Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Muli Otseguka ku Malingaliro Atsopano?
    Nsanja ya Olonda—1989 | January 15
    • Mosasamala kanthu za chimenecho, panali anthu ofunitsitsa kuyang’ana kupyola pa kunyada kwawo. Mwachitsanzo, ndimotani mmene nzika za ku Bereya zinavomerezera ku mbiri yabwino yolalikidwa ndi mtumwi Paulo ndi woyanjana naye wake Sila? Ponena za anthu a ku Bereya, wolemba Baibulo Luka ananena kuti: “Amenewa anali mfulu kuposa a mu Tesalonika, popeza analandira mawu ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m’Malembo masiku onse ngati zinthu zinali tero.” (Machitidwe 17:11) Kodi inu muli “mfulu koposa” monga anthu a ku Bereya?

      Chonde lingalirani nkhani ya Masaji. Pa nthaŵi imodzi, iye anali ndi udani wamphamvu kulinga ku Chikristu. Iye anali wofanana ndi odzipatula omwe anatsutsa kutsegulidwa kwa Japan. Pamene mkazi wake, Sachiko, anayamba kuphunzira Baibulo, iye anamutsutsa mwachiwawa. Iye anafikira pa kulingalira za kupha banja lake ndipo kenaka kudzipha. Chifukwa cha chiwawa chake, banja lake linayenera kuthaŵira kunyumba ya mbale wamkulu wa Sachiko kumpoto kwa Japan.

      Pomalizira pake, Masaji anaganiza za kutsegula maganizo ake pang’ono ndi kufufuza chipembedzo cha mkazi wake. Pambuyo pa kuŵerenga mabukhu ena a Baibulo, iye anawona chifuno cha kupanga masinthidwe. Pamene anaphunzira Malemba, mkhalidwe wake wachiwawa unasintha kukhala uja wowunikiridwa ndi chipatso cha mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23) Masaji anasinkhasinkha kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova chifukwa anawopa kuti Mboni zingafune kubwezera kaamba ka chiwawa chake molimbana nawo. Koma pamene iye pomalizira pake anafika pa Nyumba ya Ufumu, iye analandiridwa ndi ukoma woterewo kotero kuti anatulutsa misozi.

  • Kodi Muli Otseguka ku Malingaliro Atsopano?
    Nsanja ya Olonda—1989 | January 15
    • Nchiyani chomwe tingaphunzire kuchokera ku ichi? Kuti tiyenera kukhala osankha ponena za kulandira malingaliro atsopano. Tingachite bwino kutsanzira anthu a ku Bereya mwa “kusanthula Malemba masiku onse ngati zinthu [zophunzitsidwa ndi Paulo] zinali zotero.” (Machitidwe 17:11) Liwu la Chigriki logwiritsiridwa ntchito pano kaamba ka “kusanthula” limatanthauza “kupanga kufufuza kosamalitsa ndipo kwachindunji monga mu nkhani za milandu ya lamulo.” (Word Pictures in the New Testament, lolembedwa ndi A. T. Robertson) M’malo molandira mwakhungu lingaliro lirilonse latsopano loperekedwa kwa ife, tifunikira kuchita kufufuza kosamalitsa ndi kwachindunji, mongadi mmene woŵeruza angachitire m’kumva nkhani ya mlandu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena