-
“Anadzazidwa ndi Mzimu Woyera”‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
-
-
16. Kodi Akhristu a m’nthawi ya atumwi anasonyeza bwanji kuti anali opatsa?
16 N’zodziwikiratu kuti Yehova anadalitsa gulu la anthu amenewo. Nkhaniyo imati: “Onse amene anakhala okhulupirira ankakhala limodzi ndipo ankagawana zinthu zonse zimene anali nazo. Ankagulitsa malo awo ndi zinthu zina zimene anali nazo, n’kugawa kwa onse zimene apeza, mogwirizana ndi zimene aliyense akufunikira.”f (Mac. 2:44, 45) Akhristu onse oona ayenera kusonyeza chikondi poyesetsa kukhala opatsa potsanzira zimene ophunzirawo anachita.
-
-
“Anadzazidwa ndi Mzimu Woyera”‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
-
-
f Akhristuwo anachita zimenezi kwa nthawi yochepa pofuna kuthandiza alendo amene anatsalira ku Yerusalemu kuti apitirizebe kuphunzira zina ndi zina zokhudza chikhulupiriro chawo chatsopanocho. Iwo anapereka zinthu zawo mwa kufuna kwawo chifukwa cha chikondi ndipo sitiyenera kuganiza kuti anachita zimenezi potsatira mfundo imene anthu ena amanena, yoti munthu aliyense ali ndi ufulu wogwiritsa ntchito zinthu za ena mmene akufunira.—Mac. 5:1-4.
-