Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mkulu wa Ansembe Amene Anaphetsa Yesu
    Nsanja ya Olonda—2006 | January 15
    • Kuipa kwa Kayafa kunaonekera poyera pamene iyeyu anauza olamulira anzake kuti: “Kapena simuganiza kuti n’kokoma kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu, ndi kuti mtundu wonse usawonongeke.” Nkhaniyo imapitirira motere: “Koma ichi sananena kwa iye yekha; koma pokhala mkulu wa ansembe chaka chomwecho ananenera kuti Yesu akadzafera mtunduwo; ndipo si chifukwa cha mtunduwo wokha ayi, koma kuti akasonkhanitse pamodzi ana a Mulungu akubalalikawo. Chifukwa chake, kuyambira tsiku lomwelo anapangana kuti amuphe [Yesu].”​—Yohane 11:49-53.

      Kayafa sankadziwa kuti mawu akewo anali ndi tanthauzo lina lapadera. Popeza kuti anali mkulu wa ansembe, iyeyu analosera.b N’zoona kuti imfa ya Yesu inali yopindulitsa, koma osati yopindulitsa Ayuda okha ayi. Nsembe yake ya dipo inapereka njira yomasula anthu onse ku uchimo ndi imfa.

  • Mkulu wa Ansembe Amene Anaphetsa Yesu
    Nsanja ya Olonda—2006 | January 15
    • b M’mbuyomo Yehova anagwiritsa ntchito munthu woipa Balamu kunena ulosi woona wokhudza Aisrayeli.​—Numeri 23:1–24:24.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena