Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Mwakonzeka Kubatizidwa?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 3. N’chifukwa chiyani simuyenera kulola kuti mantha akulepheretseni kubatizidwa?

      Anthu ena amaopa kubatizidwa chifukwa amaona kuti akhoza kulephera kukwaniritsa zimene anamulonjeza Yehova. N’zoona kuti nthawi zina mukhoza kulakwitsadi zinthu. Koma dziwani kuti ngakhale amuna ndi akazi okhulupirika amene amatchulidwa m’Baibulo nawonso ankalakwitsa zinazake. Yehova sayembekezera kuti atumiki ake azichita zinthu mosalakwitsa kanthu. (Werengani Salimo 103:13, 14.) Yehova amasangalala mukamayesetsa kuchita zabwino. Iye ndi wokonzeka kukuthandizani. Ndipotu Yehova amatitsimikizira kuti ‘palibe chimene chingatilekanitse ndi chikondi chake.’​—Werengani Aroma 8:38, 39.

  • N’zotheka Kupirira Ena Akamakuzunzani
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • Anthu akhoza kuyamba kutizunza kapena kutitsutsa ndi cholinga choti tisiye kutumikira Yehova. Koma kodi zimenezi ziyenera kutidabwitsa?

      1. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyembekezera kuti anthu akhoza kuyamba kutizunza?

      Baibulo limanena kuti: “Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.” (2 Timoteyo 3:12) Yesu anazunzidwa chifukwa sanali mbali ya dziko la Satanali. Nafenso sitili mbali ya dzikoli, choncho sitimadabwa maboma komanso zipembedzo za m’dzikoli zikamatizunza.​—Yohane 15:18, 19.

      2. N’chiyani chingatithandize kukonzekera chizunzo?

      Tiyenera kuyamba panopa kudalira kwambiri Yehova. Tsiku lililonse tizipeza nthawi yopemphera kwa iye komanso kuwerenga Mawu ake. Tiyeneranso kumachita nawo misonkhano yampingo nthawi zonse. Zinthu zimenezi zingakuthandizeni kuti musamafooke mukamakumana ndi mayesero ngakhale ochokera kwa anthu am’banja lanu. Mtumwi Paulo yemwenso nthawi zambiri ankazunzidwa analemba kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa.”​—Aheberi 13:6.

      Tingakonzekerenso chizunzo tikamayesetsa kulalikira nthawi zonse. Kulalikira kumatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova komanso kuti tisamaope anthu. (Miyambo 29:25) Mukamalalikira molimba mtima panopa, simudzavutika kupitiriza kulalikira boma likadzaletsa ntchito yathu.​—1 Atesalonika 2:2.

      3. Kodi kupirira tikamazunzidwa kuli ndi ubwino wotani?

      N’zoona kuti sitimasangalala tikamazunzidwa. Komabe, tikamapirira pozunzidwa chikhulupiriro chathu chimalimba kwambiri. Timakhala pa ubwenzi wolimba kwambiri ndi Yehova chifukwa pa nthawi imene tikuona kuti sitingakwanitse kupirira, m’pamene iye amatithandiza. (Werengani Yakobo 1:2-4.) Yehova akamaona kuti tikuzunzidwa, zimamupweteka kwambiri. Koma iye amasangalala akaona kuti tikuyesetsa kupirira. Baibulo limati: “Ngati mukupirira povutika chifukwa cha kuchita zabwino, zimenezo n’zabwino kwa Mulungu.” (1 Petulo 2:20) Tikapitiriza kukhala okhulupirika anthu ena akamatizunza, Yehova adzatidalitsa potipatsa moyo wosatha m’dziko lomwe simudzakhala anthu otitsutsa.​—Mateyu 24:13.

      FUFUZANI MOZAMA

      Onani chifukwa chake n’zotheka kupirira ena akamatizunza komanso mmene Yehova adzatidalitsire tikapitiriza kukhala okhulupirika.

      Mtsikana akupitabe kukaphunzira Baibulo ngakhale makolo ake akumutsutsa kwambiri.

      4. N’zotheka kupirira mukamatsutsidwa ndi anthu am’banja lanu

      Yesu ankadziwa bwino kuti anthu ena am’banja lathu sangagwirizane ndi zimene tasankha zoti tizilambira Yehova. Werengani Mateyu 10:34-36, kenako mukambirane funso ili:

      • Mogwirizana ndi lembali, kodi achibale athu angachite chiyani tikasankha kutumikira Yehova?

      Kuti muone chitsanzo cha zimenezi, onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.

      VIDIYO: Yehova Anatitenga (5:13)

      • Kodi mungatani ngati wachibale kapena mnzanu akufuna kuti musiye kutumikira Yehova?

      Werengani Salimo 27:10 ndi Maliko 10:29, 30. Pambuyo powerenga lemba lililonse, mukambirane funso ili:

      • Kodi lonjezoli lingakuthandizeni bwanji achibale kapena anzanu akamakutsutsani?

      5. Musasiye kutumikira Yehova mukamazunzidwa

      Timafunika kulimba mtima kuti tipitirize kutumikira Yehova anthu ena akamatizunza. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.

      VIDIYO: Anachita Zinthu Molimba Mtima Pamene Ankazunzidwa (6:27)

      • Kodi zitsanzo zamuvidiyoyi zakulimbikitsani bwanji?

      Werengani Machitidwe 5:27-29 ndi Aheberi 10:24, 25. Pambuyo powerenga lemba lililonse, mukambirane funso ili:

      • N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kulambira Yehova ngakhale boma litatiletsa kusonkhana kapena kugwira ntchito yathu yolalikira?

      6. Yehova adzakuthandizani kuti mukwanitse kupirira

      A Mboni za Yehova amisinkhu yosiyanasiyana padziko lonse amapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika ngakhale akuzunzidwa. Kuti muone zimene zimawathandiza kupirira, onerani VIDIYO. Kenako mukambirane funso ili:

      VIDIYO: Yehova Adzandilimbitsa (3:40)

      • Muvidiyoyi, n’chiyani chinathandiza abale ndi alongowa kuti akwanitse kupirira?

      Werengani Aroma 8:35, 37-39 ndi Afilipi 4:13. Pambuyo powerenga lemba lililonse, mukambirane funso ili:

      • Kodi lembali likusonyeza bwanji kuti n’zotheka kupirira mukamakumana ndi mayesero ena alionse?

      Werengani Mateyu 5:10-12, kenako mukambirane funso ili:

      • N’chifukwa chiyani mukhoza kumasangalalabe pamene mukuzunzidwa?

      A Mboni za Yehova omwe anapirira pozunzidwa komanso potsekeredwa m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo.

      A Mboni za Yehova ambirimbiri sanasiye kutumikira Yehova ngakhale pamene ankazunzidwa. Nanunso mungakwanitse

      ZIMENE ENA AMANENA: “Sindingakwanitse kupirira ena akamandizunza.”

      • Kodi ndi malemba ati amene angathandize munthu wotereyu kukhala wolimba mtima?

      ZOMWE TAPHUNZIRA

      Yehova amayamikira khama lomwe timasonyeza pomutumikira ngakhale ena akutizunza. Iye angatipatse mphamvu zomwe zingatithandize kupirira.

      Kubwereza

      • N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kuyembekezera kuzunzidwa?

      • Kodi muyenera kuchita chiyani panopa pokonzekera chizunzo?

      • N’chiyani chingakuthandizeni kuti musamakayikire kuti mukhoza kumatumikirabe Yehova mokhulupirika ngakhale mukukumana ndi mayesero?

      Zolinga

      ONANI ZINANSO

      Onani mmene Yehova anathandizira m’bale wina kupirira atakana kulowerera ndale.

      Anapirira Ngakhale Ankazunzidwa (2:34)

      Onani chimene chinathandiza anthu am’banja lina kuti azitumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri ngakhale ankazunzidwa.

      Anatumikira Yehova Panthawi Imene Zinthu Zinali Zitasintha (7:11)

      Onani zimene mungachite kuti muzichita zinthu molimba mtima mukamazunzidwa.

      “Tizikonzekera Kuti Tidzathe Kupirira Pozunzidwa” (Nsanja ya Olonda, July 2019)

      Kodi tizitani anthu am’banja lathu akamatitsutsa? Nanga tingatani kuti tizichitabe zinthu mwamtendere komanso kuti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova?

      “Choonadi Sichibweretsa ‘Mtendere Koma Lupanga’” (Nsanja ya Olonda, October 2017)

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena