Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Pamene Lazaro Wawukitsidwa
YESU, limodzi ndi awo otsagana naye, tsopano akufika pa manda a chikumbukiro a Lazaro. M’chenicheni, iwo ali phanga lokhala ndi mwala woikidwa poloŵera. “Chotsani mwala,” akutero Yesu.
Marita akutsutsa, asanamvetsetse chimene Yesu akulingalira kuchita. “Ambuye,” iye akunena tero, “adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anayi.”
Koma Yesu akufunsa kuti: “Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupirira, udzawona ulemerero wa Mulungu?”
Chotero mwalawo uchotsedwa. Kenaka Yesu akukweza maso ake ndi kupemphera kuti: “Atate, ndiyamika inu kuti munamva ine. Koma ndadziŵa ine kuti mumandimva ine nthaŵi zonse; koma chifukwa cha khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ichi, kuti akhulupirire kuti inu munandituma ine.” Yesu apemphera poyera kotero kuti anthu adziŵe kuti chimene iye ali pafupi kuchita chidzakwaniritsidwa kupyolera m’mphamvu yolandiridwa kuchokera kwa Mulungu. Kenaka iye afuula ndi mawu aakulu kuti: “Lazaro, tuluka!”
Pa chimenecho, Lazaro atuluka. Manja ake ndi mapazi akali omangidwabe ndi nsalu za kumanda, ndipo nkhope yake iri yophimbidwa ndi mlezo. “Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke,” Yesu akutero.
Powona chozizwitsacho, ambiri a Ayuda omwe anabwera kudzatonthoza Mariya ndi Marita aika chikhulupiriro mwa Yesu. Ena, ngakhale kuli tero, achoka kukawuza Afarisi chomwe chachitika. Iwo ndi akulu ansembe mwamsanga akonza kaamba ka kukumana kwa bwalo lamilandu lapamwamba Lachiyuda, Bwalo lalikulu la Milandu la Ayuda.
Bwalo lalikulu la Mlandu la Ayuda limaphatikizapo Afarisi ndi Asaduki, ansembe aakulu, mkulu wansembe wa panthaŵiyo, Kayafa, ndi omwe kale anali akulu ansembe. Awa adzimverera chisoni kuti: “Titani ife? chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri. Ngati timleka iye kutero, onse adzakhulupirira iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.”
Ngakhale kuti atsogoleri achimpembedzo avomereza kuti Yesu “achita zizindikiro zambiri,” chinthu chokha chimene akudera nacho nkhaŵa chiri malo awo ndi ulamuliro. Kuwukitsidwa kwa Lazaro kuli makamaka nkhonya yamphamvu kwa Asaduki, popeza kuti iwo samakhulupirira m’chiwukiriro.
Kayafa, yemwe ali mwinamwake Msaduki, tsopano akulankhula, akumati: “Simudziŵa kanthu konse inu, kapena simuganiza kuti nkokoma kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu, ndi kuti mtundu wonse usawonongeke.”
Mulungu anasonkhezera Kayafa kunena chimenechi, popeza kuti mtumwi Yohane pambuyo pake analemba kuti: “Koma ichi [Kayafa] sananena kwa iye yekha.” Chimene Kayafa m’chenicheni anatanthauza chinali chakuti Yesu akayenera kuphedwa kuchinjiriza lye kusachepetsa mowonjezereka malo awo a ulamuliro ndi chisonkhezero. Komabe, mogwirizana ndi Yohane, ‘Kayafa ananenera kuti Yesu analinganizidwa kufa osati kaamba ka mtundu wokha, koma kotero kuti ana a Mulungu angasonkhanitsidwe pamodzi.’ Ndipo, ndithudi, chiri chifuniro cha Mulungu kuti Mwana wake afe monga dipo kaamba ka onse.
Kayafa tsopano akupambana m’kusonkhezera Bwalo lalikulu la Milandu la Ayuda kupanga makonzedwe a kupha Yesu. Koma Yesu, mothekera ataphunzira za makonzedwe amenewa kuchokera kwa Nikodemo, chiŵalo cha Bwalo Lalikulu la Milandu la Ayuda yemwe ali waubwenzi kwa iye, akuchoka pamenepo. Yohane 11:38-54.
◆ Nchifukwa ninji Yesu akupemphera poyera asanawukitse Lazaro?
◆ Ndimotani mmene awo omwe anawona chiwukiriro chimenechi akuchitira ku icho?
◆ Nchiyani chomwe chikuvumbula kuipa kwa ziŵalo za Bwalo Lalikulu la Milandu la Ayuda?
◆ Nchiyani chomwe chinali cholinga cha Kayafa, koma nchiyani chimene Mulungu anam’gwiritsira ntchito kulozera?