Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mwazi—Wofunika Koposa Kaamba ka Moyo
    Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?
    • Wonani chimene chinachitika pamene, zaka zingapo imfa ya Yesu itachitika, funso linabuka lakuti kaya munthu wokhala Mkristu anafunikira kusungu malamulo onse a Israyeli. Limeneli linakambitsiridwa paupo wa bungwe lolamulira Lachikristu, limene linaphatikizapo atumwi. Mbale wa atate wina wa Yesu Yakobo anasonyeza malembo okhala ndi malamulo onena za mwazi onenedwa kwa Nowa ndi kumtundu wa Israyeli. Kodi amenewo akakhala akugwira ntchito pa Akristu?—Machitidwe 15:1-21.

      Upo umenewo unatumiza chosankha chawo kumipingo yonse: Akristu safunikira kusunga mpambo wa malamulo operekedwa kwa Mose, koma “nkofunikira” kwa iwo “kuleka kusala zinthu zoperekedwa nsembe kumafano ndi kusala mwazi ndi zinthu zopotoledwa [nyama yosakhetsedwa mwazi] ndi kusala chisembwere.” (Machitidwe 15:22-29, NW) Atumwiwo sanali kokha kupereka lamulo la mwambo kapena la zakudya. Lamulolo linakhazikitsa chitsanzo cha makhalidwe ofunika, chimene Akristu oyambilira anatsatira. Pafupifupi zaka khumi nsembe kumafano ndiponso kusala mwazi . . . ndi kusala chisembwere.”—Machitidwe 21:25.

      Mukudziŵa kuti mamiliyoni a anthu amapita kumatchalitchi. Ambiri a iwo mwinamwake akavomereza kuti makhalidwe Achikristu amaphatikizapo kusalambira mofano ndi kusachita chigololo. Komabe, nkoyenerera kuti tizindikire kuti atumwiwo anaika kupeŵa mwazi pamlingo wapamwamba wofananawo ndi kupeŵa zolakwa zimenezo. Lamulo lawo linamaliza ndi kuti: “Ngati mudziletsa mosamalitsa kuzinthu zimenezi, mudzachita bwino. Thanzi labwino kwa inu!”—Machitidwe 15:​29, NW.

      Lamulo la atumwi linazindikiridwa kale kukhala lomanga. Eusebius amasinba za mkazi wina wachichepere pafupi ndi mapeto a zaka za zana lachiŵiri amene, asanafe ndi chizunzo, ananena mawu akuti Akristu “samaloledwa kudya mwazi ngakhale wa nyama zosalingalira.” Iye sanali kugwiritsira ntchito kuyenera kwa kufa. Iye anafuna kukhala ndi moyo, koma iye sakanaleka ziphunzitso zake. Kodi inu simukulemekeza awo amene amaika chiphunzitso pamwamba pa phindu lawo?

      Wasayansi Joseph Priestley anati: “Chiletso cha kudya mwazi, choperekedwa kwa Nowa, chimawonekera kukhala chomanga pambadwa zake zonse . . . Ngati titanthauzira chiletso cha atumwi[cho] ndi kachitidwe ka Akristu oyambirira, amene sangalingaliridwe kukhala asakuzindikira moyenera mtundu ndi ukulu wake, ife sitingachitire mwina kusiyapo kunena kuti, chimenecho chinalinganizidwa kukhala chotheratu ndi chachikhalire; pakuti mwazi sunadyedwe ndi Akristu alionse kwa zaka mazana ambiri.”

  • Mwazi—Wofunika Koposa Kaamba ka Moyo
    Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?
    • [Bokosi patsamba 4]

      “Mwanjira imeneyi malamulo okhazikitsidwa m’mkhalidwe wachidule ndi wadongosolo [m’Machitidwe 15] akufotokozedwa kukhala ofunika, akumapereka umboni wamphamvu koposa wakuti m’maganizo mwa atumwi ameneŵa sanali makonzedwe akanthaŵi, kapena njira yakanthaŵi.”—Pulofesala Édouard Reuss, University of Strasbourg.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena