Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Ndiwe Mkazi Wokongola”
    Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2017 | Na. 3
    • Tsiku lina Abulahamu anapita kwa Sara akuoneka wosangalala kwambiri. Anali atalankhula ndi Yehova Mulungu amene anaonekera kwa iye kudzera mwa mngelo. Sara atamva zimenezi mtima wake unali phaphapha ndipo ankafunitsitsa kuti amve zimene mngeloyo ananena. Mwina Abulahamu anakhala kaye pansi, uku akuyesa kuganizira zoti anene. Kenako anauza Sara kuti Yehova wamuuza kuti: “Tuluka m’dziko lako ndi pakati pa abale ako. Tiye ukalowe m’dziko limene ine ndidzakusonyeza.” (Machitidwe 7:2, 3) Kenako banjali linayamba kuganizira zimene Yehova anawauzazi. Ankafunika kusiya moyo wawofuwofu n’kukayamba moyo wosamukasamuka komanso wokhala m’mahema. Ndiye kodi pamenepa Sara akanatani? Kodi akanavomera kusamuka ndi mwamuna wake, ngakhale kuti izi zikanasintha kwambiri moyo wawo? Abulahamu ayenera kuti ankangoyang’anitsitsa mkazi wakeyu kuti aone kuti atani.

      Mwina tingaganize kuti zimene zinachitikira Sara sizingatichitikire ifeyo. Tingamaganize kuti, ‘Mulungu sanatipemphepo kuti tichite zinthu ngati zimenezi.’ Komatu zoona n’zakuti tonsefe nthawi zina timafunika kusankha pa zinthu ngati zimenezi. Dziko limene tikukhalali lingatipangitse kuti tizingoganizira zokhala ndi moyo wawofuwofu, katundu wambiri komanso kukonza tsogolo. Koma Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziika zinthu zokhudza kulambira Mulungu pamalo oyamba. (Mateyu 6:33) Choncho tikamaganizira zimene Sara anasankha pa nkhaniyi, tizidzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndikufuna kusankha kuchita chiyani pa moyo wanga?’

  • “Ndiwe Mkazi Wokongola”
    Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2017 | Na. 3
    • Koma panalinso nkhani ina yovuta kwambiri kwa Sara. Iye anafunika kusiya achibale ake. Paja Mulungu anauza Abulahamu kuti: “Tuluka m’dziko lako ndi pakati pa abale ako.” Mayi wachikondi komanso wochezeka ameneyu ayenera kuti ankagwirizana kwambiri ndi azichimwene ake, azichemwali ake, azimalume ake, azakhali ake komanso ana aamuna ndi aakazi a azibale akewa. Ndipotu panalibe umboni woti adzakumana nawonso. Komabe Sara anachita zinthu molimba mtima ndipo anapitiriza kukonzekera ulendo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena