Mboni Zachangu za Yehova Pakuguba!
MBONI za Yehova za m’zaka za zana loyamba zinali anthu olimba mtima ndi a machitidwe achangu. Iwo mofunitsitsa anapitiriza ndi gawo la ntchito la Yesu lakuti: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse.”—Mateyu 28:19, 20.
Koma kodi timadziŵa bwanji kuti otsatira oyambirira a Kristu analandira gawolo mwamphamvu? Eya, bukhu la Baibulo la Machitidwe a Atumwi limapereka umboni wakuti iwo anali mboni zachangu za Yehova, zokhaladi pakuguba!
MAPINDU NDI MBALI ZINA
Kufanana kwa chinenero ndi mpangidwe pakati pa bukhu lachitatu la Uthenga Wabwino ndi bukhu la Machitidwe kumasonyeza mlembi mmodzimodziyo—Luka, “sing’anga wokondedwa.” (Akolose 4:14) Pakati pa mbali zake zapadera pali kulankhulana ndi mapemphero zosungidwa m’Machitidwe. Pafupifupi 20 peresenti ya bukhulo imapanga makambitsirano, onga ngati ochitidwa ndi Petro ndi Paulo pochirikiza chikhulupiriro chowona.
Bukhu la Machitidwe linalembedwera mu Roma pafupifupi 61 C.E. Mwachiwonekere ndicho chifukwa chake silimatchula kuwonekera kwa Paulo pamaso pa Kaisara kapena pachizunzo chimene Nero anachita motsutsana ndi Akristu pafupifupi 64 C.E.—2 Timoteo 4:11.
Mofanana ndi Uthenga Wabwino wa Luka, bukhu la Machitidwe linalunjikitsidwa kwa Teofilo. Iro linalembedwera kulimbikitsa chikhulupiriro ndi kusimba za kufalikira kwa Chikristu. (Luka 1:1-4; Machitidwe 1:1, 2) Bukhulo limapereka umboni wakuti dzanja la Yehova linali ndi atumiki ake okhulupirika. Limatidziŵitsa za mphamvu ya mzimu wake ndi kulimbitsa chidaliro chathu muulosi wouziridwa mwaumulungu. Bukhu la Machitidwe limatithandizanso kupirira chizunzo, limatisonkhezera kukhala Mboni za Yehova zodzimana, ndipo limalimbikitsa chikhulupiriro chathu m’chiyembekezo cha Ufumu.
KULONDOLA KWA M’MBIRI
Monga bwenzi la Paulo, Luka analemba maulendo awo. Iye analankhulanso ndi mboni zowona ndi maso. Magwero amenewa ndi kufufuza kosamalitsa zimapangitsa zolemba zake kukhala zolondola ponena za kulondola kwa m’mbiri.
Motero katswiri William Ramsay ankakhoza kunena kuti: “Luka ali wolemba mbiri wodziŵa koposa: sikokha kuti ndemanga zake zotsimikizirika ziri zowona, iye ali ndi chidziŵitso chowona cha kulemba mbiri . . . Wolemba ameneyu ayenera kundandalikidwa limodzi ndi akatswiri ena olemba mbiri otchuka kwambiri.”
PETRO—MBONI YOKHULUPIRIKA
Ntchito yopatsidwa ndi Mulungu yolengeza mbiri yabwino ingachitidwe kokha ndi mphamvu ya mzimu woyera wa Yehova. Motero, pamene otsatira a Yesu alandira mzimu woyera, iwo adzakhala mboni zake m’Yerusalemu, Yudeya, ndi Samariya ndi “kumalekezero adziko lapansi.” Pa Pentekoste wa 33 C.E., iwo adzazidwa ndi mzimu woyera. Popeza kuti idakali kokha 9:00 mmaŵa, ndithudi iwo saali oledzera, monga mmene ena akuganizirira. Petro akupereka umboni wochititsa chidwi, ndipo 3,000 akubatizidwa. Otsutsa chipembedzo akuyesa kutontholetsa olengeza Ufumuwo, koma poyankha pemphero, Mulungu akutheketsa mboni zake kulankhula mawu ake molimba mtima. Atawopsezedwanso, iwo akuyankha kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira koposa anthu.” Ntchitoyo ikupitirizabe pamene akumkabe nalalikira kunyumba ndi nyumba.—1:1–5:42.
Kudalira pa mzimu wa Yehova kumatheketsa mboni zake kupilira chizunzo. Motero, pambuyo pakuphedwa mwa kuponyedwa miyala kwa mboni yokhulupirika Stefano, otsatira a Yesu amwazikana, koma zimenezi zikungofalitsa mawuwo. Mlaliki Filipo akuyamba kuloŵa m’Samariya. Modabwitsa, Saulo wa ku Tariso wozunza wachiwawa atembenuzidwa. Monga mtumwi Paulo, iye akuvutika ndi chizunzo chankhanza m’Damasiko koma akupulumuka machenjera a Ayuda ofuna kumupha. Kwakanthaŵi kochepa, Paulo akusonkhana ndi atumwi mu Yerusalemu ndiyeno akupitirizabe ndi utumiki wake.—6:1–9:31.
Dzanja la Yehova liri ndi mboni zake, monga mmene bukhu la Machitidwe likupitirizira kusonyeza. Petro akuukitsa Dorika (Tabita) kuchokera kwa akufa. Poyankha ku chiitanocho, iye akulengeza mbiri yabwino kwa Korneriyo mu Kaisareya, kubanja lake, ndi mabwenzi ake. Iwo akubatizidwa monga Akunja oyambirira kukhala ophunzira a Yesu. Motero “masabata makumi asanu ndi aŵiri” akutha, akumatifikitsa ku 36 C.E. (Danieli 9:24) Mwamsanga pambuyo pake, Herode Agrippa I akupha mtumwi Yakobo ndi kuchititsa Petro kumangidwa. Koma mtumwiyo akupulumutsidwa ndi mngelo kuchokera m’ndende, ndipo ‘mawu a Yehova apitirizabe kukula ndi kufalikira.’—9:32–12:25.
MAULENDO ATATU A PAULO AUMISHONALE
Madalitso akumka kwa odzipereka muutumiki wa Mulungu, monga mmene Paulo anachitira. Ulendo wake woyamba waumishonale ukuyambira pa Antiokeya, Suriya. Pachisumbu cha Kupro, mkulu wa gulu lankhondo Sergio Paulo ndi ena ambiri akukhulupirira. Pa Perge mu Pamfuliya, Yohane Marko akuchoka kumka ku Yerusalemu, koma Paulo ndi Barnaba akupitirizabe ndi ulendo wawo kufikira ku Antiokeya mu Pisidiya. Mu Lustra, Ayuda akuyamba chizunzo. Ngakhale kuti waponyedwa miyala ndikusiidwa kuti afe, Paulo akuchira ndi kupitirizabe muutumikiwo. Pomalizira pake, iye ndi Barnaba akubwerera ku Antiokeya mu Suriya, akumamaliza ulendo woyamba.—13:1–14:28.
Mofanana ndi mnzake wa m’zaka za zana loyamba, Bungwe Lolamulira lamakano limayankha mafunso motsogozedwa ndi mzimu woyera. Mdulidwe sunali pakati pa “izi zoyenerazi,” zimene zimaphatikizapo “kusala nsembe zamafano, ndi mwazi ndi zopotola, ndi dama.” (15:28, 29) Pamene Paulo akuyamba ulendo wachiŵiri, Sila akutsagana naye ndipo pambuyo pake Timoteo akumkera nawo limodzi. Kachitidwe kofulumira kakutsatira chiitano cha kuwolokera ku Makedoniya. Mu Filipi, kuchitira umboni kukuchititsa phokoso ndi kuponyedwa m’ndende. Koma Paulo ndi Sila akumasulidwa ndi chivomezi ndipo akulalikira kwa mdindo ndi banja lake, ndipo aŵa akukhala okhulupirira obatizidwa.—15:1–16:40.
Atumiki a Yehova ayenera kukhala ophunzira akhama a Mawu ake, mofanana ndi Paulo ndi Abereya osanthula Malemba. Pa Areopagi mu Atene, iye akupereka umboni wonena zakuti Yehova ndiye mlengi, ndipo ena akukhala okhulupirira. Chikondwerero chachikulu chikusonyezedwa m’Korinto kotero kuti iye akukhalabe mumzindawo kwa miyezi 18. Ali konko, iye akulemba Atesalonika Woyamba ndi Wachiŵiri. Polekana ndi Sila ndi Timoteo, mtumwiyo akupita ulendo wapanyanja kumka ku Efeso, kenaka akumka ku Kaisareya, ndikupitirira kumka ku Yerusalemu. Pamene akubwerera ku Antiokeya wa Suriya, ulendo wake wachiŵiri waumishonale watha.—17:1–18:22.
Monga mmene Paulo anasonyezera, kuchitira umboni kwa kunyumba ndi nyumba ndiko mbali yofunika kwambiri ya utumiki Wachikristu. Ulendo wachitatu wa mtumwiyu (52-56 C.E.) kwakukulukulu ngwobwerera mmene anayenda muulendo wake wachiŵiri. Utumiki wa Paulo ukudzutsa chitsutso pa Efeso, kumene akulembera Akorinto Woyamba. Akorinto Wachiŵiri akulembedwera mu Makedoniya, ndipo akulembera Aroma ali m’Korinto. Pa Mileto, Paulo akukumana ndi akulu a ku Efeso ndikuwasimbira mmene anawaphunzitsira poyera ndi kunyumba ndi nyumba. Ulendo wake wachitatu utha pamene afika mu Yerusalemu.—18:23–21:14.
CHIZUNZO CHILEPHERA
Chizunzo sichimatseka milomo ya mboni zokhulupirika za Yehova. Motero pamene chiwawa chachipwirikiti chiulika motsutsana ndi Paulo pa kachisi mu Yerusalemu, iye akuchitira umboni molimba mtima kwa oukira okwiyawo. Chiwembu cha kumupha chikulepheretsedwa pamene iye akutengeredwa kwa Bwanamkubwa Felike ku Kaisareya ndi msilikali wolonda. Paulo akusungidwira m’nsinga kwa zaka ziŵiri pamene Felike akumsunga kufunafuna chiphuphu chimene sanalandire. Woloŵa mmalo wake, Festo, akumva za apilo ya Paulo kumka kwa Kaisara. Komabe, asanayambe ulendo womka ku Roma, mtumwiyo akudzitetezera mwamphamvu pamaso pa Mfumu Agripa.—21:15–26:32.
Mosafooketsedwa ndi ziyeso, atumiki a Yehova akupitirizabe kulalikira. Ndithudi izi zinalidi choncho ndi Paulo. Chifukwa cha kuchita kwake apilo kwa Kaisara, mtumwiyo akuyamba ulendo wopita ku Roma limodzi ndi Luka pafupifupi 58 C.E. Pa Mura wa Lukiya, iwo akusinthira m’ngalaŵa ina. Ngakhale kuti akuswekeredwa ndi ngalaŵayo ndi kukaima pa chisumbu cha Mileto, pambuyo pake ngalaŵa ina ikuŵatengera ku Italiya. Ngakhale ali ndi msilikali wolonda mu Roma, Paulo akuitana anthu ndi kulengeza mbiri yabwino kwa iwo. Mkati mwa kumangidwa kumeneku, iye akulembera Aefeso, Afilipi, Akolose, Filemoni, ndi Ahebri.—27:1–28:31.
NTHAŴI ZONSE PAKUGUBA
Bukhu la Machitidwe limasonyeza kuti ntchito yoyambidwa ndi Mwana wa Mulungu inapitirizidwa mokhulupirika ndi mboni za Yehova za m’zaka za zana loyamba. Inde, mwamphamvu ya mzimu woyera wa Mulungu, iwo anachitira umboni mwachangu.
Chifukwa chakuti otsatira oyambirira a Yesu anadalira mwapemphero pa Mulungu, dzanja Lake linali nawo. Motero zikwi zambiri zinakhala okhulupirira, ndipo ‘mbiri yabwino inalalikidwa m’chilengedwe chonse chokhala pansi pathambo.’ (Akolose 1:23) Ndithudi, ponse paŵiri kalelo ndi tsopano, Akristu owona atsimikizira kukhala mboni zachangu za Yehova pakuguba!
[Bokosi/Chithunzi patsamba 25]
KENTURIYO KORNELIYO: Korneliyo anali nduna ya gulu lankhondo, kapena kenturiyo. (10:1) Malipiro a pachaka a kenturiyo anali pafupifupi kuwirikiza nthaŵi zisanu kuposa a msilikali wamba, kapena madenari okwanira 1,200, koma akakhoza kukhala oposa pamenepo. Ataleka kugwira ntchito, iye adalandira mphatso zandalama kapena munda. Zovala zake zausilikali zinali zokongola, kuyambira pa chisoti chasiliva kufikira pa malaya onga siketi, chibakuwa chaubweya, ndi zotetezera zokongola. Kwanenedwa kuti gulu la ankhondo la kenturiyo linali ndi amuna 100, koma panthaŵi zina anali 80 okha kapena cha pompo. Olembedwa ntchito a “m’gulu la ankhondo la Italiya” mwachiwonekere anali nzika za Roma ndi amuna aufulu mu Italiya.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 25]
PEMPHERO PATSINDWI: Petro sankadziwonetsera pamene anapemphera ali yekha patsindwipo. (10:9) Kampanda kozungulira denga losalalalo mwachiwonekere kanambisa kuti asawoneke. (Deuteronomo 22:8) Tsindwi linalinso malo opumirapo ndi othawira phokoso la m’khwalala m’nthaŵi yamadzulo.
[Bokosi patsamba 25]
YOLINGALIRIDWA KUKHALA MILUNGU MUMPANGIDWE WA ANTHU: Kuchiritsa mwamuna wopunduka kwa Paulo kunachititsa nzika za m’Lustra kuganiza kuti milungu inali itawonekera ngati anthu. (14:8-18) Zeu, mulungu wamkulu wa Agiriki, anali ndi kachisi mumzinda umenewo, ndipo mwana wake wamwamuna Herme, mthenga wa milunguyo, anali womveka ndikulankhula kwa myaa. Popeza kuti anthu anaganiza kuti Paulo anali Herme chifukwa chakuti anatsogolera m’kulankhula, iwo analingalira Barnaba kukhala Zeu. Unali mwambo kuveka mafano a milungu yonyenga nkhata ya maluŵa kapena masamba a naphini kapena mkungudza, koma Paulo ndi Barnaba anakana kuchitiridwa kwakulambiridwa koteroko.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 25]
MDINDO AKHULUPIRIRA: Pamene chivomezi chinatsegula makomo andende nichimasula maunyolo a akaidi, mdindo wosunga ndende wa ku Filipi anafuna kudzipha. (16:25-27) Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti lamulo Lachiroma linalamulira kuti wosunga ndende akafunikira kupatsidwa chilango cha othaŵa m’ndende. Mwachiwonekere mdindo wosunga ndendeyo anasankha kudzipha mmalo mwa imfa yozunzidwa, imene mwinamwake inali kuyembekezera ena a m’ndendemo. Komabe, iye anavomereza mbiri yabwino, ndipo “iye ndi abanja lake anabatizidwa mosazengeleza.”—16:28-34.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 26]
APILO KWA KAISARA: Monga nzika yobadwira m’Roma, Paulo anali ndi kuyenera kwa kuchita apilo kwa Kaisara ndi kukazengedwera mlandu m’Roma. (25:10-12) Nzika ya Roma siinayenere kumangidwa unyolo, kukwapulidwa, kapena kupatsidwa chilango popanda kuzengedwa mlandu.—16:35-40; 22:22-29; 26:32.
[Mawu a Chithunzi]
Musei Capitolini, Roma
[Bokosi/Chithunzi patsamba 26]
WOSUNGA KACHISI WA ARTEMI: Atakwiyitsidwa ndi kulalikira kwa Paulo, Demetrio wosula siliva anasonkhezera chipolowe. Koma mlembi wa mumzinda wa Filipi anatontholetsa khamulo. (19:23-41) Osula siliva anapanga tiakachisi tasiliva tating’ono tammbali yopatulikitsa koposa ya kachisi mmene fano loumba la Atermi la nakubala wa maere ambiri linali. Mizinda inkapikisana n’cholinga chofuna ulemu wa kukhala ne·o·koʹros wake, kapena “wosunga kachisi.”
[Bokosi/Chithunzi patsamba 26]
MAVUTO PANYANJA: Pamene ngalaŵa imene Paulo anakweramo inaswedwa ndi mphepo ya mkuntho yotchedwa Euroaquilo, iwo sanali ‘okhoza kulamulira bwato, konse.’ (27:15, 16) Bwatolo linali mwadiya yapamadzi yaing’ono imene kaŵirikaŵiri inkakokedwa ndi lalikululo. Ngalaŵayo inali ndi zingwe zimene zinazengedwa zolimba cha kunsi kwake kuitetezera kugubuduzika kochititsidwa ndi kugwedera kwa mlongoti wa ngalaŵa m’nthaŵi ya namondwe. (27:17) Amalinyero amenewa anaponya anangula anayi ndipo anamasula zingwe zomangira tsigiro, kapena zopalasira, zogwiritsidwa ntchito kuwongolera ngalaŵayo. (27:29, 40) Ngalaŵa ya Alesandriyo inali ndi fano loumbidwa lotchedwa “Ana a Zeu”—Castor ndi Pollux, olingaliridwa kukhala mbuye wa amalinyero.—28:11.