Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 5/1 tsamba 15-20
  • Anthu Oyenda m’Mapazi a Yesu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anthu Oyenda m’Mapazi a Yesu
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupatulika kwa Mwazi
  • Makhalidwe Abwino
  • Uchete
  • M’nyumba
  • Omvera Chifukwa cha Chikondi
  • Chitokoso cha Kutsatira m’Mapazi Ake
    Nsanja ya Olonda—1988
  • “Muzitsatira Mapazi Ake Mosamala Kwambiri”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Kulemekeza Moyo ndi Mwazi Mwaumulungu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kuyenda ndi Mulungu—Masitepe Oyambirira
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 5/1 tsamba 15-20

Anthu Oyenda m’Mapazi a Yesu

“Tinayenda mu mzimu womwewo, kodi sitinatero? M’mapazi omwewo, kodi sitinatero?”​—2 AKORINTO 12:18, NW.

1. Nchifukwa ninji kaŵirikaŵiri chiri chosavuta kuzindikira mmodzi wa Mboni za Yehova?

“MONGA gulu, ali aulemu, okhala ndi thayo, ndipo amachita bwino mu sukulu. Ichi sichinganenedwe ponena za magulu ena.” Anatero wamkulu pa sukulu loyambirira mu United States. Kodi iye ankalankhula ponena za ndani? Ana a Mboni za Yehova omwe anali ophunzira pa sukulu yake. Ndithudi, ambiri azindikira kuti Mboni za Yehova, kuphatikizapo ana awo kaŵirikaŵiri amalingana ndi Mboni zina m’njira zina. Mkati mwa zaka chakhala chowonekera mowonjezereka kuti iwo ali ogwirizana mwapadera ponena za chikhulupiriro ndi makhalidwe. Chotero Mboni siziri zovuta kuzizindikira.

2. Kodi nchiyani chimene chinali mkhalidwe wa chizindikiritso wa mpingo Wachikristu woyambirira, ndipo kodi nchiyani chimene Paulo ananena ponena za chimenechi?

2 Chigwirizano cha Mboni za Yehova chiri chinachake chosakhala cha nthaŵi zonse m’dziko iri losagwirizana. Koma sichiri chovuta kumvetsetsa ngati tikumbukira kuti onse a iwo akukalamira kuyenda m’mapazi a Yesu. (1 Petro 2:21) Chigwirizano choterocho chinalinso chizindikiritso cha Akristu a m’zana loyamba. Pa chochitika chimodzi, Paulo analangiza mpingo mu Korinto: “Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m’chiweruzo chomwecho.” (1 Akorinto 1:10) Paulo anaperekanso uphungu wouziridwa wonena za mmene angachitire ndi anthu osafunitsitsa kusungilira chigwirizano Chachikristu.​—Onani Aroma 16:17; 2 Atesalonika 3:6.

3, 4. Ndimotani mmene Paulo analongosolera chigwirizano pakati pa iyemwini ndi Tito, ndipo kodi nchiyani chimene chinali maziko kaamba ka chigwirizano chimenechi?

3 Chifupifupi chaka cha 55 C.E., Paulo anatumiza Tito ku Korinto kukathandiza m’kupanga kusonkhanitsa kaamba ka abale osowa m’Yudeya ndipo mothekera kuti awone mmene mpingo unkayankhira ku uphungu wa Paulo. Pamene pambuyo pake ankalembera ku Korinto, Paulo analozera kuchezera kwaposachedwa kwa Tito ndi kufunsa kuti: “Kodi Tito anakuchenjererani kanthu? Tinayenda mu mzimu womwewo, kodi sitinatero? M’mapazi omwewo, kodi sitinatero?” (2 Akorinto 12:18, NW) Kodi nchiyani chimene Paulo anatanthauza mwa kuyenda kwawo “mu mzimu womwewo” ndi “m’mapazi omwewo”?

4 Iye ankalongosola chigwirizano chomwe chinalipo pakati pa iye ndi Tito. Tito anali mnzake wa Paulo woyenda naye wa pa kanthaŵi, ndipo iye mosakaikira anaphunzira zochulukira kuchokera kwa Paulo m’njirayi. Koma chigwirizano chomwe chinalipo pakati pa aŵiriwo chinazikidwa pa chinachake cholimba kwambiri kuposa chimenecho. Icho chinazikidwa pa unansi wawo wabwino ndi Yehova ndi pa chenicheni chakuti onse aŵiri ankatsatira mapazi a Kristu. Tito anatsanzira Paulo monga mmene Paulo anatsanzira Kristu. (Luka 6:40; 1 Akorinto 11:1) Chotero chinali mu mzimu wa Yesu ndi m’mapazi ake mmene iwo ankayenda.

5. Kodi nchiyani chimene chingayembekezeredwe kwa anthu lerolino omwe amatsanzira Paulo ndi Tito pamene akuyenda “mumzimu womwewo” ndi “m’mapazi omwewo”?

5 Sichiri chodabwitsa, kenaka, kuti Akristu a m’zana la 20 lino, omwe akuyenda “mu mzimu wofananawo” ndi “mapazi ofananawo” monga Paulo ndi Tito, akusangalala ndi chigwirizano chosagwedezeka. M’chenicheni, kusagwirizana kwa Akristu opanda pake kumawapereka iwo kukhala Akristu onyenga, osayenda m’mapazi a Mtsogoleri yemwe akudzinenera kukhala akumtsatira. (Luka 11:17) Kusiyana kodabwitsa kumeneku pakati pa Akristu owona ndi abodza kungachitiridwe chitsanzo m’njira zosiyanasiyana. Tiyeni titchule zinayi.

Kupatulika kwa Mwazi

6, 7. (a) Kodi ndi kawonedwe koyenera kotani ka mwazi komwe kakuphatikizidwa m’kuyenda m’mapazi a Yesu? (b) Kodi ndi kusiyana kotani pakati pa Mboni za Yehova ndi ena lerolino omwe amakana kuthiridwa mwazi?

6 Chifupifupi chaka cha 49 C.E., bungwe lolamulira la mpingo wa m’zana loyamba linatumiza kalata yomwe inayankha funso lakuti: Kodi Akristu Achiyuda safunikira kulabadira Lamulo la Mose? Kalatayo inanena ichi: “Pakuti chinakomera mzimu woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenererazi; kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama.” (Machitidwe 15:28, 29) Dziŵani kuti pakati pa “zinthu zoyenera” panali kupewa mwazi. Kuyenda m’mapazi a Yesu kukatanthauza kusaika mwazi m’thupi kapena pakamwa kapena mwanjira ina iriyonse.

7 Lamulo limeneli laswedwa mowopsya m’Chikristu cha Dziko mwa kachitidwe ka kuthira mwazi. Ndi zowona, m’zaka zaposachedwapa chiŵerengero cha anthu akhala ogalamuka ponena za ngozi ya umoyo wa kuthiridwa mwazi ndipo akana iko kaamba ka malingaliro a za mankhwala. Ichi chiri chowona mwapadera popeza kuti ambiri ayambukiridwa ndi AIDS chifukwa cha kuthiridwa mwazi. Koma kodi ndani yemwe amasamalira kupatulika kwa mwazi chifukwa cha ulemu kaamba ka lamulo la Mulungu, akumachita tero monga gulu? Pamene wodwala akana kuthiridwa mwazi, kodi ndani yemwe dokotala mwamsanga amamlingalira iye kukhala? Kodi dokotala nthaŵi zambiri samanena kuti: ‘Ufunikira kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova’?

8. Kodi ndimotani mmene Mboni ina mu Italy inadalitsidwira kaamba ka kugamulapo kwake kusunga malamulo a Mulungu m’nkhaniyi?

8 Antonietta amakhala ku Italy. Chifupifupi zaka zisanu ndi zitatu zapitazo iye anali wodwala kwambiri, ndipo unyinji wa mwazi wake unali wochepera kotero kuti adokotala anakakamiza kuti kuthiridwa mwazi kunkafunidwa kuti apulumutse moyo wake. Iye anakana ndipo anatsutsidwa ndi adokotala aŵiri onsewo ndi achibale. Ngakhale anyamata ake achichepere aŵiri anadandaula kuti: “Amayi, ngati inu ndithudi mumatikonda ife, landirani mwazi.” Koma Antonietta anali wogamulapo kukhala wokhulupirika, ndipo mwachimwemwe iye sanafe. Chikhalirechobe, mkhalidwe wake unali woipirako kotero kuti dokotala ananena kuti: “Sitingalongosole chifukwa chimene iye akali wamoyo.” Koma mwamsanga pamene kapatsidwe ka mankhwala kosakaikiritsa kanayambika, iye anapanga kupita patsogolo kofulumira chakuti dokotala wina analongosola kuti: “Sindingakhoze kukhulupirira icho​—iwe sukanakhoza kuchira m’nthaŵi yochepa chotero, osati ngakhale ngati tikanathira mwazi mwa iwe tsiku lonse lathunthu.” Pakali pano, iye ali mpainiya wokhazikika, ndipo ana ake a amuna aŵiri, omwe ali a zaka 12 ndi 14 tsopano, akupanga kupita patsogolo kwabwino m’chowonadi. Antonietta molimbika anasunga ‘chinthu choyenera’ chimenecho, kupatulika kwa mwazi. Onse a Mboni za Yehova amasunga kawonedwe kofananako pamene akuyenda m’mapazi a Yesu.

Makhalidwe Abwino

9. Kodi ndi ‘chinthu choyenerera’ china chiti chomwe chikuphatikizidwa m’kutsatira m’mapazi a Yesu, ndipo kodi nchiyani chimene chimachitika kwa awo omwe amalephera kutsatira chimenechi?

9 ‘Chinthu china choyenera’ chowunikiridwa m’kalata imeneyo kuchokera ku bungwe lolamulira la m’zana loyamba chinali “kusala . . . dama.” M’kalata yake yoyamba ku Korinto, Paulo anakulitsa pa chimenechi, akumanena kuti: “Adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsya ndi amuna, . . . sadzalowa ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Akristu amathandiza anthu omwe amakhumba kutumikira Yehova kuchotsa kwa iwo eni machitachita oipa amenewa. Ngakhale ziwalo za mpingo zomwe zimaikidwa mu ukapolo ndi izo zimathandizidwa kudziyeretsa izo zeni ngati zitembenuka ndi kulapa. (Yakobo 5:13-15) Koma ngati Mkristu aliyense agwera m’kachitidwe koipa koteroko ndi kukana kulapa, lamulo la Baibulo lolunjika limagwira ntchito. Paulo anauziridwa mwaumulungu kunena kuti: “Musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wadama, . . . Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.”​—1 Akorinto 5:11, 13.

10, 11. (a) Kodi ndani amene ayenera kukhala ndi thayo kaamba ka miyezo ya makhalidwe otsika m’Chikristu cha Dziko, ndipo nchifukwa ninji? (b) Kodi ndimotani mmene chokumana nacho cha munthu wina mu Philippines chimachitira chitsanzo kuti, monga gulu, Mboni za Yehova zimasungilira miyezo ya makhalidwe abwino apamwamba?

10 Mosasamala kanthu za kuphunzitsa komvekera bwino kumeneku, Chikristu cha Dziko chadzazidwa ndi chisembwere. Atsogoleri a chipembedzo omwe amanyalanyaza miyezo yaumulungu ali aliwongo kaamba ka mkhalidwewu, monga mmene aliri awo omwe amapereka utumiki wa pakamwa ku miyezo ya Baibulo koma amalephera kuichirikiza iyo molimbika m’mipingo yawo. Mosasamala kanthu za chimenecho, mu ichi, nazonso, Mboni za Yehova monga anthu zimayenda m’mapazi a Yesu.

11 Lingalirani Jose, kuchokera ku Philippines. Pa zaka 17 iye anadziŵika kale monga wopanga mavuto ndi wochova juga. Iye kaŵirikaŵiri anali woledzera, ankakhala ndi moyo wamakhalidwe oipa, ndipo kaŵirikaŵiri ankapezeka m’ndende kaamba ka kuba. Kenaka iye anakumana ndi Mboni za Yehova. “Phunziro la Baibulo linasintha kotheratu moyo wanga,” iye akutero. “Sindikumwanso ndi kusuta, ndipo ndaphunzira kulamulira mkwiyo wanga. Ndiri ndi chikumbumtima changwiro tsopano, pokhala ndi mkazi mmodzi yekha. Ndapezanso ulemu kwa anansi anga, omwe ankanditcha ine ‘Jose, munthu wovuta’ ndi ‘Jose mzukwa.’ Tsopano iwo akunditcha ine ‘Jose, Mboni ya Yehova.’ Mwana wanga wamwamuna ndi mphwanga ali atumiki otumikira mu mpingo womwe pakali pano ndikutumikira monga mkulu ndi mpainiya wokhazikika.” Jose ndi mamiliyoni a mboni za Chikristu za Yehova amayenda m’mapazi a Yesu monga Akristu oyera m’makhalidwe.

Uchete

12. Kodi ndi mkhalidwe wotani wa Akristu enieni umene Yesu anawunikira m’pemphero lake lolembedwa pa Yohane mutu 17?

12 M’pemphero lalitali limene Yesu anapereka pa madzulo otsirizira pamene anali ndi ophunzira ake, iye anatchula njira ina imene atsatiri ake ‘akayendera m’mapazi ake.’ Akulankhula ponena za ophunzira ake, iye ananena kuti: “Siali mbali ya dziko, monganso ine sindiri mbali ya dziko.” (Yohane 17:16) Ichi chimatanthauza kuti Akristu ali achete. M’malo mwakutenga mbali m’ndale zadziko kapena kukanthana kwa utundu, iwo amauza ena ponena za Ufumu wa Mulungu, yankho lokha ku mavuto a dziko lino.​—Mateyu 6:9, 10; Yohane 18:36.

13, 14. (a) Ndimotani mmene Chikristu cha Dziko chimasiirana ndi Mboni za Yehova m’nkhani ya uchete? (b) Ndimotani mmene kusungirira uchete wa ndale zadziko kumbali ya Mboni mu Japan kunagwirira ntchito ku phindu la ubale wonse?

13 Lamulo limeneli la uchete laiwalidwa ndi ziwalo zambiri za Chikristu cha Dziko, kwa amene chiyambi cha utundu chiri kaŵirikaŵiri chofunika kwambiri kuposa kuyanjana kwa chipembedzo. Wolemba m’danga la nyuzipepala Mike Royko akuloza kuti “Akristu” sanakhoze ndi kalelonse “kuipidwa ponena za kumenya nkhondo pa Akristu ena,” akumawonjezera kuti: “Ngati iwo anatero, zambiri za nkhondo za umoyo mu Europe sizikanachitika.” Kunena kuti Mboni za Yehova zimasunga uchete Wachikristu mosamalitsa m’nthaŵi za nkhondo iri nsonga yodziŵika bwino lomwe. Koma monga otsatira mapazi a Yesu, iwo alinso a uchete pankhani za mayanjano ndi ndale zadziko. Chotero, palibe chirichonse chimene chimasokoneza chigwirizano chawo chodabwitsa cha dziko lonse.​—1 Petro 2:17.

14 Uchete wawo nthaŵi zina umabweretsa zotulukapo zosayembekezereka. Mu boma la Tsugaru la kumpoto kwa Japan, mwachitsanzo, masankho amatengedwa mosamalitsa. Koma Toshio, manejala wothandizira m’Gawo la za Ndalama la ofesi la boma la kumaloko, anakana kaamba ka zifukwa za chikumbumtima kulowetsedwa m’ndawala ya kusankhidwanso kwa mkulu wa mzinda. Ichi chinatulukapo m’kutsitsidwa kwake ku malo ochepa m’Gawo la Ntchito Yochotsa Zoipa m’Mizinda. Chaka chimodzi pambuyo pake, ngakhale kuli tero, mkulu wa mzindawo anamangidwa ndipo anakakamizidwa kuleka ntchito chifukwa cha kachitidwe koipa. Mkulu wa mzinda watsopano anasankhidwa. Pamene iye anamva ponena za kutsitsidwa kwa Toshio, anam’bwezanso iye ku malo aulamuliro wapamwamba, ndipo ichi chinabweretsa madalitso pa abale Achikristu a Toshio. Motani? Toshio akulongosola kuti chiri chovuta kupeza chilolezo cha kugwiritsira ntchito nyumba yochitiramo maseŵera olimbitsa thupi kaamba ka misonkhano kuposa zochitika za maseŵera. Koma m’malo ake a tsopano, “Yehova wakhala wokhoza kundigwiritsira ntchito”​—kugwira mawu a Toshio iyemwini​—“kupeza kugwiritsira ntchito kwa nyumba yochitiramo maseŵera olimbitsa thupi kaamba ka misonkhano ya chigawo itatu ndi misonkhano ya dera inayi.” Iye akumaliza kuti: “Malinga ngati tipitirizabe kukhala okhulupirika, Yehova adzatsegula njira zosayerekezeka za kutigwiritsira ntchito.”

M’nyumba

15. Ndimotani mmene Yesu anasiira chitsanzo kaamba ka otsatira mapazi ake m’nkhani ya unansi wa m’banja?

15 Mbali ina mu imene Akristu ‘amatsanzira mapazi a Yesu’ iri m’nyumba. Baibulo limakhazikitsa chitsanzo cha Yesu monga chitsanzo kaamba ka maunansi a m’nyumba pamene limati: “Ndi kumverana wina ndi mnzake m’kuwopa Kristu. Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye. Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa Eklesia . . . komatu monga Eklesia amvera Kristu, koteronso akazi amvere amuna awo m’zinthu zonse. Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda Eklesia, nadzipereka yekha m’malo mwake.”​—Aefeso 5:21-25.

16, 17. (a) Kodi ndi mkhalidwe woipa uti womwe ulipo m’Chikristu cha Dziko kulinga ku unansi wa m’banja? (b) Ndimotani kokha mmene unansi wa m’banja ungawongokere, monga momwe kwasonyezedwera ndi chitsanzo cha aŵiri okwatirana mu Brazil?

16 Chikristu cha Dziko lerolino kwambali yaikulu chimanyalanyaza uphungu umenewu ndipo chotero chiri chodzala ndi mabanja osweka. Nyumba zosweka ziri zofala, ndipo kukanthana kwa makolo ndi ana kaŵirikaŵiri kumapita mozama. “Banja likugawanika,” anawona tero profesala wa za malingaliro zaka zingapo zapitazo. Katswiri wa za malingaliro a achichepere, aphungu aukwati, ndi odokotala odziŵa matenda a malingaliro ali kokha ndi kupita patsogolo kokhala ndi polekezera m’kusungilira pamodzi mabanja okhala m’ngozi. Koma Mboni za Yehova zimayesera molimba kugwiritsira ntchito malamulo a Baibulo ndipo zikudziŵika kaamba ka unansi wa banja wokulira.

17 Aldemar, mwachitsanzo, anali nduna yaikulu mu polisi ya magulu ankhondo a ku Brazil ndipo anali ndi mavuto a banja. Mkazi wake anamusiya iye ndipo anafunafuna kulekana kwa lamulo. Iye anayamba kumwa mokulira ndipo ngakhale kuyesera kudzipha. Pambuyo pake, achibale ake omwe ali Mboni za Yehova, analankhula kwa iye ponena za Baibulo. Iye anakonda chomwe anamvetsera ndi kuyamba kuphunzira. Akumafuna kugwirizanitsa moyo wake ndi kaimidwe ka uchete komwe Mboni za Yehova zadziŵika nako, iye anapempha kuchotsedwa mu gulu lankhondo. Aldemar ndi mkazi wake anathetsa kusiyana kwawo kwa m’ukwati mwakugwiritsira ntchito malamulo a Baibulo omwe Aldemar ankaphunzira. Lerolino, iwo akutsatira m’mapazi a Yesu, kutumikira Yehova pamodzi monga apainiya okhazikika.

Omvera Chifukwa cha Chikondi

18. (a) Nchifukwa ninji Mboni za Yehova zikudalitsidwa mwauzimu lerolino? (b) Ndimotani mmene Yesaya 2:2-4 tsopano akupezera kukwaniritsidwa?

18 Chiri chowonekera kuti Mboni za Yehova zikuyendera pamodzi mogwirizana mu mzimu ndi m’mapazi a Kristu Yesu. Monga munthu aliyense payekha ndipo monga gulu, izo zikudalitsidwa mwauzimu kaamba ka kuchita tero. (Masalmo 133:1-3) Umboni wowonekera wa madalitso aumulungu pa izo wasonkhezera unyinji wa anthu owona mtima kuchita mogwirizana ndi ulosi wa pa Yesaya 2:2-4. Mu kokha zaka zisanu zapitazo, 987,828 atenga khalidwe loyenerera kaamba ka kudzipereka ndipo kenaka adziwonetsera iwo eni kaamba ka ubatizo wa m’madzi. Mwachikondi, Yehova sanaike tsankho lolekezera pa chiŵerengero cha anthu omwe angachite chimenechi “chisautso chachikulu” chisanakanthe!​—Chivumbulutso 7:9, 14.

19. (a) Kodi ndi mapindu odabwitsa otani omwe angatulukepo m’kutumikira Yehova, ndipo kodi ndimotani mmene iwo ayenera kuwonedwera? (b) Kodi ndi chiti chimene chiri chifukwa chathu chachikulu cha kumverera malamulo a Yehova?

19 Monga mmene zokumana nazo zomwe ziri pamwambazo zachitira chitsanzo, madalitso auzimu osangalalidwa ndi anthu a Mulungu amatsagana kaŵirikaŵiri ndi madalitso odabwitsa. Mwachitsanzo, mwakupewa kusuta fodya, mwakukhala mumkhalidwe wabwino, ndipo mwa kulemekeza kupatulika kwa mwazi, iwo angapewe kukhala m’nkhole ku matenda ena. Kapena chifukwa cha kukhala mogwirizana ndi chowonadi, iwo angapindule m’njira ya za chuma, mayanjano, kapena m’nyumba. Mapindu odabwitsa aliwonse oterewa amawonedwa monga madalitso kuchokera kwa Yehova, ndipo amatsimikizira kugwira ntchito kwa malamulo a Yehova. Koma kuthekera kwa kupeza mapindu ogwira ntchito oterewa sichiri mu icho chokha chifukwa chokulira kaamba ka kumvera malamulo a Mulungu. Akristu owona amamvera Yehova chifukwa chakuti amamkonda iye, chifukwa iye amafunikira kulambira kwawo, ndipo chifukwa chakuti kuchita chifuniro chake chiri chinthu chokha cholondola. (1 Yohane 5:2, 3; Chivumbulutso 4:11) Ali Satana yemwe amanena kuti anthu amatumikira Mulungu mokulira kaamba ka madalitso adyera.​—Onani Yobu 1:9-11; 2:4, 5.

20. Ndimotani mmene Mboni za Yehova za lerolino zikuyendera mu mzimu umodzimodziwo monga mboni zitatu zokhulupirika za Chihebri za m’nthaŵi yakale?

20 Mboni zamakono za Yehova zimayenda mumzimu umodzimodziwo monga mboni zitatu zokhulupirika zachichepere za Chihebri za m’tsiku la Danieli. Pamene zinawopsyedwa ndi kuponyedwa m’ng’anjo yotentha ndi moto, izo zinanena kuti: “Tawonani, Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m’ng’anjo yotentha yamoto nadzatilanditsa m’dzanja lanu, mfumu. Koma akapanda kutero [uku ndiko kunena kuti, ngakhale ngati atilola ife kufa], dziŵani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolidi mudaliimikalo.” (Danieli 3:17, 18) Mosasamala kanthu za madalitso odabwitsa a mwamsanga kapena zotulukapo, Mboni za Yehova zidzapitirizabe kutsatira mosamalitsa m’mapazi a Yesu, zikumadziŵa kuti moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu uli wotsimikizirika! Monga anthu ogwirizana, iwo adzapitirizabe kuyenda “mumzimu womwewo” ndi “m’mapazi omwewo,” mosasamala kanthu ndi chirichonse chomwe chingadze!

Kodi Mungalongosole:

◻ Nchifukwa ninji Mboni za Yehova ziri zogwirizana?

◻ Ndi m’njira zotani mmene Mboni za Yehova zimasiirana ndi Akristu abodza?

◻ Kodi nchifukwa chokulira chiti chimene Akristu owona amatumikira Yehova?

◻ Ndimotani mmene anthu a Mulungu amawonera madalitso omwe amatulukamo m’kumvera Yehova?

[Chithunzi patsamba 16]

Pamene wodwala akana kuthiridwa mwazi, icho kaŵirikaŵiri chimadziŵidwa kuti iye ali mmodzi wa Mboni za Yehova

[Chithunzi patsamba 18]

Ambiri odzinenera kukhala Akristu sanaipidwe ndi kumenya nkhondo pa wina ndi mnzake​—ndi kudalitsidwa kwa akulu awo a chipembedzo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena