Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Sonyezani Kufunitsitsa ku Kulalikira Mbiri Yabwino
    Nsanja ya Olonda—1987
    • 9. Kodi ndi motani mmene Paulo anasonyezera kufunitsitsa kwa kulalikira mbiri yabwino?

      9 Angakhale kunali tero, Paulo sanadzimve kuti anali ndi zochita zokwanira, ndiponso sanalingalire kuti anali ndi ntchito yake ndipo imeneyo inali yokwanira. Iye anafuna kuchita zowonjezereka. Mu chenicheni, iye anati: “Pali kufunitsitsa kumbali yanga kuti ndilalikire mbiri yabwino kwa inunso ku Roma.” Chimenecho ndicho chimene kufunitsitsa kuli! Moyenerera, profesa F. F. Bruce mu bukhu lake The Epistle of Paul to the Romans ananena izi ponena za mtumwiyo: “Kulalikira kwa uthenga wabwino kuli mu mwazi wake, ndipo iye sangathe kuchoka ku iwo; iye sakhala konse ‘wopuma ku ntchito’ koma ayenera kukhala mokhazikika pa iyo, ali kumachotsako mangawa owonjezereka omwe ali nawo pa mtundu wonse wa anthu—mangawa amene iye sadzakwaniritsa kubwezera ngati akali ndi moyo.” Kodi mmenemo ndi mmene munauonera utumiki wanu?

  • Sonyezani Kufunitsitsa ku Kulalikira Mbiri Yabwino
    Nsanja ya Olonda—1987
    • “Wamangawa” kwa Onse

      11. Kodi mawu akuti “ndiri wamangawa,” amatanthauzanji?

      11 Panali mphamvu ina yofulumiza pambuyo pa kuyesayesa kosatopa kwa Paulo mu kulalikira mbiri yabwino. “Ine ndiri wamangawa wa Ahelene ndi wa Akunja, kwa anzeru ndi wa opusa,” anatero Paulo. (Aroma 1:14) Ndi mwanjira yotani mmene Paulo anali “wamangawa”? Otembenuza ena amagwiritsira ntchito kalongosoledwe aka “Ndiri pansi pa thayo” (New English Bible), “Ndiri ndi thayo” (Today’s English Version), kapena “Ndiri ndi mangawa a thayo” (Jerusalem Bible). Kodi pamenepo, iye anali kunena kuti, ntchito yolalikira inali ntchito yotopetsa kapena thayo limene iye anafunikira kulipereka pamaso pa Mulungu? Chiri chapafupi kukulitsa kapenyedwe kameneko ngati ife titaleka kupenya kofulumira kapena takokedwa ndi zokopa za dziko. Koma chimenecho sindicho chimene Paulo anali nacho m’maganizo.

      12. Ndi kwa ayani kumene Paulo anali “wamangawa,” ndipo nchifukwa ninji?

      12 Monga “chotengera chosankhika” ndiponso monga “mtumwi wa anthu amitundu,” Paulo anali ndi thayo lolemera kwambiri pamaso pa Mulungu. (Machitidwe 9:15; Aroma 11:13) Komabe lingaliro lake lathayo silinali kokha kwa Mulungu. Iye ananena kuti anali “wamangawa” kwa ‘Ahelene (Agiriki), Akunja, anzeru ndi opusa.’ Kaamba ka chifundo ndi mwawi woperekedwa kwa iye, iye analiwona kukhala thayo lake la kulalikira kotero kuti onse amve mbiri yabwino. Iye anazindikira, kuti chinali chifuniro cha Mulungu chakuti “anthu onse ayenera kupulumutsidwa ndi kubwera ku chidziwitso cha chowonadi.” (1 Timoteo 1:12-16; 2:3, 4) Chimenecho ndicho chifukwa chake iye anagwirira ntchito mosalekeza, osati kokha kuti akhale ku thayo lake kulinga kwa Mulungu komanso kubwezera mangawa ake kwa anthu anzake. Kodi mumadzimva kukhala wamangawa mwa umwini chotero kulinga kwa anthu amene ali mugawo lanu? Kodi mumadzimva kukhala wamangawa kwa iwo

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena