Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Ndikachita Apilo kwa Kaisara!”
    Nsanja ya Olonda—2001 | December 15
    • Mkulu wa Ansembe Hananiya, pamodzi ndi amuna akulu a Yuda, ndi Tertulo anauza Felike mlandu umene akumuimba Paulo. Iwo ananena kuti Paulo anali ‘kuyambitsa mapanduko pakati pa Ayuda’ ndiponso kuti anali “m’tsogoleri wa m’panduko wa Anazarene.” Iwo ananenanso kuti Paulo ankafuna kuipitsa kachisi.​—Machitidwe 24:1-6.

  • “Ndikachita Apilo kwa Kaisara!”
    Nsanja ya Olonda—2001 | December 15
    • Mkulu wa Ansembe Hananiya, pamodzi ndi amuna akulu a Yuda, ndi Tertulo anauza Felike mlandu umene akumuimba Paulo. Iwo ananena kuti Paulo anali ‘kuyambitsa mapanduko pakati pa Ayuda’ ndiponso kuti anali “m’tsogoleri wa m’panduko wa Anazarene.” Iwo ananenanso kuti Paulo ankafuna kuipitsa kachisi.​—Machitidwe 24:1-6.

  • “Ndikachita Apilo kwa Kaisara!”
    Nsanja ya Olonda—2001 | December 15
    • Ayuda ankanena kuti zomwe Paulo ankaphunzitsa sizinali Chiyuda kapena chipembedzo chovomerezeka (religio licita). Choncho ankaziona kukhala zosaloledwa ndiponso zolimbikitsa kuukira boma.

      Iwo ankanena kuti Paulo anali ‘kuyambitsa mapanduko kwa Ayuda onse m’dziko lonse lokhalamo anthu.’ (Machitidwe 24:5) Panthaŵiyo n’kuti Mfumu Klaudiyo ataweruza kumene Ayuda a ku Alexandria chifukwa cha “kuyambitsa tsoka lomwe linakhudza aliyense m’dziko lonselo.” Kufanana kwa milandu iŵiriyo n’kochititsa chidwi kwambiri. Wolemba mbiri wina, A. N. Sherwin-White, ananena kuti: “Anali kumuimba mlandu Myuda wina pa nthaŵi imene Klaudiyo anali kulamulira m’boma la Lipabuliki kapena kuchiyambi kwa ulamuliro wa Nero. Ayuda anali kuyesetsa kupangira kazembeyo kuti aone kulalikira kwa Paulo monga kuyambitsa chisokonezo pakati pa Ayuda onse mu Ufumu Waukuluwo. Iwo ankadziŵa kuti akazembe sankafuna kuweruza anthu pazifukwa za chipembedzo. Chotero, anayesa kupotoza mlanduwo kuti ukhale wandale osatinso wachipembedzo.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena