Lalikirani Choonadi Chonena za Yesu
1 Akristu odzozedwa, mothandizana ndi anzawo a nkhosa zina, ali ndi ntchito yochitira ‘umboni za Yesu.’ (Chiv. 12:17) Imeneyi ndi ntchito yofunika kwambiri, chifukwa chakuti chipulumutso n’chotheka kudzera mwa Yesu yekhayo basi.—Yoh. 17:3; Mac. 4:12.
2 ‘Njira, Choonadi, ndi Moyo’: Yesu anati: “Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.” (Yoh. 14:6) Tingalankhule ndi Mulungu m’pemphero komanso tingakhale naye pa ubwenzi wabwino kudzera mwa Yesu yekha basi, amene ndi “njira.” (Yoh. 15:16) Yesu ndi “choonadi” chifukwa chakuti maulosi ndiponso zinthu za m’Malemba Achihebri zinakwaniritsidwa mwa iye. (Yoh. 1:17; Akol. 2:16, 17) Zoonadi, ntchito yeniyeni ya ulosi woona ndiyo kuunikira udindo wake waukulu pa kukwaniritsidwa kwa cholinga cha Mulungu. (Chiv. 19:10) Komanso, Yesu ndi “moyo.” Kuti onse apeze mphatso ya moyo wosatha, ayenera kukhulupirira nsembe ya dipo imene anapereka.—Yoh. 3:16, 36; Aheb. 2:9.
3 Mutu Komanso Mfumu Yolamulira: Anthu ayeneranso kuzindikira ulamuliro waukulu umene Yehova wapereka kwa Mwana wake. Yesu waikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, amene ‘anthu ayenera kumumvera.’ (Gen. 49:10) Komanso, Yehova wamuika iye kukhala Mutu wa mpingo. (Aef. 1:22, 23) Tifunika kuthandiza anthu amene timaphunzira nawo Baibulo kudziŵa momwe Yesu amayang’anira mpingo ndiponso momwe amagwiritsira ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kupereka “zakudya [zauzimu] panthaŵi yake.”—Mat. 24:45-47.
4 Mkulu wa Ansembe Wachifundo: Popeza kuti Yesu pamene anali padziko lapansi pano anakumana ndi mayesero ndi mavuto, “akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa.” (Aheb. 2:17, 18) N’zolimbikitsa kwambiri kwa anthu opanda ungwiro kudziŵa kuti Yesu amamva chifundo ndi zofooka zawo ndipo amawapempherera mwachikondi. (Aroma 8:34) Pa maziko a nsembe ya Yesu ndi mwa ntchito yake monga Mkulu wa Ansembe, tingalankhule ndi Yehova ‘molimbika mtima’ kuti tipeze ‘thandizo panthaŵi yakusoŵa.’—Aheb. 4:15, 16.
5 Kulimbikira kwathu kuuza ena choonadi chonena za Yesu kuwalimbikitsetu iwowo kuti nawonso amumvere ndi kum’tumikira.—Yoh. 14:15, 21.