Agora—Pachimake pa Atene Wakale
KUNALI chipolowe cha anthu ophunzira kwambiri a ku Atene! Nthaŵi zonse mumzinda wa ku Grisi umenewo, malingaliro atsopano anali kufalitsidwa pa agora, kapena kuti msika. Koma izi zinali zina. Atangofika mumzindawo, mwamuna wina wachiyuda anaoneka kukhala “wolalikira ziŵanda zachilendo [milungu yachilendo, NW].” Iye anali kulankhula zinthu zachilendo kwa “iwo amene anakomana nawo.” “Ichi nchiyani afuna kunena wobwetuka uyu?” anafunsa motero Aepikureya onyadawo ndi Astoiki oipitsa nkhopewo. Inde, agora wa ku Atene ndiwo anali malo okambitsiranapo nkhani iliyonse ya pansi pa thambo mwa kuchita mtsutso wapoyera. Koma kulankhula za milungu yachilendo—ayi, kumeneku kunali kunyanya!—Machitidwe 17:17, 18.
Aatene anamganizira motero mtumwi Paulo atayamba kulalikira kwa nthaŵi yoyamba pa agora wa ku Atene. Iye anali kunena za Yesu Kristu ndi za chiukiriro. Koma kwa anthu a ku Atene ooneka ngati okonda kumva zinthu zosiyanasiyana, kodi nchiyani chimene chinali chachilendo pofotokoza malingaliro atsopano amenewo pa agora?
Atene Akhala ndi Bwalo la Anthu Onse
Kwenikweni chimene chinali chapadera ndicho agora weniweniyo ndi chisonkhezero chake chachikulu pachipembedzo ndi moyo wa anthu a ku Atene. Agora wa ku Atene ndi malo otsetsereka pang’ono a mahekitala ngati khumi kumpoto chakumadzulo kwa Acropolis. Zikuoneka kuti kuchiyambi kwa zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E., pamene wolamulira ndiponso wopanga malamulo Solon anali moyo, malo ameneŵa anasankhidwa kukhala bwalo la anthu onse la mzindawo. Kuyambika kwa demokalase yofuna kuwongolera moyo wa anthu wamba ku Atene, kunachititsa kuti anthu ayambe kumanga zimango zambiri m’zaka zoyambirira za zaka za zana lotsatira. Zimenezi zinapangitsa agora kukhalanso waumoyo ndiponso wachisonkhezero chapadera kwambiri.
Liwu lachigiriki lakuti a·go·raʹ lachokera ku verebu lotanthauza “sonkhana.” Zimenezi zikugwirizana ndi ntchito ya malowo monga malo aakulu osonkhanirapo mumzindawo. Agora anadzakhala pachimake pa zochita za anthu za masiku onse. Anali likulu la oyang’anira zaumoyo wa anthu ndiponso likulu la oweruza, likulu la zamalonda, bwalo la maseŵero azisudzo achigiriki, bwalo la maseŵero olimbitsa thupi, ndiponso malo okambitsiranapo zamaphunziro.
Kodi mungakonde kuona mabwinja a akachisi, mizati, zifanizo, zipirala, ndi zimango za onse za pa agora ku Atene? Kuti tisanthule mkhalidwe wakale wa agora, tiyeni tiiŵale za phokoso ndi piringupiringu wa mzinda wamakono ndipo tiyende m’tinjira ta miyala, pakati pa mabwinja a miyala ya nsangalabwi, miyala yosemedwa, ndi makomo ogumuka a zimango zina oŵirira ndi udzu ndi zitsamba.
Akachisi, Malo Opatulika, ndi Milungu Yaikulu
Odzacheza amazizwa ndi akachisi ambiri amene ali kumeneko, ndiponso malo opatulika osiyanasiyana a milungu yosiyanasiyana. Zonsezi zinapangitsa agora kukhala malo aakulu a kulambira, achiŵiri kwa Acropolis. Mu Atene wakale wa m’nyengo ya Golden Age, chipembedzo chinali kukhudza mbali zonse za moyo wa anthu. Zimenezi zinatanthauza kuti milungu yosiyanasiyana yotchedwa “milungu yaikulu” ya madipatimenti a boma ndi ya mautumiki auyang’aniro inali kupatsidwa malo opatulika mu akachisi a pa agora.
Chimango chotchuka mwa zimango zimenezi chinali Kachisi wa Hephaestus. Mulungu wamkazi wotchedwa Athena anali kugwirizanitsidwa ndi Hephaestus. Milungu yonse iŵiriyi inali kulambiridwa pano monga milungu yaikulu ya zamaluso. Zipangizo zachitsulo ndi mitsuko yofukulidwa m’mabwinja ozungulira kachisi ameneyu zikusonyeza kuti kachisiyo anali wa Hephaestus, mulungu wa Agiriki wa zamaluso wofuna kuti azigwiritsira ntchito moto. Mwina cha m’zaka za zana lachisanu ndi chiŵiri C.E., kachisi wosamalidwa bwino ameneyu anasinthidwa kukhala Tchalitchi cha Greek Orthodox cha ku St. George, ngakhale kuti panopo salinso tchalitchicho.
Eya, agora anafunikiranso mulungu wake wamkulu. Ameneyu anali Zeus Agoraios, amene amati ndiye wouzira malankhulidwe aluso apoyera ndipo guwa lansembe lokometseredwa bwino la mwala wamtengo wapatali wosemedwa wa Pentelic marble linaperekedwa kwa iye. (Yerekezerani ndi Machitidwe 14:11, 12.) Zipilala zochititsa chidwi zoimira ngwazi zinali kumbali zonse ziŵiri za guwa lansembe loyandikana nalo la Amayi wa Milungu.
Cha apo, tikupeza kachisi wamng’ono wamamangidwe a ku Ionia. Wodziŵa za malo adziko Pausanias anati ameneyo anali Kachisi wa Apollo Atate. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti malinga ndi nthano yakale yachigiriki, iye anali atate wa Ion, woyambitsa fuko la anthu a ku Atene lotchedwa Ionia.a Pamenepa ndiye kuti Apollo anali mmodzi mwa milungu yaikulu ya bungwe laboma lauyang’aniro, makamaka chifukwa cha ubale wosiyanasiyana umene unali mumzindawo.
Kumpoto kwake, tikuona bwinja la kachisi wamng’ono wa mwala wa njereza, womangidwa chapakati pa zaka za zana lachinayi B.C.E. Pano mpamene ankalambirira Zeus ndi Athena Phatrios, milungu yaikulu ya ubale wakale wazipembedzo. Kuloŵa mu ubale umenewu kunali pafupifupi chiyeneretso chokhalira nzika ya Atene. Tsidya linalo la msewu, tikupeza mabwinja a guwa lansembe la Milungu Khumi ndi Iŵiri.
M’Khumbi la Zeus Eleutherios limene lili pafupi, mulungu wamkulukulu wachigiriki analandiranso ulemu wina, tsopano monga mulungu wa ufulu ndi chilanditso. Khumbi la mizati limeneli kapena kuti stoa, linali malo otchuka owongoleramo miyendo ndiponso malo osonkhaniramo. Wafilosofi wotchuka Socrates akuti ankakumana ndi anzake m’khumbi limeneli, mmene anali kukhala pansi ndi kucheza kapena kuwongola miyendo. Zinthu zambiri zopatuliridwa ndiponso nsembe zoperekedwa zokongoletsa khumbi limeneli, monga zishango za ankhondo amene anafa potetezera Atene, zinali kusonyeza kulanditsidwa kwa mzindawo kwa adani ake kapena kusungidwa kwa ufulu wake.
Msewu wa Panathenaea
Pakati pa agora pakudutsa msewu wotakata wafumbi kuchoka pangodya ina kupita pangodya yoyang’anizana nayo wotchedwa kuti Msewu wa Panathenaea. Dzina lake ndi mkhalidwe wake wapadera zinachokera ku phwando la Aatene lotchedwa Panathenaea. Paphwando limeneli nsalu yophimba nkhope ya mulungu wamkazi Athena inali kunyamulidwa mumsewu umenewu kuchokera ku Nyumba Yamwambo (pafupi ndi chipata cha mzindawo) kupita ku Acropolis. Chozokotedwa pakhoma la Parthenon chikutithandiza kuona kukongola ndi ulemerero wa mwambo wa phwandolo—apakavalo, magaleta aliŵiro, ng’ombe ndi nkhosa zokapereka nsembe, anyamata ndi asungwana onyamula ziŵiya zokagwiritsira ntchito popereka nsembe. Mwambowo unali kupenyereredwa ndi nzika za Atene ndi alendo awo, amene olinganiza agora anawakonzera malo okwanira. Mwachitsanzo, makumbi okhala ndi bwalo ndi masitepesi kutsogolo kwake anamangidwa pamalo abwino kwambiri oyang’anizana ndi msewu umenewu wochitiramo mwambo. Openyerera ambirimbiri anali kukhala pamasitepesi ochuluka ameneŵa osemedwa kutsogolo kwa makumbiwo.
‘Wodzala ndi Mafano’
Pokhala ndi akachisi onsewo, zifanizo, ndi zipirala, nzosadabwitsa kuti mtumwi Paulo “anavutidwa mtima pamene anaona mudzi wonse wadzala ndi mafano.” (Machitidwe 17:16) Zimene Paulo anaona ataloŵa mu agora ziyenera kuti zinamdabwitsa kwambiri. Zifanizo za mpheto za mulungu Herme zinali zochulukitsitsa moti zinafunika khumbi lakelake lozisungiramo, lodziŵika kuti Khumbi la Herme. Zovala za Herme pazithunzi zina zojambulidwa ndi utoto zikusonyeza zizindikiro za mphamvu ya kubala ndi moyo. Panali chifanizo cha Venus Genetrix, mulungu wamkazi wa chikondi chakugonana, ndi chifanizo chinanso cha Dionysus chosonyeza mitanda ingapo yampheto. Mwala wa m’malire pamodzi ndi mkhate wamadzi “oyera” oti onse oloŵa pamalowo azidziyeretsera mwamwambo nzimene zinali kusonyeza “kupatulika” kwa agora.
Polingalira za kuchuluka kwa zipembedzo kumeneku, titha kumvetsa mosavuta chifukwa chimene Paulo analili pangozi yaikulu. Anthuwo anamganizira kuti ndi “wolalikira ziŵanda zachilendo [milungu yachilendo, NW],” ndipo malamulo apanthaŵiyo anagamula kuti ‘palibe munthu amene ayenera kukhala ndi milungu yapadera iliyonse, kapena milungu yatsopano; ndiponso palibe amene ayenera kulambira milungu iliyonse yachilendo mwamtseri pokhapo itakhala yololedwa ndi onse.’ Ndiye chifukwa chake mtumwiyo anamtengera ku Areopagi kukamfunsa.—Machitidwe 17:18, 19.
Likulu la Uyang’aniro
M’nyumba yozungulira yotchedwa Tholos ndimo mmene munali likulu la boma la Atene. Apampando ambiri a mzindawo anali kugona m’nyumbayi usiku kuti akuluakulu amaudindo azikhala pafupi nthaŵi zonse. Mu Tholos anali kusungiramo miyeso yovomerezeka mwalamulo ya zopimira. Nyumba za madipatimenti osiyanasiyana a uyang’aniro zinali pafupi ndi nyumbayi. Nyumba ya Konsolo inali m’mbali mwa phiri kumpoto chakumadzulo kwa Tholos. Kumeneko, mamembala a Konsolo okwanira 500 anali kuchita misonkhano nachita ntchito ya komiti ndi kupanga malamulo kaamba ka Bungwe Lopanga Malamulo.
Chimango chinanso chofunika kwambiri chauyang’aniro chinali Khumbi Lachifumu. Mmenemo ndimo mmene Woweruza Wamkulu Wachifumu wa Atene—mmodzi mwa oweruza aakulu atatu a mzindawo—anali kuweruzira. Iye anali kuchita ntchito zambiri zauyang’aniro mmenemo zokhudza ponse paŵiri chipembedzo ndi zamalamulo. Muyenera kuti ndi m’nyumba imeneyo mmene Socrates anapita kukaonekera ataimbidwa mlandu wa kupanda ulemu. Malamulo amakolo a mzinda wa Atene anazokotedwa pakhoma la nyumba yoyang’anizana nayo. Chaka chilichonse, oweruza aakulu anali kuima pamwala umene uli patsogolo pa nyumbayi kuti alumbire poyamba ntchito yawo.
Khumbi la Attalus
Chimango cha pa agora chimene chasungidwa bwino kwambiri ndicho Khumbi la Attalus. Pamene anali wachinyamata, Attalus, Mfumu ya Pergamo (zaka za zana lachiŵiri B.C.E.), anaphunzira m’masukulu a ku Atene, monga momwe anachitira ana ambiri a m’mabanja achifumu ochokera kumaiko a ku Mediterranean. Atakhala mfumu, anapereka mphatso yochititsa chidwi imeneyi—Khumbi la Attalus—ku mzinda umene anaphunzirako.
Khumbi la Attalus linapangidwa kuti kwenikweni likhale mthunzi wabwino ndiponso khumbi lokongola kwambiri lowongoleramo miyendo ndi kukambitsirana. Pansi pake ndiponso bwalo lapatsogolo pake anali malo abwino kwambiri okhalapo popenyerera zochitika za mapwando, pamene kuli kwakuti kutchuka kwake monga khumbi lowongoleramo miyendo kuyenera kuti kunalichititsa kukhala malo abwino kwambiri amalonda. Boma liyenera kuti linkabwereketsa masitolowo kwa amalonda kotero kuti khumbilo linakhala magwero a ndalama.
Pamene lakonzedwanso kuti likhale monga momwe linalili kale, Khumbi la Attalus likupereka chitsanzo chabwino kwambiri cha kulinganiza nyumba mwaluso. Ukulu wake, kusiyana kochititsa chidwi kwa mizere yapansi ndi yapamwamba ya mizati, kuloŵanaloŵana kosangalatsa kwa kuunika ndi mthunzi, ndiponso kukongola kochititsa kaso kwa milimo yake, zonse zimapangitsa khumbilo kukhala lapadera. Kusiyana kosangalatsa kwa mbali zake nkoonekeratu, makamaka chifukwa cha mitu ya mizati yake yamitundu itatu yosiyanasiyana—ya Doric, ya Ionia, ndi yachiaigupto.
Malo Ochitiramo Miyambo Yosiyanasiyana
Nyumba imene nthaŵi zambiri anali kuchitiramo zamwambo ku Atene inali Nyumba ya Zosangulutsa. Iyo inali mphatso ya Vipsanius Agrippa, mpongozi wa Mfumu Augustus ya Roma. Chigawo chake chakutsogolo chinali cha miyala ya nsangalabwi yamaonekedwe osiyanasiyana. Chigawo chokhalamo anthu, chimene chinali ndi malo a anthu ngati 1,000, chinali chautali wa mamita ngati 25 ndipo poyamba chinali ndi denga lopanda mizati mkati. Limeneli linali limodzi mwa madenga achilendo omangidwa molimba mtima kwambiri panthaŵi yakaleyo. Komabe, zosangulutsa zambiri zimene zinali kuchitikira m’nyumbayi ziyenera kuti zinali zokayikitsa kwa Akristu oona chifukwa cha khalidwe lawo lapamwamba kwambiri.—Aefeso 5:3-5.
Anthu ena a m’nthaŵi zakale ofuna kudziŵa zambiri ayenera kuti ankapita ku Laibulale ya Pantainos. Makoma ake anangophimbidwa ndi makabati osungiramo mipukutu ya gumbwa ndi zikopa zolembedwa pamanja. Chipinda chachikulu cha laibulale chinayang’ana kumadzulo, ndipo chakutsogolo kwa mizati kunali kuonekera khumbi lalikulu lamizati—malo osangalatsa powongola miyendo, kuŵerenga, kapena kusinkhasinkha. Mawu ozokotedwa osonyeza aŵiri mwa malamulo a laibulaleyo apezedwa. Malamulowo anali akuti: “Musatuluke ndi buku lililonse,” ndi “[Laibulale] imatsegulidwa pa ola loyamba mpaka ola lachisanu ndi chimodzi.”
Agora Lerolino
M’zaka zaposachedwapa, pafupifupi malo onse a agora afukulidwa ndi sukulu yotchedwa American School of Classical Studies. Malo okhala chamunsi mwa Acropolis ameneŵa, akhala okopa alendo ofuna kudziŵa zina ndi zina ponena za mbiri ya Atene wakale.
Msika Wakaunjika wa Monastiraki woyandikana nawo—kungoyenda pang’ono kuchokera pa agora ndi pa Acropolis—ali malo enanso osangalatsa kwambiri. Amasonyeza mlendo zochitika zodabwitsa komanso zosangalatsa za chikhalidwe chachigiriki ndi zochitika za pamsika wa Kummaŵa kwa Middle-East pamodzi ndi mitengo yake yazinthu. Ndiponso mlendoyo adzaona Mboni za Yehova kumeneko zikuchita mwachimwemwe ndendende zimene mtumwi Paulo anachita zaka zoposa 1,900 zapitazo—kulalikira poyera uthenga wabwino wa Ufumu kwa ‘iwo amene akomana nawo.’
[Mawu a M’munsi]
a Dzinalo Ionia lachokera ku dzina lakuti Yavani, mwana wa Yafeti ndiponso mdzukulu wa Nowa.—Genesis 10:1, 2, 4, 5.
[Bokosi patsamba 28]
Malonda ku Atene
Agora sanali chabe mchombo wa Atene wa zamaphunziro ndi zachikhalidwe cha anthu komanso anali msika waukulu wa mzindawo. Atene anadzakhala likulu la zamalonda, lotchuka chifukwa cha ndalama yake yamphamvu ndi khama la oweruza ake aakulu, amene anali ndi udindo woonetsetsa kuti malonda onse akuchitika moona mtima ndiponso mosadyererana.
Atene anali kugulitsa ku maiko ena vinyo, mafuta a azitona, uchi, miyala ya nsangalabwi, ndi zinthu zina zopangidwa monga mbale ndi mitsuko yadothi ndi zitsulo. Ndiyeno mzindawo unali kugula kwambiri tirigu kuchokera kumaiko ena. Popeza kuti Attica (dera lozungulira Atene) sinali kutulutsa zakudya zambiri zodyetsa anthu ake, malamulo a malonda anali okhwima. Msika wa ku Piraeus (doko la Atene) nthaŵi zonse unayenera kukhala ndi chakudya chatsopano chokwanira kaamba ka anthu a mumzinda ndi asilikali. Ndipo amalonda sanali kuloledwa kusunga katundu kuti adzamgulitse pamtengo wokwera atayamba kusoŵa.