Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 7/1 tsamba 32
  • Nthaŵi Yofunafuna Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nthaŵi Yofunafuna Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1992
Nsanja ya Olonda—1992
w92 7/1 tsamba 32

Nthaŵi Yofunafuna Mulungu

CHITHUNZITHUNZI chiri patsamba lino ndicho ngaka ya Acropolis wa ku Atene, amene kalelo anali phata lolambirira milungu ndi milungu yachikazi. Munsi mwa Acropolis muli Areopagi, wonenedwa kuti anali malo kumene khoti lachiweruzo linali m’nthaŵi zamakedzana. Panali pamaloŵa, pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, pamene mtumwi Paulo anaima ndi kukamba nkhani yochititsa chidwi. Zina za zimene ananena ndi izi:

“Ndi mmodzi [Mulungu] analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zawo, ndi malekezero a pokhala pawo; kuti afunefune Mulungu, kapena akamfufuze ndi kumpeza, ngakhale sakhala patali ndi yense wa ife; pakuti mwa iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu.”​—Machitidwe 17:26-28.

Mbiri ikanakhala yosiyana chotani nanga ngati anthu onse akanalabadira mawu a Paulo! Nkhondo zambiri, ndi kuvutika kwakukulu, zikanapeŵedwa ngati anthu akanazindikira zofuna zawo monga mbadwa za munthu mmodzi wolengedwa ndi Mfumu Ambuye, Yehova.

Lerolino, anthu ngogaŵanika chifukwa cha utundu, kusiyana kwa olemera ndi osauka, maudani aufuko, ndi chisalungamo pakati pa anthu. Chikhalirechobe, mawu a Paulo amagwirabe ntchito. Tonsefe tiri mbadwa za munthu mmodzi ameneyo wolengedwa ndi Mulungu. M’lingaliro limenelo, tonsefe ndife abale ndi alongo. Ndipo kufunafuna Mulungu sikunakhalebe m’mbuyo mwa alendo pamene angapezeke.

Mawu a Paulo amakhala amphamvudi pamene tipenda mawu omaliza a nkhani yake. Iye anati: “[Mulungu] anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene anamuukitsa iye kwa akufa.”

Kuuka kwa Yesu ndinkhani yeniyeni ya mumbiri, ndipo monga momwe Paulo akusonyezera, ndichitsimikiziro chakuti kudzakhala tsiku lakuweruza anthu. Liti? Eya, tidziŵa kuti layandikirirapo ndi pafupifupi zaka 2,000 kuposa pamene Paulo anaima pa Areopagi ndi kunena mawu ameneŵa. Ndithudi, kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo kumasonyeza kuti layandikira kwambiri. Ndilingaliro lamphamvu chotani nanga! Nkofulumira chotani nanga kuti tifunefune Mulungu mowona mtima, popeza kuti, monga momwe Paulo anauzira Aatene, “tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponseponse atembenuke mtima”!​—Machitidwe 17:30, 31.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena