Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 5/1 tsamba 23-28
  • Sonyezani Chikhulupiriro Kaamba ka Moyo Wosatha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sonyezani Chikhulupiriro Kaamba ka Moyo Wosatha
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiyembekezo cha Moyo Wosatha
  • Chiukiriro​—Kupita Kuti?
  • Kusakhoza Kufa
  • “Sadzamwalira Nthawi Yonse”
  • Kodi Chikhulupiriro Chanu cha Chiukiriro Ncholimba Motani?
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Moyo Pambuyo pa Imfa—Motani, Kuti, Liti?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Moyo wa Pambuyo pa Imfa—Kodi Baibulo Limanenapo Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Akufa Adzaukitsidwa
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 5/1 tsamba 23-28

Sonyezani Chikhulupiriro Kaamba ka Moyo Wosatha

‘Khalani nacho chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.’​—AHEBRI 10:39.

1. Kodi bukhu lanazonse Lachikatolika likuvomereza chiyani ponena za kugwiritsira ntchito kwa Baibulo kwa liwu lakuti “moyo”?

PALIBE paliponse pamene Baibulo limanena kuti anthu ali ndi moyo wosakhoza kufa umene umapulumuka thupi pa imfa ndikuti umakhalabe ndimoyo m’dziko lamizimu. Ngakhale New Catholic Encyclopedia ikuvomereza kuti: “Lingaliro la kupulumuka kwa moyo pambuyo pa imfa silikumveka bwino m’Baibulo. . . . Moyo mu Chi[pangano] Cha[kale] sumatanthauza mbali ya munthu, koma munthu yense​—munthu monga chinthu chamoyo. Mofananamo, mu Chi[pangano] Cha[tsopano] umatanthauza moyo wa munthu: moyo wa munthu payekha.” Chotero anthu alibe miyoyo, iwo ndiwo miyoyo.

2. (a) Kodi chikhulupiriro cha moyo wosakhoza kufa chinachokera kuti? (b) Kodi chowonadi nchiyani ponena za mkhalidwe wa munthu pambuyo pa imfa?

2 Monga mmene nkhani yapitayi yasonyezera, chikhulupiriro cha moyo wosakhoza kufa chiri lingaliro lachikunja limene lingalondoledwe mpaka ku nthaŵi zakale. Mkonzi wake ali iye amene anatsutsa chilengezo chomveka cha Mulungu chakuti munthu ‘adzafa ndithu’ chifukwa cha kusamvera. (Genesis 2:17) Adali wotsutsayo, Satana Mdyerekezi, amene anati: “Kufa simudzafai.” (Genesis 3:4) Ndipo limenelo linali bodza. (Yohane 8:44) Pambuyo pake, Satana anachilikiza chiphunzitso cha moyo wa munthu wosakhoza kufa. Koma chowonadi chonena za mkhalidwe wa munthu pambuyo pa imfa chiri chimene chalembedwa m’Mawu ouziridwa a Mulungu pa Mlaliki 9:5: “Akufa sadziwa kanthu bi.”​—Onaninso Aroma 5:12.

Chiyembekezo cha Moyo Wosatha

3. Kodi Baibulo liri ndi zonena zambiri ponena za chiyembekezo chotani?

3 Pamene kuli kwakuti Baibulo limasonyeza bwino lomwe kuti kulibeko moyo wosakhoza kufa, limanena zambiri ponena za moyo wosatha. Chiyembekezo cha moyo wopanda malire chinali chiphunzitso chachikulu cha Yesu. Iye anati: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Ponena za awo amene amasonyeza chikhulupiriro mwa Mulungu ndi Kristu, Yesu anati: “Ine ndizipatsa moyo wosatha.” (Yohane 10:28) Ndi chidaliro chotheratu, anati: “Iye wokhulupira ali nawo moyo wosatha. . . . Adzakhala ndi moyo kosatha.” (Yohane 6:47, 51) Ndipo analengezanso kuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.”​—Yohane 3:16.

4. Kodi Yesu ananenanji ponena za chiyembekezo chamtsogolo?

4 Popeza kuti kulibe moyo wosakhoza kufa umene umapulumuka imfa ya thupi, kodi lonjezo la Baibulo la moyo wosatha lidzakwaniritsidwa motani? Yesu anapereka chidziŵitso chowonjezereka pamene anachezera Marita ndi Mariya pambuyo pa kufa kwa mlongo wawo Lazaro. Iye anati kwa Marita: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo.” Anamfunsa Marita kuti: “Kodi ukhulupirira ichi?” Iye anayankha kuti: “Inde Ambuye; ndakhulupirira ine kuti Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu.”​—Yohane 11:25-27.

5, 6. Kodi kuukitsa Lazaro kwa Yesu kubwereranso ku moyo kunasonyeza chiyani?

5 Kuti asonyeze kuti iye, monga Mwana wa Mulungu, anapatsidwa mphamvu za kuukitsa akufa, Yesu anapita ku manda a Lazaro. Lazaro anali wakufa kwa masiku anayi, ndipo thupi lake linayamba kuola. Mosasamala kanthu za izo, “[Yesu] anafuula ndi mawu aakulu, Lazaro, tuluka. Ndipo womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nawo, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.” (Yohane 11:43, 44) Lazaro womwalirayo anaukitsidwa!

6 Lazaro sanaukitsidwe kuchokera kumwamba kapena kwina kulikonse m’dziko lamizimu. Iye sanapite ku dziko lamizimu pamene anamwalira koma anali wosadziŵa kanthu m’manda, kumene akufa onse ali. (Salmo 146:4; Yohane 3:13; Machitidwe 2:34) Sizingakhale zatanthauzo kuganiza kuti moyo wosakhoza kufa wa Lazaro unali kusangalala ndi chikondwerero chakumwamba ndipo kenaka moyowo unatsompholedwa kumwamba kuti udzagwirizane ndi thupi lake lopanda ungwiro pa dziko lapansi kuti akhalenso ndi moyo m’dziko lodzazidwa ndi kuvutika, matenda, ndi imfa. Koma popeza kuti sanali kumwamba, kubwezeretsedwa kwake ku moyo kunalandiridwa, popeza kunatanthauza kuwonjezera zaka za kukhalapo kwa iye ndi kugwirizananso ndi okondedwa ake. Pambuyo pake, akamwaliranso.

7, 8. (a) Kodi ndi pazochitika zina ziti pamene Yesu anaukitsa akufa? (b) Kodi nchifukwa ninji Yesu anapanga zozizwitsa zimenezo zobwezeretsa anthu ku moyo?

7 Pamene Yesu anaukitsa msungwana wachichepere amene anali wakufa, makolo ake “anadabwa pomwepo ndi kudabwa kwakukulu.” (Marko 5:42) Komabe, msungwana ameneyo m’kupita kwa nthaŵi anamwaliranso. Pamene Yesu anaukitsa mwana wa mkazi wamasiye wa ku Nayini, “mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu.” (Luka 7:16) Koma mwamuna ameneyo m’kupita kwa nthaŵi anamwaliranso. Ponena za zozizwitsa zimenezi, The New International Dictionary of New Testament Theology ikutsimikiza kuti: “Awo amene anaukitsidwa ndi Kristu mu uminisitala wake wa padziko lapansi anayenera kufa, popeza kuti kuukitsidwa kumeneku sikunatanthauze kusakhoza kufa.”

8 Kodi nchifukwa ninji Yesu anaukitsa ameneŵa kwa akufa? Osati kupereka moyo wosatha pa nthaŵiyo, koma kusonyeza kuti anali Mesiya ndi kusonyeza zimene Mulungu anampatsa mphamvu yozichita. Zinamangirira chikhulupiriro m’chiukiriro ndi moyo wamuyaya pansi pa ulamuliro wakutsogolo wa Ufumu wakumwamba wa Mulungu m’manja mwa Kristu.​—Mateyu 6:9, 10; Yohane 11:41, 42.

9. Kodi ndimotani mmene Marita ndi Paulo molondola anamvetsetsera chiphunzitso cha Yesu cha chiyembekezo cha chiukiriro?

9 Marita anadziŵa za chiyembekezo chimenecho mwa kuyanjana kwake ndi Yesu, popeza kalelo anali atanena naye za Lazaro kuti: “Ndidziŵa kuti adzauka m’kuuka tsiku lomaliza.” (Yohane 11:24) Anadziŵa kuti chiukiriro chidzakhalako, osati pa tsiku lake (la Lazaro) lomaliza, koma mtsogolo, “pa tsiku lomaliza”​—Tsiku Loweruza, pamene akufa onse adzaukitsidwa pansi pa ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu. Mtumwi Paulo anadziwanso zimenezi, popeza ananena kuti: “[Mulungu] anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo.” (Machitidwe 17:31) Paulo ananenanso kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Iye sananene kuti chiukirirocho chinali kuchitika koma “kudzakhala” mtsogolo​—pansi pa ulamuliro wa Ufumu.

10. Kodi ndi ndemanga yotani imene profesala Wachifrenchi akupanga ponena za zikhulupiriro za Dziko Lachikristu za chiukiriro poyerekezera ndi chiphunzitso chomveka cha Baibulo?

10 M’bukhu lakuti Immortality of the Soul or Resurrection of the Dead? profesala Wachiprotesitanti Wachifrenchi Oscar Cullmann akulemba kuti: “Pali kusiyana kwakukulu pakati pa chiyembekezo Chachikristu cha kuuka kwa akufa ndi chikhulupiriro Chachigiriki cha moyo wosakhoza kufa. . . . Ngakhale kuti Chikristu pambuyo pake chinakhazikitsa chogwirizanitsa pakati pa ziphunzitso ziŵirizi, ndipo lerolino Mkristu wamba amasokoneza ziŵirizo kotheratu, sindikuwona chifukwa chobisira zimene ine ndi akatswiri ambiri timalingalira kukhala chowonadi. . . . Moyo (life) ndi lingaliro la Chipangano Chatsopano zimalamuliridwa kotheratu ndi chikhulupiriro cha chiukiriro. . . . Munthu yense, amene alidi wakufa, amabwezedwa ku moyo ndi kachitidwe kolenga katsopano ka Mulungu.”

Chiukiriro​—Kupita Kuti?

11, 12. (a) Kodi nchiyani chimene chiri chifuno cha Mulungu kaamba ka anthu ndi dziko lapansi? (b) Kodi Yesu anasonyeza motani kuti chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi sichinasinthe?

11 Pamene Mulungu analenga anthu, anawapatsa dziko lapansi monga mudzi wawo wosatha ndi cholinga chakuti alidzaze pulaneti ndi fuko la anthu olungama. (Genesis 1:26-28; Salmo 115:16) Baibulo limalankhula za Yehova monga “amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe.”​—Yesaya 45:18.

12 Mosasamala kanthu za zaka zikwizikwi za kupanda ungwiro ndi imfa chiyambire pamene munthu anapanduka, chifuno cha Mulungu chidakali chakuti dziko lapansi likhale mudzi wosatha wa munthu: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:5) Chotero, pamene Yesu anaukitsa akufa, iye anawaukitsa pompano pa dziko lapansi, ndipo anadziŵidwa nthaŵi yomweyo ndi ena monga anthu amene adamwalira. Zimenezi zinatsimikizira kuti pansi pa ulamuliro wa Ufumu akufa adzabwezeretsedwa ku moyo pano pa dziko lapansi kudzakhala ndi mwaŵi wa kukhala ndi moyo kosatha pa ilo. (Chibvumbulutso 20:12, 13) Zimenezo zidzakwaniritsa chifuno cha Mulungu kaamba ka anthu ndi dziko lapansi.​—Yesaya 46:9-11; 55:11; Tito 1:1, 2.

13. Kodi ndi vuto lotani limene limayang’anizana ndi matchalitchi a Dziko Lachikristu, ndipo kodi ndimotani mmene akuyesera kulithetsa?

13 Komabe, popeza kuti matchalitchi a Dziko Lachikristu amakhulupirira kusakhoza kufa kwa moyo, zimenezi zimawapatsa vuto: Kodi angagwirizanitse motani kuukitsidwa kwa “munthu wathunthu,” monga mmene zinasonyezedwera ndi Yesu, ndi chikhulupiriro chawo cha moyo wosakhoza kufa umene uli kale kumwamba kapena m’helo? The Catholic Encyclopedia ikutsutsa kuti: “Lateran Bungwe Lachinayi la limaphunzitsa kuti anthu onse, kaya owongoka kapena ochimwa, ‘adzaukanso ndi matupi awo amene ali nawo pa nthaŵi ino.’” Ikuwonjezera kuti: “Popeza kuti thupi ndilo bwenzi la maupandu a moyo, ndipo mnzake wa zotulukapo zake, chilungamo cha Mulungu chikuwoneka kukhala chimafuna kuti thupi likhale lotengako mbali ku chilango cha moyo ndi mphotho.” Mogwirizana ndi chikhulupiriro chimenechi, thupi lidzagwirizanitsidwa ndi moyo kumwamba kapena m’helo. Kodi kwautali wotani? “Matupi oukitsidwa a oyera mtima ndi ochimwa adzavekedwa kusakhoza kufa,” magwero amenewo akutero.

14. Kodi ndimotani mmene mlembi Wachijesuit akuyesera kumveketsa lingaliro la Dziko Lachikristu la chiukiriro cha thupi?

14 M’bukhu lakuti The Future Life, lolembedwa ndi Jesuit J. C. Sasia, tikuŵerenga kuti: “Chotero moyo (life) wakumwamba udzakhala wosangalatsanso kupyolera m’malingaliro olemekezedwa [a thupi logwirizanitsidwa ndi moyo (soul)].” Ponena za matupi ogwirizanitsidwa ndi miyoyo yawo m’helo, magwero amenewo akunena kuti: “M’helo, pambuyo pa chiukiriro [cha thupi], nzeru iriyonse ya thupi la munthu idzakhala ndi chilango chake chapadera . . . Nzeru ya kumva kapena kukhudza idzalangidwa koposa, chifukwa chakuti kuli makamaka mwa machimo a thupi kuti ochimwa amalakwira Mulungu. . . . Kugwirizana kwawo ndi matupi awo kudzakhala chochititsa cha zizunzo zowonjezereka ndi zisoni.”

15. Kodi nchifukwa ninji uli mwano kuphunzitsa kuti Mulungu amazunza anthu m’helo kosatha?

15 Chotero, kuvomereza lingaliro lachikunja la moyo wosakhoza kufa kunatsegula njira kwa Dziko Lachikristu kuvomerezanso lingaliro lachikunja la chizunzo chowawa cha miyoyo​—ndipo ngakhale matupi​—m’helo kosatha. Komabe, ponena za machitidwe akale otentha ana monga nsembe kwa milungu yonama, Yehova analongosola kuti: “Apsereze ana awo mmenemo nsembe zopsereza za Baala, chimene sindinawauza, sindinachinena, sichinalowa m’mtima mwanga.” (Yeremiya 19:5) Chotero ndimwano kuphunzitsa kuti Mulungu amazunza anthu kosatha, pamene Mawu ake amasonyeza mowonekera kuti ochimwa osalapa adzawonongedwa, kuchotsedwapo. “Wamoyo aliyense samvera mneneri [Yesu] ameneyu, adzasakazidwa konse.”​—Machitidwe 3:23; onaninso Mateyu 10:28; Luka 17:27; Yohane 3:16; 2 Petro 2:12; Yuda 5.

Kusakhoza Kufa

16. Kodi Baibulo limaphunzitsanji ponena za kusakhoza kufa?

16 Komabe, kodi Baibulo siliphunzitsa kuti anthu adzapita kumwamba kukakhala ndi miyoyo yosakhoza kufa kumeneko? Inde, limatero. Koma palibe kugwirizana kulikonse ndi miyoyo yosakhoza kufa ya anthu. Kusakhoza kufa kumatulukapo chifukwa cha kuukitsidwa kwa munthu monga cholengedwa chauzimu (monga mmene analiri Yesu) ndipo osati chifukwa cha kukhala kwake ndi moyo wosakhoza kufa umene umapulumuka imfa. Mphotho yamtsogolo ya kusakhoza kufa inaperekedwa kwa anthu okhulupirika, onga Kristu ndipo inayenera kukhalako kokha pambuyo pa kuyamba kulamulira kwa Kristu mu Ufumu kumwamba, osati mwamsanga pambuyo pa kukwera kumwamba kwa Kristu m’zaka za zana loyamba.​—Salmo 110:1; 1 Akorinto 15:53, 54.

17. Kodi ndangati amene adzakhala ndi moyo wosakhoza kufa, ndipo kodi ndi mbali yotani imene amachita m’chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi?

17 Kuwonjezerapo, chiyembekezo chimenecho chinaperekedwa kwa oŵerengeka a banja la anthu. Yesu anawatcha “kagulu ka nkhosa.” (Luka 12:32) Gulu limeneli, lokwanira 144,000 m’chiŵerengero, limaukitsidwira kumoyo wakumwamba monga zolengedwa zauzimu zosakhoza kufa kulamulira pa dziko lapansi ndi Kristu mu Ufumu wake wakumwamba. (2 Petro 3:13; Chibvumbulutso 7:4; 14:1, 4; 20:4) M’kupita kwa nthaŵi, dziko lapansi limene amalilamulira lidzadzazidwa ndi anthu angwiro, mosakaikira zikwi mamiliyoni a iwo. Ambiri a anthu amenewo adzakhala amene abwerera ku dziko lapansi mwa “kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Komabe, padzakhala ena amene adzapeza moyo m’dziko latsopano pambali pa awo amene adzaukitsidwa kwa akufa. Kodi ena ameneŵa ndayani?

“Sadzamwalira Nthawi Yonse”

18. Kuwonjezera pa chiyembekezo cha chiukiriro kwa anthu akufa, kodi ndi chinthu chosangalatsa chotani chimene Yesu ananeneratu?

18 Pamene kuli kwakuti chiyembekezo chotsimikizirika kaamba ka anthu akufa ndicho chiukiriro, pali chiyembekezo china chozizwitsa m’nthaŵi yathu. Icho chikukhudza chimene Yesu anamuuza Marita. Pambuyo ponena kuti: “Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo [m’chiukiriro],” Yesu anawonjezera kuti, “ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthaŵi yonse.” (Yohane 11:25, 26) M’ndemanga yomalizirayi, Yesu ananeneratu chinthu chosangalatsa: Ikafika nthaŵi imene anthu amene ali ndi moyo sakafunikira kumwalira! Koma kodi zimenezo zidzachitika liti?

19. (a) Kodi chiyembekezo cha kusamwalira konse chidzakwaniritsidwa mkati mwa nyengo iti? (b) Kodi ndimotani mmene Baibulo limalongosolera awo amene ali ndi chiyembekezo cha kusamwalira konse?

19 Tsopano​—tsiku lathu​—ndiyo nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwa lonjezo limenelo! Maumboni onse akusonyeza kuti tiri pafupi kwambiri ndi mapeto a dziko loipali. (Mateyu 24:3-14; 2 Timoteo 3:1-5, 13) Chotero, anthu amene akusonyeza chikhulupiriro lerolino mwa Mulungu ndi Mwana wake ali ndi chiyembekezo chosangalatsa cha kupulumuka mapeto a dongosolo lino ndi kupitiriza kukhala ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu​—osamwalira konse! Ameneŵa akulankhulidwa pa Chibvumbulutso 7:9, 14 monga “khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uli wonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, . . . [amene] akutuluka m’chisautso chachikulu,” osungidwa ndi Mulungu chifukwa cha kusonyeza kwawo chikhulupiriro. Yesu analankhula za kudza kwa kuthetsedwa kwa dongosolo lino loipa monga “masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.”​—Mateyu 24:21; onaninso Miyambo 2:21, 22; Salmo 37:10, 11, 34.

20, 21. Kodi mamiliyoni lerolino akusonyeza motani chikhulupiriro mwa Mulungu ndi Kristu, ndipo kodi ambiri a iwo sadzafunikira chiyani?

20 Pa dziko lonse, mamiliyoni a khamu lalikulu amene akufuna kukhala kosatha pa dziko lapansi akusonyeza kale chikhulupiriro m’malonjezo a Mulungu ndi mwa amene anampatsa ulamuliro wokhala “kuuka ndi moyo,” Yesu Kristu. Ndipo adzipatulira iwo eni kwa Mulungu, kuzindikiritsa zimenezi mwa ubatizo wa m’madzi. (Mateyu 28:19, 20) Iwo amavomereza kuti chipulumutso chawo chatheka kotheratu ndi “Mulungu . . . wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa,” Yesu Kristu.​—Chibvumbulutso 7:10.

21 Awo a khamu lalikulu amene adzapulumuka mapeto a dzikoli sadzafunikira kuukitsidwa kwa akufa chifukwa iwo “sadzamwalira nthaŵi yonse”! Kodi mukuwatenga masitepe a kukhala wa m’gulu limeneli? Ngati ndi tero, ndi mwaŵi wosangalatsa, wapadera wotani nanga umene watseguka kwa inu​—uja wa kupulumuka mapeto a dongosolo loipa la Satana ndi kuloŵetsedwa m’nyengo yolungama yatsopano imene idzakubweretserani umoyo wangwiro ndi moyo wosatha pa dziko lapansi la paradaiso! (Luka 23:43; Chibvumbulutso 21:4, 5) Mwakuphunzira chimene chifuniro cha Mulungu chiri ndi kulimbikira kuchichita, mungasonyeze kuti inu ‘sindinu a iwo akubwerera kulowa chitayiko.’ Nanunso mungakhale ndi “chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.”​—Ahebri 10:39; 1 Yohane 2:15-17; Chibvumbulutso 7:15.

Mafunso Obwereramo

◻ Kodi nchiyani chimene chiri chiyembekezo chowona kaamba ka akufa?

◻ Kodi nchifukwa ninji chikhulupiriro cha Dziko Lachikristu cha kuuka kwa thupi chiri mwano kwa Mulungu?

◻ Kodi Baibulo limaphunzitsanji ponena za kusakhoza kufa?

◻ Kodi ndi chiyembekezo chosangalatsa chotani chimene anthu angakhale nacho lerolino?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena