-
Phunzirani Kukhala Maso Kuchokera kwa Atumwi a YesuNsanja ya Olonda—2012 | January 15
-
-
4, 5. Kodi mzimu woyera unatsogolera motani Paulo ndi anzake pa ntchito yawo?
4 Choyambirira, atumwi anali maso kwambiri kuti adziwe kumene anayenera kukalalikira. Lemba lina limatiuza mmene Yesu anagwiritsira ntchito mzimu woyera umene Yehova anamupatsa kuti atsogolere Paulo ndi anzake pa ulendo wina wovuta kwambiri. (Mac. 2:33) Tiyeni tione mmene anayendera.—Werengani Machitidwe 16:6-10.
-
-
Phunzirani Kukhala Maso Kuchokera kwa Atumwi a YesuNsanja ya Olonda—2012 | January 15
-
-
7 Pa nthawiyi, zimene amunawa anasankha kuchita zingaoneke zosamveka. Vesi 8 limatiuza kuti: “Analambalala Musiya ndi kukafika ku Torowa.” Choncho iwo anabwerera kulowera chakumadzulo. Anayenda mtunda wokwana makilomita 563 kudutsa mizinda ingapo mpaka anakafika ku Torowa kumene kunali njira yolowera ku Makedoniya. Kumeneku Paulo ndi anzake anagogodanso ndipo tsopano khomo linawatsegukira. Pofotokoza zimene zinachitika Vesi 9 limati: “Ndiyeno usiku Paulo anaona masomphenya. Munthu wina wa ku Makedoniya anaimirira ndi kumupempha kuti: ‘Wolokerani ku Makedoniya kuno mudzatithandize.’” Apa tsopano Paulo anadziwa kumene angapite kuti akalalikire. Mosazengereza, iye limodzi ndi amuna amene anali nawo anawolokera ku Makedoniya.
-