Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 11/1 tsamba 4-7
  • Mmene Mungathetsere Mavuto Mwamtendere

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungathetsere Mavuto Mwamtendere
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchoka pa Wachiwawa Kukhala Wololera
  • Kulimbana ndi Malingaliro Ofuna Kuchita Chiwawa
  • Kodi Nzotheka?
  • Kodi Mulungu Amachiona Bwanji Chiwawa?
    Galamukani!—2002
  • Kodi Zachiwawa Zidzatha Padzikoli?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Pitani Patsogolo Mwauzimu Potsanzira Paulo
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi N’chifukwa Chiyani Saulo Anazunza Akristu?
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 11/1 tsamba 4-7

Mmene Mungathetsere Mavuto Mwamtendere

CHIWAWA cha anthu chakhalapo pafupifupi chiyambire kukhalapo kwa mtundu wa anthu. Baibulo limasonyeza kuti nkhanza inayamba kalelo ndi Kaini, mbale wake wa Abele ndiponso mwana wamwamuna woyamba wa anthu aŵiri oyambirira. Pamene Mulungu anakondapo nsembe ya Abele ndipo osati ya Kainiyo, iye “anakwiya kwambiri.” Ndiye anatani pamenepo? “Kaini anamuukira Abele mphwake, namupha.” Kenako anakhala pavuto lalikulu kwambiri ndi Mulungu. (Genesis 4:5, 8-12) Nkhanza siinathetse vuto la kaimidwe koipa ka Kaini pamaso pa Mlengi wake.

Kodi tingaipeŵe motani njira ya Kaini yogwiritsira ntchito mphamvu yakuthupi pofuna kuthetsa mavuto?

Kuchoka pa Wachiwawa Kukhala Wololera

Talingalirani za munthu amene analola ndi kupenyerera kuphedwa kwa Stefano, Mkristu woyamba kufera chikhulupiriro chake. (Machitidwe 7:58; 8:1) Munthuyo, Saulo wa ku Tariso, sanali kugwirizana ndi chipembedzo cha Stefano ndipo anavomereza kuti njira yabwino yoletsera ntchito za Stefano ndiyo kumupha mwankhanza. Inde, mwina Saulo sanali wachiwawa pazochita zake zonse. Koma anavomereza chiwawa ndi mtima wonse monga njira yothetsera mavuto. Kungochokera pa imfa ya Stefano, Saulo “anapasula [“anayamba kusakaza,” NW] Mpingo [wachikristu], naloŵa m’nyumba m’nyumba, nakokamo amuna ndi akazi, nawaika m’ndende.”​—Machitidwe 8:3.

Malinga nkunena kwa katswiri wa maphunziro a za Baibulo Albert Barnes, liwu lachigiriki lotembenuzidwa pano kuti “kusakaza” limasonyeza kuwononga kumene zilombo, monga mikango ndi ankhandwe, zingachite. “Saulo,” anafotokoza motero Barnes, “anachita mpingo chiwawa monga chilombo​—mawu amphamvu, osonyeza changu ndi mkwiyo umene anachitira chizunzo.” Pamene Saulo anali kupita ku Damasiko kuti akagwire otsatira a Kristu owonjezereka, iye anali adakali “wosaleka kupumira pa akuphunzira a Ambuye [Kristu] kuopsa ndi kupha.” Ali paulendowo, Yesu woukitsidwayo anamlankhula, ndipo zimenezi zinapangitsa Saulo kutembenuka kukhala Mkristu.​—Machitidwe 9:1-19.

Atatembenuka, zochita za Saulo kwa ena zinasintha. Zimene zinachitika patapita zaka 16 zinasonyeza kusintha kumeneku. Khamu la anthu linafika pampingo wakwawo ku Antiokeya ndi kulimbikitsa Akristu kumeneko kuti azitsatira Chilamulo cha Mose. Panabuka “makani.” Saulo, wodziŵika kwambiri kuti Paulo panthaŵiyi, analoŵapo pamtsutsanowu. Mwachionekere, panali kutsutsana kwamphamvu. Koma Paulo sanachite chiwawa. M’malo mwake, anagwirizana ndi chosankha cha mpingo choti apereke nkhaniyo kwa atumwi ndi akulu kumpingo wa ku Yerusalemu.​—Machitidwe 15:1, 2.

Ku Yerusalemunso kunachitika “mafunsano ambiri” pamsonkhano wa akuluwo. Paulo anadikira kufikira “khamu lonse linatonthola” kenako anapereka lipoti la ntchito yodabwitsa ya mzimu wa Mulungu pakati pa okhulupirira osadulidwa. Atakambitsirana Malemba, atumwi ndi akulu a ku Yerusalemu ‘anagwirizana ndi mtima umodzi’ kuti asathodwetse okhulupirira osadulidwa ndi zinthu zosafunika koma kuwalangiza ‘kuti asale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama.’ (Machitidwe 15:3-29) Ndithudi, Paulo anali atasintha. Anaphunzira kuthetsa nkhani mosachita chiwawa.

Kulimbana ndi Malingaliro Ofuna Kuchita Chiwawa

“Kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndewu,” analangiza motero Paulo pambuyo pake, “komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziŵa kuphunzitsa, woleza, wolangiza iwo akutsutsana mofatsa.” (2 Timoteo 2:24, 25) Paulo analimbikitsa Timoteo, woyang’anira wocheperapo msinkhu, kuti azisamalira nkhani zovuta moleza mtima. Paulo anali kunena zenizeni. Anadziŵa kuti ngakhale pakati pa Akristu pangakhale kupsetsana mtima. (Machitidwe 15:37-41) Pachifukwa chabwino analangiza kuti: “Kwiyani, koma musachimwe; dzuŵa lisaloŵe muli chikwiyire.” (Aefeso 4:26) Ukakwiya, kudziletsa popanda kuzaza ndiyo njira yabwino yothetsera mkwiyo. Koma kodi zimenezi mungazichite motani?

Lerolino, nzovuta kudziletsa pamkwiyo. “Kukhala waukali nkofala,” anatero Dr. Deborah Prothrow-Stith, woyang’anira wachiŵiri pa Sukulu ya Harvard ya Zaumoyo wa Anthu. “Kwenikweni, mikhalidwe yofunika kuti pakhale kumvana​—kukambirana, kumva za wina, chifundo, kukhululukira​—ndi imene nthaŵi zambiri amati ndi mikhalidwe ya anthu amantha.” Koma imeneyo ndiyo mikhalidwe yachamuna, ndipo ndiyo yofunika kwambiri poletsa malingaliro ofuna kuchita chiwawa amene angaloŵe m’mitima mwathu.

Atakhala Mkristu, Paulo anaphunzira njira yabwino kwambiri yochitira zinthu pakakhala kusiyana malingaliro. Njirayo inazikidwa paziphunzitso za Baibulo. Pokhala katswiri wamaphunziro a Chiyuda, Paulo anali kuwadziŵa bwino Malemba Achihebri. Ayenera kuti anali kukumbukira bwino malemba monga akuti: “Usachitire nsanje munthu wachiwawa; usasankhe njira yake iliyonse.” “Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; wolamulira mtima wake naposa wolanda mudzi.” “Wosalamulira mtima wake akunga mudzi wopasuka wopanda linga.” (Miyambo 3:31; 16:32; 25:28) Komabe, chidziŵitso chimenecho sichinamletse Paulo kuchita Akristu chiwawa iye asanakhale Mkristu. (Agalatiya 1:13, 14) Koma kodi nchiyani chinathandiza Paulo, monga Mkristu, kuti azithetsa nkhani zokwiyitsa mwa kukambirana ndi kulimbikitsa m’malo mwa chiwawa?

Paulo anatisonyeza njira pamene anati: “Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Kristu.” (1 Akorinto 11:1) Anayamikira kwambiri zimene Yesu Kristu anamchitira. (1 Timoteo 1:13, 14) Kristu anakhala chitsanzo chake. Anadziŵa mmene Yesu anazunzikira kaamba ka mtundu wa anthu ochimwa. (Ahebri 2:18; 5:8-10) Paulo anapereka chitsimikizo chakuti ulosi wa Yesaya wonena za Mesiya unakwaniritsidwa ndi Yesu: “Iye anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha osatsegula pakamwa pake; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwana wa nkhosa amene ali du pamaso pa omsenga, motero sanatsegula pakamwa pake.” (Yesaya 53:7) Mtumwi Petro analemba kuti: “[Yesu] pochitidwa chipongwe sanabwezera chipongwe, pakumva zoŵaŵa, sanaopsa, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama.”​—1 Petro 2:23, 24.

Paulo anasonkhezereka kusintha atazindikira njira imene Yesu Kristu anachitira ndi mikhalidwe yovutitsa. Analangiza okhulupirira anzake kuti: “[Pitirizani] kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso.” (Akolose 3:13) Kungovomereza kuti sitiyenera kukhala achiwawa sikokwanira. Kuyamikira zimene Yehova ndi Yesu Kristu atichitira kumathandizira kutisonkhezera moyenerera kuti tigonjetse malingaliro ofuna kuchita chiwawa.

Kodi Nzotheka?

Mwamuna wina ku Japan anafunikira chisonkhezero champhamvu chimenecho. Atate wake, amene anali msilikali wamtima wapachala, ankalamulira banja lawo mwankhanza. Pokhala wochitidwa nkhanza ndiponso poona amayi wake akuvutika mofananamo, mwamunayo anakhalanso wankhanza. Anali kunyamula malupanga aŵiri a samurai autali wosiyana amene anali kuwasolola pofuna kuthetsa mavuto ndi poopseza anthu.

Pamene mkazi wake anayamba kuphunzira Baibulo, iye anapezeka paphunzirolo mongoyesa. Koma ataŵerenga kabuku kakuti Mbiri Yabwino Imeneyi ya Ufumu,a anasintha. Chifukwa? “Nditaŵerenga pamutu waung’ono wakuti ‘Yesu Kristu’ ndi ‘Dipo,’ ndinachita manyazi,” anafotokoza motero. “Ngakhale kuti ndinali wopulupudza, ndinkakondabe kusonyeza kukoma mtima kwa aja amene ndinali kugwirizana nawo. Ndinali kukondwera ndikamasangalatsa mabwenzi anga koma kokha ngati zimenezo sizikukhudza moyo wanga. Koma, Mwana wa Mulungu, Yesu, anali wofunitsitsa kupereka moyo wake m’malo mwa mtundu wa anthu, kuphatizikizapo anthu monga ine. Ndinazizwa, monga kuti wina wandipanda ndi nyundo ya mtengo.”

Anasiya kuyanjana ndi mabwenzi ake akale ndipo posapita nthaŵi analembetsa Sukulu ya Utumiki Wateokratiki mumpingo wa Mboni za Yehova. Sukulu imeneyi imathandizira olembetsawo kuphunzira luso lophunzitsa ena Baibulo. Kosiyo inapindulitsa mwamunayu m’njira inanso. Akukumbukira kuti: “Pamene ndinali wamng’ono, ndinali kuopseza ena ndi kuwachita nkhanza chifukwa chakuti sindinali kutha kufotokozera ena za mumtima mwanga. Pamene ndinaphunzira kufotokozera ena za mumtima mwanga, ndinayamba kukambirana nawo m’malo mochita chiwawa.”

Kodi iye, monga Paulo, wapanga njira ya moyo ya Kristu kukhala yake? Chikhulupiriro chake chinayesedwa pamene bwenzi lake lakale limene anapangana nalo pangano la ubale linayesa kumletsa kuti asakhale Mkristu. “Bwenzi” lakelo linampanda ndipo linatukwana Mulungu wake, Yehova. Mwamunayu amene kale anali wachiwawa anadziletsa napepesa polephera kusunga pangano lawo. Atakhumudwa, “mbale” wakeyo anamsiya.

Mwa kugonjetsa malingaliro ake ofuna kuchita chiwawa, mwamuna amene kale anali waukali ameneyu wapeza abale ndi alongo auzimu, ambiri amene ali muumodzi wa chikondi cha pa Mulungu ndi anansi awo. (Akolose 3:14) Ndiponso, patapita zaka zoposa 20 atakhala Mkristu wodzipatulira, iye tsopano akutumikira monga woyang’anira woyendayenda wa Mboni za Yehova. Akusangalala chotani nanga kusonyeza mogwiritsira ntchito Baibulo kuti anthu onga zilombo angaphunzire kuthetsa mikangano popanda chiwawa monga momwe iye anachitira! Ndipotu ali ndi mwayi waukulu chotani nanga wofotokoza kukwaniritsidwa kwakukulu kwa mawu aulosiwo akuti: “Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”​—Yesaya 11:9.

Monga mtumwi Paulo ndi mwamuna amene kale anali wachiwawa ameneyu, inunso mungaphunzire kulaka mikhalidwe yokwiyitsa, kuthetsa mavuto mwamtendere. Mboni za Yehova za kwanu konko nzofunitsitsa kukuthandizani.

[Mawu a M’munsi]

a Kofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Paulo anali kunena zenizeni. Anadziŵa kuti ngakhale pakati pa Akristu pangakhale kupsetsana mtima

[Chithunzi patsamba 7]

Kuyamikira zimene Mulungu watichitira kumatipangitsa kukhala ndi maunansi abwino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena