Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 5/15 tsamba 10-15
  • Mulungu Alibe Tsankho

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mulungu Alibe Tsankho
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mlengi Wathu​—Watsankho?
  • Kodi Yesu Anali Watsankho?
  • Kusintha Kwakukulu
  • “Kuchokera mwa Mtundu Uliwonse”
  • Chikondi cha pa Mnansi Nchotheka
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Yehova “Alibe Tsankho”
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Tonsefe Tikhale Ogwirizana Ngati Yehova ndi Yesu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • “Mulungu Alibe Tsankho”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 5/15 tsamba 10-15

Mulungu Alibe Tsankho

“Mulungu alibe tsankho, koma m’mitundu yonse, wakuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”​—MACHITIDWE 10:34, 35.

1. Mu Atene wakale, kodi ndi ganizo lofunika lotani limene Paulo anapanga ponena za fuko?

“MULUNGU yemwe anapanga dziko ndi zonse zomwe zirimo, akumakhala Mbuye wa ponse paŵiri Kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m’makachisi opangidwa ndi anthu. . . . Kuyambira ku kholo limodzi iye walenga fuko lirilonse la anthu kukhala pa nkhope ya dziko lonse lapansi.” (Machitidwe 17:24-26, Phillips) Ndani amene analankhula mawu amenewo? Mtumwi Wachikristu Paulo, mkati mwa uthenga wake wotchuka pa Phiri la Mara, kapena Areopagi, mu Atene, Grisi.

2. Nchiyani chimene chimathandizira kupanga moyo kukhala wokongola ndi wosangalatsa, ndipo nchiyani chimene mlendo mmodzi wa ku Japan anasangalatsidwa nacho mu South Africa?

2 Ganizo la Paulo moyenerera lingatipangitse ife kuganizira ponena za kusiyana kosangalatsa komwe kulipo m’chilengedwe. Yehova Mulungu analenga anthu, zinyama, mbalame, tizirombo, ndi mitengo ya mitundu yosiyanasiyana. Ndi mosasangalatsa chotani nanga mmene moyo ukanakhalira ngati zonse zinali zofanana! Kusiyana kwawo kumapangitsa kupanga moyo kukhala wokongola ndi wosangalatsa. Mwachitsanzo, mlendo wochokera ku Japan akupezeka pa msonkhano wa Mboni za Yehova mu South Africa anakondweretsedwa ndi ukulu wa fuko ndi mtundu wowonedwa pamenepo. Iye anachitira ndemanga mmene chinaliri chosiyana ku Japan, kumene ambiri a iwo ali ndi zizindikiro zofanana za ufuko.

3. Ndimotani mmene ena amawonera mtundu wa khungu losiyana, kudzutsa chiyani?

3 Koma kuchulukira kwa mtundu pakati pa mafuko kaŵirikaŵiri kumapangitsa mavuto okulira. Ambiri amalingalira awo a khungu la mtundu wosiyana kukhala otsika. Ichi chimautsa nkhwidzi, ngakhale udani ndi mliri wa kunyada kwa ufuko. Kodi Mlengi wathu anafuna kuti ichi chikhale tere? Kodi mafuko ena ali apamwamba m’maso mwake? Kodi Yehova ali watsankho?

Mlengi Wathu​—Watsankho?

4-6. (a) Nchiyani chimene Mfumu Yehosafati ananena ponena za tsankho? (b) Ndimotani mmene ponse paŵiri Mose ndi Paulo anatsimikizira ndemanga ya Yehosafati? (c) Ndi mafunso otani amene ena angadzutse?

4 Tingapeze lingaliro lina la kawonedwe ka Mlengi wathu ka mtundu wonse wa anthu mwa kubwerera m’mbuyo m’mbiri yakale. Mfumu Yehosafati, yemwe analamulira Yuda kuyambira 936 mpaka 911 B.C.E., anapanga kuwongokera kochuluka ndipo anakonzekeretsa kaamba ka kugwira ntchito koyenerera kwa dongosolo la lamulo lozikidwa pa lamulo laumulungu. Iye anapereka uphungu wabwino uwu kwa oweruza: “Khalani maso umo muchitira, pakuti simuweruzira anthu koma Yehova . . . musamalire ndi kuchita, pakuti palibe chosalungama kwa Yehova Mulungu wathu, kapena kusamalira monga mwa nkhope ya munthu.”​—2 Mbiri 19:6, 7.

5 Mazana a zaka poyambirirapo, mneneri Mose anali atauza mafuko Aisrayeli kuti: “Yehova Mulungu wathu . . . wosasamalira nkhope za anthu.” (Deuteronomo 10:17) Ndipo m’kalata yake kwa Aroma, Paulo anachenjeza kuti: “Padzakhala mavuto ndi nsautso kwa munthu aliyense yemwe ali wochita choipa, kwa Myuda choyamba ndipo kwa m’Griki . . . Popeza Mulungu alibe amene amawakondera.”​—Aroma 2:9-11, The New English Bible.

6 Koma ena angafunse kuti: ‘Bwanji ponena za Aisrayeli? Kodi iwo sanali anthu osankhidwa a Mulungu? Kodi iye sanali watsankho kulinga kwa iwo? Kodi Mose sanawauze Aisrayeli onse kuti: “Yehova Mulungu wanu anakusankhani, mukhale mtundu wa pawokha kwa iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu akukhala pa nkhope ya dziko”?’​—Deuteronomo 7:6.

7. (a) Kodi nchiyani chimene chinatulukapo pamene Ayuda anakana Mesiya? (b) Lerolino, kodi ndani yemwe angasangalale ndi madalitso odabwitsa kuchokera kwa Mulungu, ndipo motani?

7 Ayi, Mulungu sanali watsankho m’kugwiritsira ntchito Aisrayeli kaamba ka chifuno chapadera. Kusankha anthu kupyolera mwa amene akatulutsa Mesiya, Yehova anasankha mbadwa za makolo a Chihebri okhulupirika. Koma pamene Ayuda anakana Mesiya, Yesu, ndi kumpangitsa iye kuphedwa, iwo anataya chiyanjo cha Mulungu. Lerolino, ngakhale kuli tero, awo a fuko kapena mtundu uliwonse omwe amasonyeza chikhulupiriro mwa Yesu angasangalale ndi madalitso ozizwitsa ndipo angakhale ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. (Yohane 3:16; 17:3) Ndithudi, ichi chikutsimikizira kuti kulibe tsankho kumbali ya Mulungu. M’kuwonjezerapo, Yehova analamulira Aisrayeli “kukondana naye mlendo” ndi “kusamsautsa,” mosasamala kanthu za fuko lake kapena mtundu. (Deuteronomo 10:19; Levitiko 19:33, 34) Zowonadi, chotero, Atate wathu wa kumwamba sali watsankho.

8. (a) Kodi nchiyani chimene chimatsimikizira kuti Yehova sanasonyeze tsankho kulinga kwa Israyeli? (b) Kodi ndimotani mmene Yehova anagwiritsira ntchito Israyeli?

8 Chiri chowona kuti Aisrayeli anasangalala ndi mwaŵi wapadera. Koma analinso ndi thayo lalikulu. Iwo anali pansi pa thayo la kusunga malamulo a Yehova, ndipo awo olephera kumvera iwo anabwera pansi pa temberero. (Deuteronomo 27:26) M’chenicheni, Aisrayeli anayenera kulangidwa mobwerezabwereza chifukwa cha kusamvera Lamulo la Mulungu. Chotero, Yehova sanachite nawo ndi kukondera. M’malomwake, iye anawagwiritsira ntchito iwo kupanga dongosolo la ulosi ndi kupereka zitsanzo zochenjeza. Mwachimwemwe, chinali kupyolera mwa Israyeli kuti Mulungu anatulutsa Mpulumutsi, Yesu Kristu, kaamba ka dalitso la mtundu wonse wa anthu.​—Agalatiya 3:14; yerekezani ndi Genesis 22:15-18.

Kodi Yesu Anali Watsankho?

9. (a) Kodi ndimotani mmene Yehova ndi Yesu aliri ofanana? (b) Kodi ndi mafunso otani omwe amabuka ponena za Yesu?

9 Popeza palibe tsankho ndi Yehova, kodi Yesu angakhale watsankho? Chabwino, lingalirani ichi: Yesu kamodzi ananena kuti: “Sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha iye wondituma ine.” (Yohane 5:30) Umodzi wangwiro ulipo pakati pa Yehova ndi Mwana wake wokondedwa, ndipo Yesu amachita chifuniro cha Atate wake m’njira iriyonse. M’chenicheni, iwo ali ofanana m’kawonedwe ndi cholinga chakuti Yesu ananena kuti: “Iye amene wandiwona ine wawona Atate.” (Yohane 14:9) Kwa zaka zoposa 33, Yesu m’chenicheni analaŵa kukhala monga munthu padziko lapansi, ndipo Baibulo limavumbulutsa mmene anachitira ndi anthu anzake. Nchiyani chimene chinali kawonedwe kake kulinga kwa mafuko ena? Kodi iye anali wonyada kapena watsankho? Kodi Yesu anali wa ufuko?

10. (a) Kodi ndimotani mmene Yesu anayankhira ku funso la mkazi wa ku Fonike kaamba ka thandizo? (b) Mwakutchula Akunja kukhala “tiagaru tochepa,” kodi Yesu anali kusonyeza tsankho? (c) Kodi ndimotani mmene mkaziyo anagonjetsera chitsutso, ndipo ndi chotulukapo chotani?

10 Yesu anathera mbali yokulira ya moyo wake wa padziko lapansi ndi anthu Achiyuda. Koma tsiku lina iye anafikiridwa ndi mkazi wa ku Fonike, Wakunja, yemwe anam’pempha iye kuchiritsa mwana wake wamkazi. M’kuyankha Yesu anati: “Sindinatumidwa kwa ena koma kwa nkhosa zotaika za banja la Israyeli.” Komabe, mkaziyo anadandaula: “Ambuye, ndithangateni ine.” Pa chimenecho, iye anawonjezera: “Sichabwino kutenga mkate wa ana, ndi kuponyera tiagaru.” Kwa Ayuda, agaru anali nyama zodetsedwa. Chotero mwakulozera kwa Akunja monga “tiagaru,” kodi Yesu anasonyeza kunyada? Ayi, popeza iye anali atangotchula kumene ntchito yake yapadera yochokera kwa Mulungu kusamalira kaamba ka ‘nkhosa zotaika za Israyeli.’ M’kuwonjezerapo, mwakuyerekeza osakhala Ayuda ndi “tiagaru tochepa,” osati nkhandwe, Yesu anafewetsako kuyerekezako. Ndithudi, chimene iye ananena chinayesa mkaziyo. Modzichepetsa, ngakhale kuti anagamulapo kulaka chitsutso chimenechi, iye mwaluntha anayankha kuti: “Etu, Ambuye, pakutinso tiagaru timadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye awo.” Posangalatsidwa ndi chikhulupiriro cha mkaziyo, Yesu anachiritsa mwana wake wamkazi panthaŵi yomweyo.​—Mateyu 15:22-28.

11. Monga mmene chachitidwira chitsanzo ndi chochitika chokhudza Yesu, ndi kawonedwe kotani kamene Ayuda ndi Asamariya anali nako kulinga kwa wina ndi mnzake?

11 Lingalirani, kachiŵirinso, chokumana nacho cha Yesu ndi Asamariya ena. Nkhwidzi yozama inalipo pakati pa Ayuda ndi Asamariya. Pa chochitika chimodzi, Yesu anatumiza amithenga kukamkonzekera malo iye m’mudzi wina wa Chisamariya. Koma Asamariya amenewo “sanamlandira iye, chifukwa nkhope yake inali yoloza kunka ku Yerusalemu.” Ichi chinakhumudwitsa Yakobo ndi Yohane ku nsonga yakuti iwo anafuna kuitanira moto kuchokera kumwamba kuwapsyereza iwo. Koma Yesu anadzudzula ophunzira aŵiriwo, ndipo onse a iwo anapita ku mudzi wina.​—Luka 9:51-56.

12. Nchifukwa ninji mkazi wina wa Chisamariya anadabwitsidwa pa pempho la Yesu?

12 Kodi Yesu anagawana malingaliro ankhwidzi omwe analipo pakati pa Ayuda ndi Asamariya? Chabwino, dziŵani chimene chinachitika pa chochitika china. Yesu ndi ophunzira ake anali pa ulendo wawo kuchokera ku Yudeya kupita ku Galileya ndipo anali atadutsa m’Samariya. Atatopa chifukwa cha ulendowo, Yesu anakhala pansi pambali pa chitsime cha Yakobo kuti apume pamene ophunzira ake anapita ku mzinda wa Sukari kukagula chakudya. Panthaŵiyi, mkazi wa Chisamariya anabwera kudzatunga madzi. Tsopano, Yesu iyemwini pa nthaŵi ina anawatcha Asamariya kukhala “a fuko lina.” (Luka 17:16-18, The Kingdom Interlinear Translation of the Greek Scriptures) Koma iye anati kwa iye: “Undipatse ine ndimwe.” Popeza Ayuda analibe chochita ndi Asamariya, mkazi wodabwitsidwayo anayankha kuti: “Bwanji inu, muli Myuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi Msamariya?”​—Yohane 4:1-9.

13. (a) Ndimotani mmene Yesu anavomerezera ku chitsutso cha mkazi wa Chisamariyayo, ndipo nchiyani chimene chinali chivomerezo chake? (b) Nchiyani chimene chinali chotulukapo chomalizira?

13 Koma Yesu ananyalanyaza chitsutso cha mkaziyo. M’malomwake, iye anaugwira mwaŵi wakupereka umboni kwa iye, ngakhale kudziŵikitsa kuti iye anali Mesiya! (Yohane 4:10-26) Mkazi wozizwitsidwayo anasiya mtsuko wake pa chitsimepo, kubwerera ku mzinda, ndi kuyamba kuuza ena zimene zachitika. Ngakhale kuti iye anali kukhala ndi moyo wamakhalidwe oipa, iye anavumbulutsa chikondwerero chake mu zinthu zauzimu mwa kunena kuti: “Ameneyu sali Kristu nanga?” Nchiyani chimene chinali chotulukapo chomalizira? Anthu ambiri akumeneko anaika chikhulupiriro mwa Yesu pa maziko a umboni wabwino woperekedwa ndi mkaziyo. (Yohane 4:27-42) Mosangalatsa, m’bukhu lake A Biblical Perspective on the Race Problem, wanthanthi yaumulungu wa Mpingo Thomas O. Figart anapanga ndemanga iyi: “Ngati Ambuye wathu analingalira icho kukhala chofunika mokwanira kukweza mwambo wa fuko loyendayenda ndi jesichala lolemekezeka, chotero tiyenera kutenga chenjezo kuti sitiri omezedwa m’mtsinje wa fuko wa lerolino.”

14. Ndi chitsimikiziro cha kupanda tsankho kwa Yehova chotani chimene chinadziwonetsera icho chokha mkati mwa utumiki wa Filipo mlengezi?

14 Kupanda tsankho kwa Yehova Mulungu kwalola kaamba ka anthu a mafuko osiyanasiyana kukhala atembenuki Achiyuda. Lingaliraninso chimene chinachitika mazana 19 apitawo pa msewu wa chipululu pakati pa Yerusalemu ndi Gaza. Mwamuna wachikuda mu utumiki wa mfumu yaikazi ya ku Aitiopiya anali kuyenda pa gareta pamene anali kuŵerenga ulosi wa Yesaya. Nduna imeneyi inali mtembenuki wodulidwa, popeza “anapita ku Yerusalemu kukapembedza.” Mngelo wa Yehova nawonekera kwa mlengezi Wachiyuda Filipo ndi kumuuza iye: “Yandikira, nudziphatike ku gareta uyu.” Kodi Filipo ananena kuti: “Oh, ayi! Iye ali munthu wafuko lina”? Kutalitali ndi chimenecho! Nkulekelanji, popeza Filipo anasangalatsidwa kulandira chiitano cha munthu wa ku Aitiopiyayo kukwera m’garetayo, kukhala ndi iye, ndi kulongosola ulosi wa Yesaya wonena za Yesu Kristu! Pamene anafika ku madzi, munthu wa ku Aitiopiyayo anafunsa: “Chindiletsa nchiyani ndisabatizidwe?” Popeza chirichonse sichinaletse ichi, Filipo mwachimwemwe anabatiza munthu wa ku Aitiopiyayo, ndipo Yehova analandira munthu wachimwemwe ameneyo monga wotsatira wodzozedwa wa Mwana wake wopanda tsankho, Yesu Kristu. (Machitidwe 8:26-39) Koma chitsimikiziro chowonjezereka cha kupanda tsankho kwaumulungu mwamsanga chinadziwonetsera icho chokha.

Kusintha Kwakukulu

15. Ndi kusintha kotani kumene kunachitika pambuyo pa imfa ya Yesu, ndipo ndimotani mmene Paulo akulongosolera ichi?

15 Imfa ya Kristu sinathetse kunyada kwa ufuko kwadziko. Koma kupyolera mwa imfa ya nsembe imeneyo, Mulungu anasintha unansi wa ophunzira Achiyuda a Yesu kwa atsatiri ake Achikunja. Mtumwi Paulo anasonyeza ichi ngakhale pamene iye analembera Akristu Achikunja ku Aefeso ndi kunena kuti: “Pitirizani kusunga m’maganizo kuti kale inu munali anthu amitundu kuthupi; . . . kuti inu pa nthaŵiyo munali opanda Kristu, opatulidwa ku mbumba ya Israyeli ndi alendo ku mapangano a lonjezo, ndipo munalibe chiyembekezo ndipo munali opanda Mulungu m’dziko. Koma tsopano m’chigwirizano ndi Kristu Yesu inu amene kale munali kutali, anakusendezani mukhale pafupi m’mwazi wa Kristu. Pakuti iye ndiye mtendere wathu, amene anachita kuti onse aŵiri akhale mmodzi, nagumula khoma lokudulitsani pakati.” “Khoma” limenelo, kapena chizindikiro cha kulekanitsa, linali makonzedwe apangano la Lamulo lomwe linagwira ntchito monga cholekanitsa pakati pa Ayuda ndi Akunja. Ilo linagumulidwa pamaziko a imfa ya Kristu kotero kuti kupyolera mwa iye ponse paŵiri Ayuda ndi Akunja angakhoze “kufikira Atate mwa mzimu umodzi.”​—Aefeso 2:11-18.

16. (a) Nchifukwa ninji Petro anapatsidwa mfungulo za Ufumu? (b) Ndi mfungulo zingati zimene zinalipo, ndipo nchiyani chimene chinatulukapo kuchokera kukugwiritsiridwa ntchito kwake?

16 M’kuwonjezerapo, mtumwi Petro anapatsidwa “mfungulo za ufumu wa kumwamba” kotero kuti anthu a mtundu uliwonse angaphunzire ponena za zifuno za Mulungu, “kubadwanso” kuchokera ku mzimu woyera, ndi kukhala olowa m’malo ndi Kristu auzimu. (Mateyu 16:19; Yohane 3:1-8) Petro anagwiritsira ntchito mfungulo zitatu zophiphiritsira. Yoyambirira inali ya Ayuda, yachiŵiri ya Asamariya, ndipo yachitatu ya Akunja. (Machitidwe 2:14-42; 8:14-17; 10:24-28, 42-48) Chotero Mulungu wopanda tsankho, Yehova, anatsegula kwa osankhidwa a mafuko onse mwaŵi wa kukhala abale auzimu a Yesu ndi olowa m’malo a Ufumu.​—Aroma 8:16, 17; 1 Petro 2:9, 10.

17. (a) Kodi ndi masomphenya achilendo otani amene Petro anapatsidwa, ndipo nchifukwa ninji? (b) Ndi kunyumba ya ndani kumene amuna ena anampereka Petro, ndipo ndi ndani amene anali kumdikirira iye kumeneko? (c) Nchiyani chimene Petro anakumbutsa Akunja amenewo, ndipo komabe nchiyani chimene Mulungu momvekera anam’phunzitsa iye?

17 Ndi cholinga chofuna kumkonzekeretsa Petro kugwiritsira ntchito mfungulo yachitatu​—kaamba ka Akunja​—iye anapatsidwa masomphenya achilendo anyama zodetsedwa ndi kuuzidwa: “Tauka Petro, ipha, nudye.” Phunziro linali lakuti: “Chimene Mulungu anachiyeretsa, musachiyese chinthu wamba.” (Machitidwe 10:9-16) Petro anadabwitsidwa koposa patanthauzo la masomphenyawo. Koma mwamsanga amuna atatu anafika kumtenga iye kupita naye kunyumba kwa Korneliyo, nduna ya gulu lankhondo la Chiroma wokhala ku Kaisareya. Popeza mzinda umenewo unali malikulu enieni a magulu ankhondo a Chiroma m’Yudeya, anali malo achibadwa kwa Korneliyo kukhala ndi nyumba yake. Akumadikirira kaamba ka Petro m’makhazikitsidwe Achikunja amenewo anali Korneliyo, limodzi ndi anansi ake ndi mabwenzi apamtima. Mtumwiyo anakumbutsa iwo kuti: “Mudziŵa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina; koma Mulungu anandiwonetsera ine ndisanenere aliyense ali munthu wamba kapena wonyansa; chifukwa chakenso ndinadza wosakana mmene munatuma kundiitana.”​—Machitidwe 10:17-29.

18. (a) Ndi chilengezo cha mwadzidzidzi chotani chimene Petro anapanga kwa Korneliyo ndi alendo ake? (b) Pambuyo pa umboni wa Petro wonena za Yesu, ndi chochitika chozizwitsa chotani chimene chinachitika? (c) Ndi sitepi lotani limene kenaka linatengedwa m’chigwirizano ndi Akunja okhulupirira amenewo?

18 Pambuyo pa kulongosola kwa Korneliyo kwa chitsogozo cha Mulungu cha nkhaniyo, Petro anati: “Zowona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankho, koma m’mitundu yonse wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:30-35) Kenaka, pamene mtumwiyo anapitiriza kupereka umboni ponena za Yesu Kristu, chinachake chodabwitsa chinachitika! “Petro ali chilankhulire, mzimu woyera unagwa pa onse akumva mawuwo.” Anzake Achiyuda a Petro, “anadabwa, chifukwa pa amitundunso panathiridwa mphatso ya mzimu woyera. Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu.” Petro anayankha: “Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira mzimu woyera ngatinso ife?” Ndani amene akanatsutsa, popeza mzimu woyera wa Mulungu wa kumwamba wopanda tsankho unali utatsanuliridwa pa Akunja okhulupirira amenewo? Chotero, Petro analamula kuti “iwo abatizidwe m’dzina la Yesu Kristu.”​—Machitidwe 10:36-48.

“Kuchokera mwa Mtundu Uliwonse”

19. Nchifukwa ninji nkhwidzi ya utundu ikuwonjezereka, ndipo ku ukulu wotani?

19 Tikudzipeza tsopano ife eni “m’masiku otsiriza,” ndipo “nthaŵi zovuta kuchita nazo” ziri zenizeni za moyo. Pakati pa zinthu zina, anthu ali odzikonda okha, odzitamandira, odzikuza, opanda chikondi chachibadidwe, osayanjanitsika, osakhoza kudziletsa, aukali, aliuma olimbirira, ndipo otukumuka mtima. (2 Timoteo 3:1-5) Mu mkhalidwe wa mayanjano woterowo, sichiri chodabwitsa kuti nkhwidzi ya ufuko ndi kuwombana zikuwonjezereka m’dziko lonse. M’maiko ambiri, anthu amafuko osiyanasiyana kapena mtundu amapeputsa kapena ngakhale kudana wina ndi mnzake. Ichi chatsogolera kukumenyana kwenikweni ndipo ngakhale nkhanza yowopsya kwambiri m’maiko ena. Ngakhale m’zitaganya zotchedwa zotukuka, anthu ambiri ali ndi mavuto m’kulaka kunyada kwa ufuko. Ndipo “nthenda” imeneyi ikuwoneka kukhala ikufalikira m’madera kumene wina sangayembekezere iyo, monga ngati m’zisumbu za m’nyanja zomwe panthaŵi ina zinawoneka za bata mu mtendere wawo.

20. (a) Ndi masomphenya ouziridwa otani amene Yohane anawona? (b) Ndi ku ukulu wotani kumene masomphenya a ulosi amenewa akukwaniritsidwira? (c) Ndi vuto lotani limene ena adakali nalo m’kulaka mokwanira, ndipo ndi kuti kumene iwo ayenera kufuna yankho?

20 Mosasamala kanthu za kusoweka kwa kugwirizana kwa ufuko m’mbali zina zadziko, ngakhale kuli tero, Mulungu wopanda tsankho, Yehova, ananeneratu za kubweretsa anthu owona mtima a mafuko onse ndi mitundu mu umodzi wotsimikizirika wa mitundu yonse. Mwakuuziridwa kwaumulungu, mtumwi Yohane anawona “gulu lalikulu, losatheka kuliŵerenga, la anthu ochokera ku mtundu uliwonse, fuko, anthu ndi manenedwe; iwo anali kuimirira kutsogolo kwa mpando wachifumu ndi kutsogolo kwa Mwana Wankhosa,” akulemekeza Yehova. (Chivumbulutso 7:9, The Jerusalem Bible) Ulosi umenewu uli kale panjira ya kukwaniritsidwa. Lerolino, m’maiko 210 mboni za Yehova zoposa 3,300,000, za mitundu yonse ndi mafuko, zikusangalala ndi umodzi ndi chigwirizano cha ufuko. Koma iwo akali opanda ungwirobe. Ngakhale ena a iwo ali ndi mavuto m’kulaka kotheratu kunyada kwa utundu, ngakhale kuti iwo angakhale osazindikira za ichi. Ndimotani mmene vuto limeneli lingalakidwire? Tidzakambitsirana nkhani imeneyi m’nkhani yotsatira, yozikidwa pa uphungu wathandizo wochokera m’Mawu ouziridwa a Mulungu wopanda tsankho, Yehova.

Kodi Mukayankha Motani?

◻ Nchifukwa ninji munganene kuti Yehova sanali watsankho m’kugwiritsira ntchito Aisrayeli?

◻ Ndi umboni wotani umene ulipo wakuti Yesu Kristu sanali wonyada mwaufuko kapena watsankho?

◻ Ndimotani mmene Petro anathandizidwira kuwona kuti “Mulungu sali watsankho”?

◻ Mosasamala kanthu za kusoweka kwa chigwirizano cha ufuko m’dziko iri, ndi ulosi wotani wosonyeza umodzi umene ukukwaniritsidwa tsopano?

[Chithunzi patsamba 10]

Mtumwi Paulo anauza anthu a ku Atene kuti Mulungu “analenga fuko lirilonse la anthu kukhala pa nkhope yonse ya dziko lapansi”

[Chithunzi patsamba 12]

Chifukwa chakuti Yesu anali wopanda tsankho, iye anachitira umboni kwa mkazi wa Chisamariya pa chitsime cha Yakobo pafupi ndi Sukari

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena