-
Phunzirani Kukhala Maso Kuchokera kwa Atumwi a YesuNsanja ya Olonda—2012 | January 15
-
-
4, 5. Kodi mzimu woyera unatsogolera motani Paulo ndi anzake pa ntchito yawo?
4 Choyambirira, atumwi anali maso kwambiri kuti adziwe kumene anayenera kukalalikira. Lemba lina limatiuza mmene Yesu anagwiritsira ntchito mzimu woyera umene Yehova anamupatsa kuti atsogolere Paulo ndi anzake pa ulendo wina wovuta kwambiri. (Mac. 2:33) Tiyeni tione mmene anayendera.—Werengani Machitidwe 16:6-10.
-
-
Phunzirani Kukhala Maso Kuchokera kwa Atumwi a YesuNsanja ya Olonda—2012 | January 15
-
-
6, 7. (a) Kodi n’chiyani chinachitikira Paulo ndi anzake atafika pafupi ndi Bituniya? (b) Kodi atumwiwo anasankha kuchita chiyani, ndipo zotsatira zake zinali chiyani?
6 Kodi Paulo ndi anzake analowera kuti? Vesi 7 limafotokoza kuti: “Atafika ku Musiya anayesetsa kuti apite ku Bituniya, koma mzimu wa Yesu sunawalole.” Ataletsedwa kukalalikira ku Asia, Paulo ndi anzake analowera chakumadzulo kuti akalalikire m’mizinda ya ku Bituniya. Komabe atatsala pang’ono kufika ku Bituniya kachiwirinso Yesu anagwiritsa ntchito mzimu woyera kuwaletsa kuti asalalikire kumeneko. Pa nthawiyi amunawa ayenera kuti anazunguzika. Iwo ankadziwa uthenga woti alalikire ndiponso njira zolalikirira koma sankadziwa kumene angakalalikire. Tikhoza kunena kuti iwo anagogoda khomo lolowera ku Asia koma silinatseguke. Anagogodanso khomo lolowera ku Bituniya koma silinatsegukenso. Kodi iwo anangosiya kugogoda? Ayi sanasiye.
-