Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesu Amadyetsa Anthu Ambiri Kudzera mwa Anthu Ochepa
    Nsanja ya Olonda—2013 | July 15
    • 8. Kodi pa Pentekosite, Akhristu atsopano anasonyeza bwanji kuti ankadziwa bwino anthu amene Khristu anali kuwagwiritsa ntchito podyetsa ophunzira ake?

      8 Khristu ataukitsidwa, ankagwiritsa ntchito atumwi podyetsa ophunzira ake odzozedwa. Izi zinayamba pa Pentekosite mu 33 C.E. (Werengani Machitidwe 2:41, 42.) Ayuda ndiponso anthu olowa Chiyuda, omwe anadzozedwa pa tsikulo, ankadziwa bwino zimenezi. Iwo “anapitiriza kulabadira zimene atumwiwo anali kuphunzitsa.” Katswiri wina ananena kuti mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “anapitiriza kulabadira,” angatanthauzenso kuti “sankafuna ngakhale pang’ono kusiya zimene anayamba kuchita.” Akhristu atsopanowa ankafunitsitsa kuphunzira Mawu a Mulungu ndipo ankadziwa anthu amene angawaphunzitse. Iwo ankadalira atumwi ndi mtima wonse kuti awaphunzitse za Yesu ndiponso awathandize kumvetsa bwino malemba onena za iye.c—Mac. 2:22-36.

  • Yesu Amadyetsa Anthu Ambiri Kudzera mwa Anthu Ochepa
    Nsanja ya Olonda—2013 | July 15
    • c Ndime 8: Mawu akuti Akhristu atsopano “anapitiriza kulabadira zimene atumwiwo anali kuphunzitsa” akusonyeza kuti atumwi ankaphunzitsa anthu nthawi zonse. Zinthu zina zimene atumwi ankaphunzitsa zinalembedwa m’mabuku a Malemba Achigiriki.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena