Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Mvetserani Mawu Anga Odziteteza”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
    • 11. Kodi akulu anapereka malangizo otani kwa Paulo, ndipo iye anafunika kuchita chiyani pomvera malangizowo? (Onaninso mawu a m’munsi.)

      11 Akhristu a Chiyuda anakhumudwa kwambiri ngakhale kuti mphekesera zomwe anamvazo zinali zabodza. Choncho akulu anapatsa Paulo malangizo akuti: “Tili ndi amuna 4 amene anachita lumbiro. Utenge anthu amenewa ndipo ukachite nawo mwambo wa kudziyeretsa. Uwalipirire zonse zofunika, kuti amete tsitsi lawo. Ukatero, aliyense adziwa kuti mphekesera zimene anamva za iwe ndi nkhambakamwa chabe. Adzaona kuti ukuchita zinthu motsatira dongosolo komanso kuti umasunga Chilamulo.”c​—Mac. 21:23, 24.

      12. Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti anali womvera komanso wokonzeka kusintha, akulu a ku Yerusalemu atamupatsa malangizo?

      12 Paulo akanatha kuuza akuluwo kuti vuto silinali mphekesera zimene anamvazo, koma Akhristu a Chiyudawo, amene ankaumirira kwambiri Chilamulo cha Mose. Koma iye anali wokonzeka kusintha bola ngati zimene anamuuzazo sizikanamuchititsa kuphwanya mfundo za Mulungu. M’mbuyomo, iye anali atalemba kuti: “Kwa anthu otsatira Chilamulo ndinakhala ngati wotsatira Chilamulo kuti ndithandize anthu otsatira chilamulo, ngakhale kuti sinditsatira Chilamulo.” (1 Akor. 9:20) Choncho pa nkhaniyi, Paulo anamvera akulu a ku Yerusalemu ndipo anakhala “ngati wotsatira Chilamulo.” Pamenepa iye anatipatsa chitsanzo chabwino masiku ano kuti tizimvera akulu ndiponso tisamaumirire kuchita zinthu mmene ifeyo tikufunira.​—Aheb. 13:17.

      Zithunzi: 1. Paulo akumvetsera malangizo amene akulu a ku Yerusalemu akumuuza. 2. Pamsonkhano wa akulu, m’bale wina akuyang’ana mwachidwi pamene akulu anzake akukweza manja.

      Paulo ankagonjera ngati palibe chilichonse chosemphana ndi mfundo za m’Malemba. Kodi inunso mumatero?

      MMENE MALAMULO A AROMA ANKAKHUDZIRA NZIKA ZAWO

      Nthawi zambiri, akuluakulu a boma la Roma sankalowerera nkhani za anthu am’madera amene ankalamulira. Tinganene kuti Ayuda anali ndi malamulo awo amene ankatsatira. Koma Aroma analowerera pa mlandu wa Paulo chifukwa chipwirikiti chimene chinayamba iye atafika kukachisi chikanasokoneza mtendere.

      Boma la Roma silinkapereka ufulu wambiri kwa anthu omwe sanali nzika zake m’madera amene ankawalamulira. Komabe anthu amene anali nzika, bomali linkawachitira zinthu mosiyana.f Anthu oterewa ankakhala ndi ufulu wapadera womwe unkalemekezedwa m’madera onse amene ankalamulidwa ndi Aroma. Mwachitsanzo, kumanga kapena kumenya nzika ya Roma asanaizenge mlandu kunali kuphwanya malamulo chifukwa Aroma ankaona kuti zinthu ngati zimenezo zinali zoyenera kuchitira akapolo okha. Komanso nzika za Roma zimene sizinakhutire ndi chigamulo cha bwanamkubwa wa chigawo chawo, zinali ndi ufulu wopempha kuti zikaonekere pamaso pa mfumu ya Roma.

      Panali njira zosiyanasiyana zopezera mwayi wokhala nzika ya Roma. Njira yoyamba inali kubadwira m’banja limene linali nzika. Nthawi zina mafumu a Roma ankatha kupereka mwayi wokhala nzika kwa anthu osiyanasiyana kapena kwa anthu onse okhala mumzinda kapena m’chigawo chinachake, powathokoza akagwira ntchito inayake. Kapolo ankathanso kukhala nzika akagula ufulu kwa nzika ya Roma kapena akamasulidwa ndi Muroma. Komanso msilikali amene si Muroma koma wamenya nkhondo kwa nthawi yaitali pamodzi ndi asilikali a Roma ndipo wapuma pa ntchito, ankapeza mwayi wokhala nzika ya Roma. Zikuoneka kuti nthawi zina zinkathekanso kugula unzika. N’chifukwa chake mkulu wa asilikali Kalaudiyo Lusiya atauza Paulo kuti, “ine ndinagula ufulu wokhala nzika ndi ndalama zambiri,” Paulo anayankha kuti: “Koma ine wanga ndinachita kubadwa nawo.” (Mac. 22:28) Izi zikusonyeza kuti mmodzi wa agogo aamuna a Paulo ayenera kuti anali nzika ya Roma, ngakhale sitikudziwa kuti anaupeza bwanji mwayi umenewu.

      f Mu nthawi ya atumwi, ndi anthu ochepa okha amene ankakhala ku Yudeya omwe anali nzika za Roma. Koma m’zaka za m’ma 200 C.E., anthu amene ankakhala m’madera onse olamuliridwa ndi Aroma anapatsidwa mwayi wokhala nzika za Roma.

  • “Mvetserani Mawu Anga Odziteteza”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
    • c Akatswiri ena amanena kuti amunawo anachita lumbiro lokhala Anaziri. (Num. 6:1-21) N’zoona kuti Chilamulo cha Mose chimene chinali ndi mfundo zokhudza lumbiro limenelo chinali chitasiya kugwira ntchito. Komabe, Paulo ayenera kuti anaganiza kuti palibe cholakwika chilichonse ngati amunawo atachita zimene analumbira kwa Yehova. Choncho panalibe cholakwika kuti awalipirire zonse zofunika ndiponso kupita nawo limodzi. Sitikudziwa lumbiro limene anthuwo anachita. Komabe, zikuoneka kuti Paulo sakanawathandiza kuti apereke nsembe ya nyama (ngati mmene Anaziri ankachitira), chifukwa ankadziwa kuti nsembeyo singathandize munthu kukhala oyera ku machimo ake. Nsembe yangwiro ya Khristu inachititsa kuti nsembe za nyama zisakhalenso ndi mphamvu yochotsa machimo. Sitikudziwa zonse zimene Paulo anachita, komabe tikukhulupirira kuti sakanavomera kuchita chilichonse chosemphana ndi chikumbumtima chake.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena