-
Chitani Zonse Chifukwa cha Uthenga WabwinoNsanja ya Olonda—1989 | November 15
-
-
3. Kodi kufunitsitsa kwa Paulo kwa kuchita zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino kunasonyezedwa motani m’chigwirizano ndi Timoteo ndi Ayuda?
3 Chiyambi Chachiyuda cha Paulo ndi kufunitsitsa kwake kwa kuchita zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino kunamukonzekeretsa kuthandiza Ayuda odzichepetsa kulandira Yesu monga Mesiya. Mwachitsanzo, lingalirani zimene mtumwiyo anachita pamene anasankha Timoteo monga mnzake woyenda naye. Timoteo, amene atate ake anali Mgriki, sanali wodulidwa monga mmene ana aamuna Achiyuda analiri. (Levitiko 12:2, 3) Paulo anadziŵa kuti Ayuda angakhumudwe ngati mwamuna wachichepere wosadulidwa anayesera kuŵathandiza kuti ayanjanitsidwe kwa Mulungu. Chotero, kotero kuti Ayuda owona mtima asatsekerezedwe kulandira Yesu, kodi Paulo anachitanji? Iye “anamtenga [Timoteo] namdula chifukwa cha Ayuda.” Izi zinachitidwa ngakhale kuti kudulidwa sikunali chiyeneretso Chachikristu.—Machitidwe 16:1-3.
4. Molingana ndi 1 Akorinto 9:20, kodi nchiyani chimene chinali cholinga cha Paulo?
4 Chotero chinali chifukwa chakuti Paulo anali kuchita zinthu chifukwa cha uthenga wabwino pamene anasonyeza kudera nkhaŵa kwachikondi kaamba ka Ayuda anzake. Iye analemba kuti: “Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindinakhala ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo.” (1 Akorinto 9:20) Inde, monga mmene zasonyezedwera mu nkhani ya Timoteo, Paulo anachita zomwe akanatha kuti apindule Ayuda, kuwathandiza iwo kukhala Akristu. Koma kodi iye anachita mofananamo ndi Akunja?
-
-
Chitani Zonse Chifukwa cha Uthenga WabwinoNsanja ya Olonda—1989 | November 15
-
-
7. Ponena za kudulidwa, kodi nchifukwa ninji mkhalidwe wa Tito unali wosiyana ndi uja wa Timoteo?
7 Pamene Paulo anapita ku Yerusalemu chifupifupi mu 49 C.E. kukapezekapo pa msonkhano wofunika kwambiri wa bungwe lolamulira la mpingo Wachikristu, iye anapita ndi wophunzira Wachigriki Tito. Kwa abale osonkhanawo, Paulo anapereka ripoti la ntchito yake yolalikira pakati pa anthu amitundu, ndipo pambuyo pake analemba kuti: “Komatu ngakhale Tito, amene anali ndi ine, ndiye Mhelene, sanamkakamiza adulidwe.” (Agalatiya 2:1-3) Mosiyana ndi Timoteo, Tito anachita uminisitala wake choyambirira pakati pa anthu amitundu osadulidwa. Ndicho chifukwa chake nkhani ya mdulidwe sinabuke kwa iye.—2 Akorinto 8:6, 16-18, 23; 12:18; Tito 1:4, 5.
-