Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Nchifukwa ninji Yesu analonjeza kuti awo oika chikhulupiriro mwa iye ‘sadzamwalira nthaŵi yonse,’ pamene m’chenicheni omvetsera ake onse anamwalira?—Yohane 11:25, 26.
Pamene Yesu analankhula ponena za kusafa, kapena za kukhala ndi moyo kosatha, iye mowonekera sanatanthauze kuti omvetsera ake kumbuyoko sakakhoza kukumana ndi imfa ya umunthu. Nsonga yaikulu imene Yesu anali kupanga inali yakuti chikhulupiriro mwa iye chikatsogolera ku moyo wosatha.
Pa chochitika chimodzi, Yesu anadzitcha iyemwini “mkate wa moyo.” Kenaka iye anawonjezera kuti: “Mkate wotsika kumwamba ndi uwu, kuti munthu akadyeko ndi kusamwalira. Mkate wa moyo wotsika kumwamba ndine amene; ngati munthu wina akadyako mkate umene adzakhala ndi moyo kosatha.”—Yohane 6:48-51.
Kuyang’ana kokha pa mawu amenewo, munthu angatsirize kuti Yesu anali kuuza omvetsera ake kuti iwo angakhoze kupewa chokumana nacho cha imfa. Mawu ozungulira, ngakhale ndi tero, samachirikiza mathedwe amenewo. Yesu anali atangonena kumene kuti: “Chifuniro cha iye amene anandituma ine ndi ichi, kuti za ichi chonse iye anandipatsa ine ndisatayeko kanthu koma ndichiwukitse tsiku lomalizira. . . . Yense wakuyang’ana Mwana ndi kukhulupirira iye akhale nawo moyo wosatha, ndipo ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza. . . . Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa ine koma ngati Atate, wondituma ine, amukoka iye; ndipo ine ndidzamuwukitsa iye tsiku lomaliza.” (Yohane 6:39-44) Ndipo pambuyo pake iye anawonjezera kuti: “Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nawo moyo wosatha; ndipo ine ndidzamuwukitsa iye tsiku lomalizira.” (Yohane 6:54) Ndiponso, lonjezo la Yesu la ‘kukhala ndi moyo kosatha’ siliyenera molungamitsidwa kumvedwa kukhala likutanthauza kuti omvetsera ake sakakhoza kukumana ndi imfa.
Chiri chofanana ndi lonjezo lodziŵika bwino kwambiri la Yesu kwa Marita: “Ine ndine kuwuka ndi moyo. Wokhulupirira ine, ngakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; ndipo yense wakukhala ndi moyo nakhulupirira ine, sadzamwalira nthaŵi zonse.” (Yohane 11:25, 26) Yesu motsimikizirika sanatanthauze kuti atumwi okhulupirika, mwachitsanzo, sakakhoza kufa monga mmene anachitira anthu ena. Mkati mwa chaka chimodzi, iwo akakhoza kudzozedwa ndi mzimu woyera ndipo akapatsidwa chiyembekezo cha kulamulira monga mafumu kumwamba. Kulandira mphoto imeneyo, iwo akafunikira kufa monga anthu. (Aroma 8:14-23; 1 Akorinto 15:36-50) Ndipo dziŵani kuti Yesu anali atangonena kuti: “Wokhulupirira mwa ine, ngakhale amwalira, adzaukitsidwa.”
Lonjezo la Yesu lidzakwaniritsidwa kulinga kwa atumiki okhulupirika a Mulungu omwe anakhalapo ndi moyo ndi kufa isanafike nthaŵi pamene moyo wosatha ukayamba kuperekedwa. Okhulupirika oterowo ali mu mzere kaamba ka kuwukitsidwa kwa mtsogolo. Mwa kukhala okhulupirika pambuyo pa kuwukitsidwa, iwo sadzakumanapo ndi “imfa yachiŵiri,” imfa yosatha.—Chibvumbulutso 20:15; 21:8; Yohane 8:51.
Koma ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti ife lerolino tiri ndi mwaŵi wapadera. Kukhala monga momwe tiriri m’nthaŵi yotsiriza ya dongosolo loipa la zinthu, tingapulumuke “chisautso chachikulu” chomwe chikudzacho ndi kulowa m’dziko latsopano. Oterewo omwe ali ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’paradaiso ya dziko lapansi ndi omwe amasungirira chikhulupiriro chawo kwa Mulungu sadzafunikira kukumana ndi imfa ya umunthu m’pang’ono pomwe. Pokhala atapulumuka “chisautso chachikulu,” iwo adzatsogozedwa “ku akasupe a madzi a moyo.”—Chibvumbulutso 7:9-17.
[Chithunzi patsamba 31]
Mawu a Yesu kwa Marita wogwidwa ndi chisoniyo amatipatsa ife chiyembekezo cha moyo wosatha