Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Baibulo Ndi Buku Lochokera kwa Mulungu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 6. Buku la anthu onse

      Baibulo ndi buku limene lamasuliridwa komanso kufalitsidwa kwambiri kuposa buku lina lililonse. Werengani Machitidwe 10:34, 35, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

      • N’chifukwa chiyani Mulungu amafuna kuti Mawu ake amasuliridwe ndi kufalitsidwa m’zinenero zambiri?

      • Kodi ndi zinthu ziti zokhudza Baibulo zimene zimakusangalatsani?

      Anthu amitundu yosiyanasiyana komanso ochokera m’mayiko osiyanasiyana akuwerenga Baibulo m’zinenero zawo.

      Pafupifupi

      munthu aliyense

      padzikoli

      akhoza kupeza Baibulo m’chinenero chimene amamva

      Baibulo likupezeka m’zinenero zoposa

      3,000

      lathunthu kapena mbali zake zina

      Mabaibulo

      5,000,000,000

      afalitsidwa

      ndipo nambala imeneyi ikuposa buku lina lililonse

  • Yehova Akhoza Kukhala Mnzanu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 3. Kodi Yehova amafuna kuti anzake azichita chiyani?

      N’zoona kuti Yehova amakonda anthu onse, koma amakonda kwambiri “anthu owongoka mtima.” (Miyambo 3:32) Yehova amafuna kuti anzake aziyesetsa kuchita zinthu zimene iye amaziona kuti ndi zabwino, n’kumapewa zinthu zimene iye amaziona kuti ndi zoipa. Anthu ena amaona kuti sangakwanitse kuchita zinthu zonse zimene Yehova amafuna komanso kupeweratu zoipa zonse. Koma Yehova ndi Mulungu wachifundo. Iye amalandira aliyense amene amamukonda ndi mtima wonse ndiponso amene amayesetsa kuchita zinthu zomusangalatsa.​—Salimo 147:11; Machitidwe 10:34, 35.

  • Pitirizani Kuchita Zinthu Mogwirizana Mumpingo
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 4. Yesetsani kuthetsa mtima watsankho

      Tonsefe timafuna kumakonda abale ndi alongo athu onse. Komabe tingavutike kugwirizana ndi munthu yemwe amaoneka wosiyana ndi ife. Ndiye n’chiyani chimene chingatithandize? Werengani Machitidwe 10:​34, 35, kenako mukambirane mafunso awa:

      • Yehova amalandira anthu amitundu yonse kuti akhale Mboni zake. Ndiye kodi mungatengere bwanji chitsanzo cha Yehova pa nkhani ya mmene mumaonera anthu omwe ndi osiyana ndi inu?

      • Kodi inuyo mukufuna kupewa zinthu ziti zomwe anthu ambiri m’dera lanu amachita posonyeza tsankho?

      Werengani 2 Akorinto 6:​11-13, kenako mukambirane funso ili:

      • Kodi mukuganiza kuti muyenera kuchita chiyani kuti muzikonda kwambiri abale ndi alongo omwe mumasiyana nawo zinthu zina?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena