-
“Ife Tiyenera Kumvera Mulungu Monga Wolamulira”‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
-
-
Mofanana ndi atumwi, ifenso timalalikira “kunyumba ndi nyumba”
16. Kodi atumwi anasonyeza bwanji kuti ndi otsimikiza mtima kuchitira umboni mokwanira, ndipo ifeyo timatsanzira bwanji njira imene iwo ankagwiritsa ntchito polalikira?
16 Atumwi sanachedwe kuyambiranso ntchito yawo yolalikira. Mopanda mantha, iwo “tsiku lililonse anapitiriza kuphunzitsa mwakhama m’kachisi ndiponso kunyumba ndi nyumba komanso ankalengeza uthenga wabwino wonena za Khristu Yesu.”d (Mac. 5:42) Atumwi amenewa, omwe ankalalikira mwakhama, anatsimikiza mtima kuchitira umboni mokwanira. Onani kuti iwo ankapita m’makomo a anthu kukalalikira uthenga wabwino potsatira zimene Yesu Khristu anawauza. (Mat. 10:7, 11-14) N’chifukwa chake anakwanitsa kudzaza Yerusalemu ndi mfundo zimene ankaphunzitsa. Masiku ano, Mboni za Yehova zimadziwika chifukwa chotsatira njira ya atumwi imeneyi polalikira. Tikamalalikira kunyumba ndi nyumba m’gawo lathu, timasonyeza kuti ifenso tikufuna kuonetsetsa kuti wina aliyense ali ndi mwayi woti amve uthenga wabwino. Kodi Yehova wadalitsa utumiki wathu wa kunyumba ndi nyumba? Inde. M’nthawi ya mapeto ino, anthu ambirimbiri akhala atumiki a Mulungu ndipo ambiri anamva koyamba za uthenga wabwino umenewu a Mboni atafika panyumba pawo.
-