-
Yesu Anaukitsa LazaroYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
Oweruza onse a m’khotili anagwirizana ndi maganizo a Kayafa ofuna kupha Yesu. Koma kodi Nikodemo, yemwe anali m’modzi wa oweruza a m’khotili komanso amene ankadziwana ndi Yesu, anauza Yesu zimene khotili linakonza? Kaya zinthu zinayenda bwanji koma Yesu anachoka m’dera limeneli, lomwe linali kufupi ndi Yerusalemu, kuti asaphedwe pa nthawi imene Mulungu anali asanalole.
-
-
Pa Anthu 10 Akhate, Mmodzi Anathokoza YesuYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
Yesu atachoka m’mudzi womwe unali kufupi ndi ku Betaniya anapita kumzinda wa Efuraimu, womwe unali kumpoto chakum’mawa kwa mzinda wa Yerusalemu. Iye anakonza ulendowu pofuna kulepheretsa zimene akuluakulu a khoti la Sanihedirini anakonza zoti amuphe. Yesu ndi ophunzira ake anakakhala kumzinda wa Efuraimu, komwe kunali kutali ndi adani ake. (Yohane 11:54) Koma mwambo wa Pasika wa mu 33 C.E. unali utatsala pang’ono kuchitika, choncho Yesu sanakhalitse ku Efuraimu. Ananyamuka n’kulowera chakumpoto kukadutsa m’chigawo cha Samariya mpaka anakafika ku Galileya. Umenewu unali ulendo wake womaliza kupita ku Galileya.
-