Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 | Muziyesetsa Kupewa Tsankho
    Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2022 | Na. 1
    • Baibulo Limati:

      “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”​—MACHITIDWE 10:34, 35.

      Zimene Lembali Limatanthauza:

      Yehovaa Mulungu samatiweruza potengera mtundu wathu, mmene khungu lathu limaonekera kapenanso chikhalidwe chathu. Mulungu amaona zinthu zofunika kwambiri monga zomwe timaganiza komanso zimene timalakalaka mumtima mwathu. Baibulo limanenanso kuti munthu amaona zooneka ndi maso “koma Yehova amaona mmene mtima ulili.”​—1 Samueli 16:7.

  • 1 | Muziyesetsa Kupewa Tsankho
    Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2022 | Na. 1
    • Poyamba Titus ankavutika kuthetsa chidani mumtima mwake. Iye anati: “Zinali zovuta kuti ndisinthe mmene ndimaganizira ndiponso khalidwe langa.” Koma lemba la Machitidwe 10:34, 35, linamuthandiza kuzindikira kuti Mulungu alibe tsankho.

      Ndiye zotsatirapo zake zinali zotani? Titus anafotokoza kuti: “Ndinakhulupirira kuti Mboni za Yehova zimalambira Mulungu moona nditaona kuti zimakondana mosayang’ana mtundu kapena khungu la munthu. Ndipo ngakhale ndisanabatizidwe munthu wina wa Mboni yemwe anali mzungu anandiitanira kunyumba kwake kuti ndikadye naye chakudya. Sindinakhulupirire zimenezi chifukwa ndinali ndisanakhalepo mwamtendere ndi mzungu ndipo sizikanatheka n’komwe kudya naye pamodzi. Tsopano zinali zotheka chifukwa ndili m’gulu la anthu okondana kwambiri lapadziko lonse.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena