Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Ndilibe Mlandu wa Magazi a Anthu Onse”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
    • 12, 13. (a) Kodi mpingo unakhudzidwa bwanji Utiko ataukitsidwa? (b) Kodi ndi mfundo iti ya m’Baibulo imene imatonthoza anthu omwe abale awo anamwalira?

      12 Paulo ndi anzake aja anadutsa m’chigawo cha Makedoniya ali limodzi koma kenako zikuoneka kuti anasiyana. Patapita masiku angapo, zikuoneka kuti anthuwa anakumananso ku Torowa.d Nkhaniyi imati: “Tinawapeza ku Torowa patapita masiku 5.”e (Mac. 20:6) Ku Torowa n’kumene Paulo anaukitsa mnyamata uja Utiko, monga taonera kumayambiriro kwa nkhaniyi. Taganizirani mmene abale ndi alongo anasangalalira ataona kuti Utiko waukitsidwa. Mogwirizana ndi zimene nkhaniyi ikunena, abalewo “anatonthozedwa kwambiri.”​—Mac. 20:12.

  • “Ndilibe Mlandu wa Magazi a Anthu Onse”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
    • d Pa Machitidwe 20:5, 6 Luka anagwiritsa ntchito mawu akuti “ankatiyembekezera” komanso akuti “tinawapeza,” omwe akusonyeza kuti anali limodzi ndi Paulo. N’kutheka kuti anakumananso ndi Paulo ku Filipi, chifukwa Paulo anamusiya mumzinda umenewu m’mbuyomu.​—Mac. 16:10-17, 40.

      e Abalewo anayenda ulendo wapanyanja kwa masiku 5 kuchoka ku Filipi kupita ku Torowa. Zimenezi zikusonyeza kuti mwina panyanjapo panali mphepo yamkuntho chifukwa m’mbuyomu, iwo anayenda ulendo womwewu kwa masiku awiri okha.​—Mac. 16:11.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena