Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Anakambirana Nawo Mfundo za M’Malemba”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
    • Paulo ndi Sila athawira ku mpanda poopa gulu la anthu a chipolowe. Bambo wina akulankhula ndi gulu la anthuwo pa geti.

      “Anapita . . . kukafuna Paulo ndi Sila kuti awatulutse n’kuwapereka ku gulu limene linkachita chipolowelo.”​—Machitidwe 17:5

      10 Kenako Luka anafotokoza zimene zinachitika. Iye anati: “Ayuda anachita nsanje ndipo anasonkhanitsa anthu ena oipa amene ankangokhala pamsika. Iwowa anapanga gulu lachiwawa n’kuyambitsa chipolowe mumzindamo. Kenako anapita kunyumba ya Yasoni, kukafuna Paulo ndi Sila kuti awatulutse n’kuwapereka ku gulu limene linkachita chipolowelo. Atalephera kuwapeza, anakokera Yasoni ndi abale ena kwa olamulira a mzindawo, akufuula kuti: ‘Anthu awa, amene ayambitsa mavuto kwina konseku, tsopano akupezekanso kuno. Ndipo Yasoni wawalandira ngati alendo ake. Anthu onsewa akuchita zotsutsana ndi malamulo a Kaisara. Eti akunena kuti kulinso mfumu ina dzina lake Yesu.’” (Mac. 17:5-7) Kodi Paulo ndi anzakewo anachita chiyani ataukiridwa ndi gulu la anthu achiwawawo?

      11. Kodi Ayuda ananamizira milandu yotani Paulo ndi anzake amene ankalalikira nawo uthenga wa Ufumu, ndipo Ayudawo ayenera kuti ankaganizira za lamulo liti? (Onani mawu a m’munsi.)

      11 Anthu akayambitsa gulu lachiwawa, amachita zinthu zoopsa kwambiri ndipo samva za munthu. Ndipo izi n’zimene Ayuda anachita pofuna kuthana ndi Paulo ndi Sila. Iwo atayambitsa “chipolowe” mumzindamo, anayesetsa kutsimikizira olamulira kuti atumwiwo anapalamula milandu ikuluikulu. Mlandu woyamba unali wakuti Paulo ndi anzake amene ankalalikira nawo uthenga wa Ufumu “ayambitsa mavuto kwina konseku” ngakhale kuti Paulo ndi anzakewo si amene anayambitsa chipolowe ku Tesalonika. Mlandu wachiwiri unali woopsa kwambiri. Ayudawo ananena kuti amishonalewo ankalengeza kuti pali Mfumu ina dzina lake Yesu, ndipo pochita zimenezi iwo anaphwanya malamulo a mfumu ya Roma.a

      12. N’chiyani chikusonyeza kuti Akhristu a ku Tesalonika akanakumana ndi mavuto aakulu chifukwa cha milandu imene anawanamizira?

      12 Musaiwale kuti atsogoleri achipembedzo ananamizira Yesu mlandu ngati womwewu. Iwo anauza Pilato kuti: “Ife tapeza munthu uyu akupandutsa mtundu wathu . . . komanso akunena kuti ndi Khristu mfumu.” (Luka 23:2) Mwina poopa kuti mfumu ya Roma ingaganize kuti Pilato akulekerera munthu woukira boma, iye anapereka Yesu kwa iwo kuti akamupachike. Mofanana ndi zimenezi, Akhristu a ku Tesalonika akanathanso kukumana ndi mavuto aakulu chifukwa cha milandu imene Ayuda ankawanamizira. Buku lina limanena kuti: “Mlandu umene [Akhristuwo] ankawaimba unali woopsa kwambiri chifukwa ‘munthu amene ankaimbidwa mlandu woukira mfumu ya Roma, kawirikawiri ankapatsidwa chilango choti aphedwe.’” Kodi zolinga zoipa za Ayudawo zinatheka?

  • “Anakambirana Nawo Mfundo za M’Malemba”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
    • a Katswiri wina ananena kuti pa nthawiyo panali lamulo la Kaisara limene linkaletsa munthu aliyense kulosera kuti “kudzabwera mfumu ina kapena ufumu, umene akuganiza kuti udzagonjetsa kapena kuweruza mfumu ya Roma imene inkalamulira pa nthawiyo.” Adani a Paulo ayenera kuti anapotoza uthenga wa mtumwiyu kuti aoneke ngati waphwanya lamulo limeneli. Onani bokosi lakuti “Olamulira a Roma M’nthawi ya Atumwi.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena