—Onani Yohane 15:20; 16:33; 17:15.
Kodi Mbewu ya Mkazi Ikuimira Ndani?
11. Kwa zaka zambiri, kodi Mulungu wakhala akuulula chiyani chokhudza mbewu ya mkazi?
11 Pomalizira, ulosi wa pa Genesis 3:15 ukutchula mbewu ya mkazi. Pamene Satana ankasonkhanitsa mbewu yake, Yehova anali akukonzekeretsa “mkazi” wake, yemwe ndi gulu la kumwamba, kuti atulutse mbewu. Kwa zaka 4,000, Yehova wakhala akuulula pang’onopang’ono mfundo zokhudza kubwera kwa mbewuyi. Iye wakhala akuulula zimenezi kwa anthu amene amamumvera ndiponso kumuopa. (Yesaya 46:9, 10) Motero Abulahamu, Isaki, Yakobo ndi ena ambiri anali ndi chikhulupiriro choti mbewu yolonjezedwayo idzadzera m’fuko lawo. (Genesis 22:15-18; 26:4; 28:14) Ndipo Satana ndi gulu lake nthawi zambiri ankazunza atumiki a Yehova ngati amenewa chifukwa cha chikhulupiriro chawo cholimba.—Aheberi 11:1, 2, 32-38.
12. (a) Kodi mbali yaikulu kwambiri ya mbewu ya mkazi inaonekera liti ndipo panachitika zotani? (b) Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anadzozedwa?
12 Patapita nthawi, m’chaka cha 29 C.E., Yesu yemwe anali munthu wangwiro, anapita kumtsinje wa Yorodano kukabatizidwa. Yehova atamudzoza Yesu ndi mzimu woyera, anavomereza kuti iye ndi Mwana wake ponena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.” (Mateyu 3:17) Pamenepa Mulungu anasonyeza kuti Yesu anatumizidwa kuchokera ku mbali yakumwamba ya gulu lake, yopangidwa ndi zolengedwa zauzimu. Yesu anadzozedwa kuti adzakhale Mfumu ya Ufumu wakumwamba umene udzabwezeretse ulamuliro wa Mulungu padziko lapansi. Iye adzachita zimenezi m’dzina la Yehova ndipo adzathetseratu nkhani yokhudza boma, kapena kuti amene ali woyenera kulamulira. (Chivumbulutso 11:15) Choncho Yesu, yemwe ndi Mesiya wolonjezedwa, ndi amene ali mbali yaikulu kwambiri ya mbewu ya mkazi.—Yerekezerani ndi Agalatiya 3:16; Danieli 9:25.
13, 14. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa kuti mbewu ya mkazi singakhale munthu mmodzi yekha wotchuka? (b) Kodi Mulungu wasankha anthu angati kuti akhale mbali yachiwiri ya mbewu, ndipo anthu amenewa amapanga gulu liti? (c) Ndi anthu enanso ati amene akutumikira Mulungu mogwirizana ndi mbewu?
13 Kodi mbewu ya mkazi ingakhale munthu mmodzi yekha wotchuka? Kumbukirani za mbewu ya Satana ija. Baibulo limasonyeza kuti mbewu ya Satana ndi gulu la angelo oipa ndiponso anthu osalemekeza Mulungu. Choncho sitiyenera kudabwa kuti Mulungu ali ndi cholinga chosankha anthu 144,000 amene amamutumikira ndi mtima wosagawanika. Ali ndi cholinga chosankha anthu amenewa kuchokera padziko lapansi kuti akakhale ansembe komanso olamulira pamodzi ndi Yesu Khristu, yemwe ndi Mbewu komanso Mesiya. Buku la Chivumbulutso limanena za anthu amenewa pamene limati Mdyerekezi, chifukwa cha udani umene ali nawo pa gulu la Mulungu limene lili ngati mkazi, ‘anapita kukachita nkhondo ndi otsala a mbewu yake.’—Chivumbulutso 12:17; 14:1-4.
14 M’Baibulo, Akhristu odzozedwa amatchedwa abale a Yesu. Choncho, monga abale ake, Atate awo komanso amayi awo ndi amodzi ndi Atate komanso amayi a Yesu. (Aheberi 2:11) Atate awo ndi Yehova Mulungu. Chotero, amayi awo ayenera kukhala “mkazi,” amene akuimira mbali yakumwamba ya gulu la Mulungu, limene lili ngati mkazi wokwatiwa. Akhristu odzozedwawo ndiwo mbali yachiwiri ya mbewu, ndipo Khristu Yesu ndiye mbali yoyamba. Mpingo wa Akhristu obadwa ndi mzimu amenewa, omwe ali padziko lapansi, ndiwo mbali yooneka ya gulu la Mulungu limene limam’tumikira motsogoleredwa ndi mbali yakumwamba ya gulu la Mulungu, lomwe lili ngati mkazi. Akhristu amenewa akadzaukitsidwa, adzakhala m’gulu lakumwamba limeneli pamodzi ndi Khristu Yesu. (Aroma 8:14-17; Agalatiya 3:16, 29) Ngakhale kuti anthu ambirimbiri a nkhosa zina ochokera m’mitundu yonse sali mbali ya mbewu imeneyi, akugwirizana ndi mbali yapadziko lapansi ya gulu la Mulungu pomutumikira. Kodi inuyo muli m’gulu la nkhosa zina limeneli? Ngati muli m’gulu limeneli ndiye kuti muli ndi chiyembekezo chodzalandira moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi.—Yohane 10:16; 17:1-3.
Mmene Chidani Chinayambira
15. (a) Fotokozani zimene zinachitika kuti anthu ena ndiponso angelo akhale mbewu ya Satana. (b) Kodi n’chiyani chimene chinachitikira mbewu ya Satana pa Chigumula cha m’nthawi ya Nowa?
15 Anthu amene ndi mbewu ya Satana anayamba kuonekera kale kwambiri anthu atangolengedwa kumene. Mwachitsanzo, panali Kaini, munthu woyamba kubadwa, “amene anachokera kwa woipayo n’kupha m’bale wake” Abele. (1 Yohane 3:12) Kenako Inoki ananena kuti Yehova adzabwera “ndi miyandamiyanda ya oyera ake, kudzapereka chiweruzo kwa onse, ndi kudzagamula kuti onse osaopa Mulungu apezeka ndi mlandu chifukwa cha ntchito zawo zonyoza Mulungu zimene anazichita mosaopa Mulungu, komanso chifukwa cha zinthu zonse zonyoza koopsa zimene ochimwa osaopa Mulungu anamunenera.” (Yuda 14, 15) Komanso angelo amene anagalukira Mulungu aja anagwirizana ndi Satana ndipo anakhala mbali ya mbewu yake. Angelo amenewa “anasiya malo awo” kumwamba kuti avale matupi a anthu ndipo anakwatira ana aakazi a anthu. Iwo anabereka ana ankhanza omwe anali ziphona. Pa nthawi imeneyo dziko linadzaza ndi chiwawa ndi zoipa, ndipo Mulungu analiwononga ndi Chigumula. Koma Nowa ndi banja lake, amene anali okhulupirika, ndi anthu okhawo amene anapulumuka. Angelo osamvera aja, amene tsopano ndi ziwanda zimene zikulamuliridwa ndi Satana, anakakamizika kusiya akazi ndi ana awo akuwonongedwa. Angelo amenewo anavula matupi awo aja ndi kubwerera kumalo amizimu. Kumeneko akuyembekezera chiweruzo chimene Mulungu watsala pang’ono kupereka kwa Satana ndi mbewu yake.—Yuda 6; Genesis 6:4-12; 7:21-23; 2 Petulo 2:4, 5.
16. (a) Kodi ndi wolamulira wankhanza uti amene anayamba kulamulira pambuyo pa Chigumula, ndipo anasonyeza bwanji kuti iye anali mbali ya mbewu ya Satana? (b) Kodi Mulungu anasokoneza bwanji anthu amene ankafuna kumanga nsanja ya Babulo?
16 Patapita nthawi yochepa Chigumula chitachitika, munthu wina wankhanza wotchedwa Nimurodi anayamba kulamulira anthu ena padziko lapansi. Baibulo limati iye anali “mlenje wamphamvu wotsutsana ndi Yehova,” zomwe zikusonyeza kuti analidi mbali ya mbewu ya Njoka. Mofanana ndi Satana, Nimurodi anasonyeza mtima wopanduka pomanga mzinda wa Babele, kapena kuti Babulo. Zimenezi zinali zosemphana ndi cholinga cha Yehova chakuti anthu adzaze dziko lonse lapansi. Nimurodi anakonza zoti amange nsanja yaikulu imene ‘ikanafika m’mwamba mwenimweni,’ n’cholinga choti mzinda wa Babulo utchuke. Koma Mulungu anasokoneza anthu amene ankafuna kumanga nsanjayo. Iye anasokoneza chinenero chawo ndipo “anawabalalitsa pamalopo, kuti afalikire padziko lonse lapansi.” Koma mzinda wa Babulowo sanauwononge.—Genesis 9:1; 10:8-12; 11:1-9.
Kuyambika kwa Ulamuliro Wandale
17. Pamene anthu ankachulukirachulukira, kodi anayamba kuchita chinthu chiti cholakwika, ndipo zimenezi zinachititsa kuti pakhale maulamuliro akuluakulu ati?
17 Anthu a ku Babulo anayamba kuchita zinthu zotsutsana ndi ulamuliro wa Yehova. Chimodzi mwa zinthu zimenezo chinali ulamuliro wandale. Anthu atayamba kuchuluka, anthu ena ofuna kutchuka anatengera chitsanzo cha Nimurodi n’kuyamba kulamulira anzawo. Munthu anayamba kupweteka munthu mnzake pomulamulira. (Mlaliki 8:9) Mwachitsanzo, m’nthawi ya Abulahamu, mizinda ya Sodomu, Gomora ndi ina yapafupi inkalamuliridwa ndi mafumu a ku Sinara ndiponso a m’madera ena akutali. (Genesis 14:1-4) Kenako akatswiri ankhondo komanso odziwa kuyendetsa zinthu anayamba kulamulira madera akuluakulu kuti apeze chuma chochuluka ndiponso ulemerero. Ena mwa maulamuliro amenewa, omwe Baibulo limatchula, anali Iguputo, Asuri, Babulo, Mediya ndi Perisiya, Girisi ndiponso Roma.
18. (a) Kodi atumiki a Mulungu amawaona bwanji olamulira andale? (b) Kodi nthawi zina olamulira andale athandiza bwanji kuti zolinga za Mulungu zichitike? (c) Kodi olamulira ambiri asonyeza bwanji kuti iwo ndi mbali ya mbewu ya Njoka?
18 Yehova analola kuti maulamuliro andale amenewo akhalepo, ndipo atumiki a Mulungu amene ankakhala m’madera olamulidwa ndi andale amenewa ankayesetsa kuwamvera pa zinthu zimene sizinkatsutsana ndi malamulo a Mulungu. (Aroma 13:1, 2) Nthawi zina olamulira andale ankachita zinthu zothandiza kuti zolinga za Mulungu zichitike, kapena ankateteza anthu a Yehova. (Ezara 1:1-4; 7:12-26; Machitidwe 25:11, 12; Chivumbulutso 12:15, 16) Komabe, olamulira ambiri akhala akutsutsa kwambiri kulambira koona, ndipo asonyeza kuti iwo ndi mbali ya mbewu ya Njoka.—1 Yohane 5:19.
19. Kodi buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti n’chiyani chimene chikuimira mafumu amphamvu kwambiri padziko lonse?
19 Ngakhale zili choncho, kumbali yaikulu ulamuliro wa anthu walephera kutithandiza kuti tikhale ndi moyo wosangalala kapena kuchotsa mavuto athu. Yehova walola anthu kuti ayese mitundu yosiyanasiyana ya maboma, koma iye sagwirizana ndi chinyengo ndiponso nkhanza zimene maboma amachitira anthu. (Miyambo 22:22, 23) Buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti chilombo chodzikweza ndiponso choopsa chikuimira mafumu amphamvu kwambiri padziko lonse, omwe ndi ankhanza.—Chivumbulutso 13:1, 2.
Amalonda Achinyengo Komanso Odzikonda
20, 21. Kodi ndi gulu lachiwiri liti lomwe likupanga mbali ya mbewu yoipa ya Satana pamodzi ndi “akuluakulu a asilikali” komanso “amuna amphamvu,” ndipo n’chifukwa chiyani tikutero?
20 Kuwonjezera pa atsogoleri andale, palinso anthu ochita malonda, omwe ndi achinyengo, ndipo amagwirizana ndi anthu andalewo. Zolembalemba zimene anazifukula m’mabwinja a mzinda wa Babulo zimasonyeza kuti amalonda ambiri ankadyera masuku pamutu anthu ovutika. Masiku ano, ochita malonda padzikoli akupitirizabe kuchita zinthu zodzikonda kuti apeze phindu lochuluka. Ndipo m’mayiko ochuluka, anthu ochepa ndi olemera kwambiri pamene anthu ochuluka akuvutika chifukwa cha umphawi. Masiku ano pamene ntchito zamafakitale zapita patsogolo kwambiri, anthu amalonda ndiponso makampani akugulitsa kwa magulu andale zida zankhondo zoopsa zedi, kuphatikizapo zida zoti zikhoza kupha anthu ambiri nthawi imodzi, ndipo akupeza phindu lalikulu chifukwa cha malonda amenewa. Zida zimenezi tsopano zikudetsa anthu nkhawa kwambiri padziko lonse lapansi. Anthu achinyengo ochita malonda a zida zoopsazi ndiponso anthu ena adyera amalonda ali m’gulu la mbewu yoipa ya Satana, pamodzi ndi “akuluakulu a asilikali” komanso “amuna amphamvu.” Onsewa ndi mbali ya gulu la padziko lapansi limene Mulungu ndi Khristu akuliona kuti ndi loyenera kuwonongedwa.—Chivumbulutso 19:18.
21 Kuwonjezera pa andale achinyengo ndi anthu adyera amalonda, palinso gulu lina lachitatu limene Mulungu akuliona kuti ndi loyenera kuwonongedwa. Kodi gulu limeneli ndi liti? Mukhoza kudabwa kwambiri mutadziwa zimene buku la Chivumbulutso limanena za gulu lapadziko lonse lodziwika bwino limeneli.
Babulo Wamkulu
22. Kodi mumzinda wakale wa Babulo munayambika chipembedzo chotani?
22 Ntchito yomanga mzinda wa Babulo, sinangosonyeza chabe mphamvu za wolamulira wa mzindawo. Panalinso nkhani yokhudza kulambira, popeza anamanga mzindawo motsutsana ndi ulamuliro wa Yehova. Choncho kulambira mafano kunayambira mumzinda wakale wa Babulo. Ansembe awo ankaphunzitsa zinthu zosalemekeza Mulungu, monga zoti munthu akafa mzimu wake umapitiriza kukhala ndi moyo. Komanso iwo ankaphunzitsa zoti munthu akamwalira amapita kumalo oopsa a ziwanda kumene amakazunzidwa kwamuyaya. Ansembewo anayambitsa kulambira zinthu zolengedwa ndiponso kulambira milungu yambiri yaimuna ndi yaikazi. Anapeka nkhani zabodza zofotokoza chiyambi cha dzikoli ndi anthu, ndipo ankachita miyambo yoipa ndi kupereka nsembe kwa milungu yonyenga. Iwo ankachita zimenezi poganiza kuti zingathandize anthu kuti akhale obereka, kuti akolole mbewu zambiri ndiponso kuti apambane pa nkhondo.
23. (a) Pamene anthu anamwazikana kuchoka ku Babulo, kodi anapitiriza kuchita chiyani, ndipo zotsatira zake zinali zotani? (b) Kodi buku la Chivumbulutso limati zipembedzo zonyenga zonse pamodzi zili ngati chiyani? (c) Kodi chipembedzo chonyenga chimalimbana ndi ndani nthawi zonse?
23 Pamene anthu olankhula zinenero zosiyanasiyana anamwazikana padziko lonse lapansi kuchoka ku Babulo, anapitiriza chipembedzo cha ku Babulo chija. Choncho, miyambo ndi zikhulupiriro zofanana ndi za ku Babulo wakale zinafalikira kwa anthu a ku Ulaya, Africa, North ndi South America, mayiko a kum’mawa kwa Asia ndiponso mayiko a ku South Pacific. Ndipo zambiri mwa zikhulupiriro zimenezi zidakalipobe mpaka pano. M’pake kuti buku la Chivumbulutso limati zipembedzo zonyenga zonse pamodzi, zili ngati mzinda wotchedwa Babulo Wamkulu. (Chivumbulutso chaputala 17 ndi 18) Kulikonse kumene zipembedzo zonyengazi zili, zimakhala ndi ansembe opondereza ndipo anthu ake amakhulupirira mizimu, amakhala mbuli mwauzimu ndiponso amakonda chiwerewere. Chipembedzo chonyenga ndi chida champhamvu chimene Satana akugwiritsira ntchito. Nthawi zonse Babulo Wamkulu amalimbana kwambiri ndi olambira oona a Yehova, yemwe ndi Ambuye Wamkulu Koposa.
24. (a) Kodi Njoka inavulaza bwanji “chidendene” cha Mbewu ya mkazi? (b) N’chifukwa chiyani kuzunzidwa ndi kuphedwa kwakeko kuli ngati chilonda cha pachidendene basi?
24 Alembi ndi Afarisi a m’nthawi ya Yesu, amene anali atsogoleri a chipembedzo cha Chiyuda, ndi amene ali mbali yoipa kwambiri ya mbewu ya Njoka, chifukwa ndi amene anatsogolera pozunza ndi kupha mbali yoyamba ya mbewu ya mkazi. Pamenepa Njoka ‘inavulaza chidendene’ cha “mbewu.” (Genesis 3:15; Yohane 8:39-44; Machitidwe 3:12, 15) N’chifukwa chiyani kuzunzidwa ndi kuphedwa kwa mbali yoyamba ya mbewu ya mkazi kuli ngati chilonda cha pachidendene basi? N’chifukwa chakuti kuvulazidwa kumeneku kunali kwa nthawi yochepa padziko lapansi pano. Sikunali kokhalitsa chifukwa Yehova anaukitsa Yesu pa tsiku lachitatu ndi kumukweza kuti akhale ndi moyo wauzimu.—Machitidwe 2:32, 33; 1 Petulo 3:18.
25. (a) Kodi Yesu, amene tsopano anapatsidwa ulemerero waukulu, wapereka kale chilango chotani kwa Satana ndi angelo ake? (b) Kodi mbewu yapadziko lapansi ya Satana idzachotsedwa liti? (c) Kodi chidzachitike n’chiyani Mbewu ya mkazi wa Mulungu ‘ikadzaphwanya mutu’ wa Satana, amene ndi njoka?
25 Yesu Khristu amene tsopano anapatsidwa ulemerero waukulu, akutumikira kudzanja lamanja la Mulungu, kuweruza adani a Yehova. Wapereka kale chilango kwa Satana ndi angelo ake powachotsa kumwamba n’kuwaponya padziko lapansili. Zimenezi zachititsa kuti mavuto achuluke kwambiri masiku ano. (Chivumbulutso 12:9, 12) Koma ulosi wakuti mbewu ya padziko lapansi ya Satana idzachotsedwa, udzakwaniritsidwa Mulungu akadzaweruza Babulo Wamkulu ndi mbali zina zonse za gulu la Satana padziko lapansi. Kenako Mbewu ya mkazi wa Mulungu, Yesu Khristu, “idzaphwanya mutu” wa Satana, amene ndi njoka yokalamba ndi yachinyengo. Zimenezi zikutanthauza kuti Satana adzawonongedweratu ndipo sadzalowereranso pa zochita za anthu.—Aroma 16:20.
26. N’chifukwa chiyani kuphunzira ulosi wa m’buku la Chivumbulutso n’kofunika kwambiri?
26 Kodi zonsezi zidzachitika bwanji? Buku la m’Baibulo la Chivumbulutso likutiululira mmene zimenezi zidzachitikire. Likutiululira zimenezi m’masomphenya osiyanasiyana, amene ali ndi zizindikiro zochititsa chidwi. Choncho tiyeni tiphunzire ulosi wamphamvu umenewu mwachidwi. Tingakhale odala ngati tikumva komanso kutsatira mawu a m’buku la Chivumbulutso. Tikamachita zimenezi tidzathandizira kulemekeza dzina la Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndipo iye adzatipatsa madalitso osatha. Tikukupemphani kuti mupitirize kuwerenga ndi kugwiritsa ntchito zimene mukuwerengazo. Zimenezi zikuthandizani kuti mudzapulumuke chiwonongeko cha nthawi yamapeto ino.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 13]
Nkhani za malonda zolembedwa m’chinenero chakale
Buku lina limene linakonzedwanso ndi James B. Pritchard, limatchula malamulo pafupifupi 300 amene analembedwa ndi Hammurabi, pamene ankalamulira Babulo. Malamulo amenewa akusonyeza kuti ku Babulo pa nthawiyo anthu ambiri ankachita chinyengo kwambiri pa nkhani zamalonda, moti panafunikadi kukhazikitsa malamulo ambirimbiri oletsa chinyengocho. Mwachitsanzo, taonani lamulo limodzi ili: “Ngati munthu wolemekezeka wagula kwa mwana wake kapena kapolo wake siliva, golide, kapolo wamwamuna kapena wamkazi, ng’ombe, nkhosa, bulu kapena chinthu china chilichonse, komanso ngati wapatsidwa zinthu zimenezi kuti asunge popanda mboni kapena kusainirana makalata, munthu wolemekezekayo aphedwe chifukwa ndi wakuba.”—Ancient Near Eastern Texts.