Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Mvetserani Mawu Anga Odziteteza”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
    • 5 Pamsonkhanowu, Paulo ayenera kuti anawauzanso za mphatso zimene anabweretsa kuchokera ku Europe. Abalewo ayenera kuti anasangalala ndiponso kuyamikira kwambiri ataona kuti abale awo am’madera akutali ankawakonda komanso kuwadera nkhawa. Choncho n’zosadabwitsa kuti akuluwo “anayamba kutamanda Mulungu.” (Mac. 21:20a) Masiku anonso Akhristu amene akupirira mavuto aakulu kapena kudwala kwambiri, amalimbikitsidwa Akhristu anzawo akamawathandiza ndiponso kuwauza mawu olimbikitsa.

      Ambiri Anapitirizabe Kukhala “Odzipereka pa Nkhani Yotsatira Chilamulo” (Machitidwe 21:20b, 21)

      6. Kodi Paulo anamva za vuto liti?

      6 Kenako akuluwo anauza Paulo kuti ku Yudeya kuli vuto lina limene linayamba chifukwa cha mphekesera zokhudza iyeyo. Iwo anati: “M’bale, pali Ayuda ambiri okhulupirira ndipo onsewa ndi odzipereka pa nkhani yotsatira Chilamulo. Komatu iwo anamva mphekesera zakuti iwe wakhala ukuphunzitsa Ayuda onse amene ali pakati pa anthu a mitundu ina kuti asiye kutsatira Chilamulo cha Mose. Akuti ukuwauza kuti asamachitenso mdulidwe wa ana awo komanso asamatsatire miyambo imene takhala tikuitsatira kuyambira kalekale.”a​—Mac. 21:20b, 21.

      7, 8. (a) Kodi Akhristu ambiri ku Yudeya anali ndi maganizo ati olakwika? (b) N’chifukwa chiyani sitinganene kuti Akhristuwo anali ampatuko?

      7 N’chifukwa chiyani Akhristu ambiri ankatsatirabe Chilamulo cha Mose ngakhale kuti panali patapita zaka zoposa 20, Chilamulocho chitasiya kugwira ntchito? (Akol. 2:14) Mu 49 C.E. atumwi ndi akulu amene anasonkhana ku Yerusalemu anatumiza kumipingo kalata yofotokoza kuti Akhristu onse a mitundu ina sankafunika kudulidwa ndiponso kutsatira Chilamulo. (Mac. 15:23-29) Komabe, kalatayo sinatchule Akhristu a Chiyuda ndipo ambiri mwa iwo sankamvetsa mfundo yoti Chilamulo cha Mose sichikugwiranso ntchito.

      8 Kodi Akhristu a Chiyudawo anali osayenera kukhala Akhristu chifukwa cha maganizo olakwikawa? Ayi. Sikuti iwo anali ngati anthu amene poyamba ankalambira milungu yabodza ndipo ankapitirizabe kutsatira miyambo ya zipembedzo zawo zakale. Komanso Yehova ndi amene anapereka Chilamulo chimene Akhristu a Chiyudawo ankachionabe kuti ndi chofunika kwambiri. M’Chilamulocho munalibe mfundo iliyonse yolakwika kapena yochokera kwa ziwanda. Kungoti chinali chogwirizana ndi pangano lakale, koma tsopano Akhristu anali m’pangano latsopano. Choncho Akhristu oona sankafunika kutsatira miyambo yogwirizana ndi pangano la Chilamulo chifukwa panganolo linali litasiya kugwira ntchito. Akhristu a Chiheberi amene ankaumirirabe Chilamulo, sankamvetsa komanso sankakhulupirira njira yatsopano yolambirira imene Yehova anakhazikitsa. Iwo ankafunika kusintha maganizo awo kuti agwirizane ndi mfundo zatsopano za choonadi zimene Mulungu ankawaphunzitsa.b​—Yer. 31:31-34; Luka 22:20.

  • “Mvetserani Mawu Anga Odziteteza”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
    • a Popeza panali Akhristu ambiri a Chiyuda, n’kutheka kuti panali mipingo yambiri imene inkasonkhana m’nyumba za abale.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena