Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 7/15 tsamba 4-7
  • Kumangirira Chikhulupiriro Kuti Chisunthe Mapiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kumangirira Chikhulupiriro Kuti Chisunthe Mapiri
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Zidina” Zomangira Chikhulupiriro
  • “Zidina” Zina Zomangira Chikhulupiriro
  • “Tiwonjezereni Chikhulupiriro”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Muzisonyeza Kuti Mumakhulupirira Malonjezo a Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Chikhulupiriro Chimatipatsa Mphamvu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Sonyezani Chikhulupiriro Chozikidwa pa Chowonadi
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 7/15 tsamba 4-7

Kumangirira Chikhulupiriro Kuti Chisunthe Mapiri

“NDIRI ndi chikhulupiriro; aha, ndithandizeni ine kukhala nacho chowonjezereka!” Awa anali mawu a atate wodera nkhawa wamwana wodwala khunyu wotchulidwa m’nkhani yapitayo. (Marko 9:24, The Living Bible) Chingakhale chakuti ganizo limeneli likuwunikiridwanso m’maganizo anu. Ngati ndi tero, khalani otsimikiziridwa kuti simuli nokha. Mikhalidwe yadziko lerolino imakhoterera kukufooketsa chikhulupiriro mwa Yehova ndi Mawu ake. Nthanthi yokana Mulungu, kukonda zinthu zakuthupi, chiwawa mu matchalitchi, ndi kuwonjezeka kochititsa mantha kwaupandu zonse zimayedzamira pa kuchepsya chikhulupiriro chowona. Chotero, loyenera koposa, linali funso la Yesu Kristu, “Koma Mwana wa munthu pakudza iye, adzapeza chikhulupiriro padziko lapansi kodi?”​—Luka 18:8.

Pachochitika china, ngakhale atumwi a Yesu anachonderera, “Mutiwonjezere chikhulupiriro;” Komabe, m’malo mwakuwapatsa iwo chikhulupiriro chowonjezereka mozizwitsa, iye anati: “Mukakhala nacho chikhulupiriro ngati kambewu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, ‘Uzulidwe nuwokedwe m’nyanja!’ ndipo ukadamvera inu.” (Luka 17: 5, 6) Chotero, kodi ndimotani mmene tingapezere chikhulupiriro chowonjezereka?

Kumangirira Chikhulupiriro

Mtumwi Paulo analemba: “Ndipo adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira? . .Chomwecho chikhulupiriro chidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mawu a Kristu.” (Aroma 10:14-17) Chotero, icho chitsatira kuti, ngati tifuna chikhulupiriro chowonjezereka, tiyenera kumva ndi kutenga chidziŵitso cha Malemba. Chimenecho ndi chimene munthu wakufa ziwalo wotchulidwa pamwambayo anachita. Mboni za Yehova zinaphunzira Baibulo ndi iye, anapeza chikhulupiriro, ndipo kenaka anagwiritsira ntchito zimene iye anaphunzira m’moyo wake wa tsiku ndi tsiku. Chotero iye anapeza chikhulupiriro kuti asunthe zokhumudwitsa zonga phiri m’moyo wake.

Chimatenga nthawi kusonkhanitsa chitsimikiziro chokhutiritsa monga maziko a chikhulupiriro. (Ahebri 11:1) Ndipo chimafunikira kuyesetsa. Kodi muli wofunitsitsa kuwononga nthawi ndi kuika kuyesetsa kwanu pa maziko okhazikika kotero kuti musonkhanitse chitsimikiziro chofunikira kumangirira chikhulupiriro?

“Zidina” Zomangira Chikhulupiriro

Ntchito ya kumangirira chikhulupiriro ingafanizidwe ndi kumanga nyumba. Ngakhale nyumba zazikulu kwambiri zimapangidwa ndi chidina chimodzi ndi chimodzi. Chidina chirichonse chimaikidwa m’malo ake ndi mazana a zidina zina kupereka kwa nyumbayo kulimba kofunikira kulaka mphepo yaikulu limodzinso ndi kusakaza kwanthaŵi. Chikhulupiriro, nachonso, chazikidwa pa “chidina” chimodzi ndi chimodzi cha chitsimikiziro chosamalitsa chondandalikidwa m’chigwirizano ndi china. “Chidina” chirichonse chidzawonjezera chitsimikiziro chakuti Mulungu alipo, kuti ali Mlengi wa zinthu zonse, ndikuti iye ali ndi cholinga chophatikizapo chilengedwe chake chaumunthu. Kodi nchiyani chimene chiri “zidina” zomangira zimenezi?

Choyambirira, yang’anani pathupi lanu lenilenilo. Kodi simukuwona chitsimikiziro chokhutiritsa cha Mlengi, mwachitsanzo, bongo lanu losangalatsa koposa​—chinthu chomwe sayansi siingathe ngakhale kulota za kuchitsanzira icho? Kodi munganene monga mmene anachitira wamasalmo, “Chipangidwe changa nchowopsya ndi chodabwitsa”? (Masalmo 139:14) Ngati mungatero, ndiye kuti muli ndi “chidina” chimodzi chimene mudzamangira chikhulupiriro chanu.

Kodi mumapeza chitsimikiziro chowonjezereka cha Mlengi wachikondi mu zinthu zosiyanasiyana zosawerengeka ndi kukongola kwa mitengo, zomera, ndi maluwa? Kodi mungawone chitsimikiziro choterocho mu zinyama, mbalame, ndi zolengedwa zam’madzi ndi m’kudalirana kwawo kwa chikatikati limodzinso ndi kufunika kwawo ku mtundu wa munthu? Ngati tiri ofunitsitsa kumvetsera, “tingamve” zonse za izo zikulengeza kuti, ‘Mulungu aliko!’​—Aroma 1:20.

Ngakhale kuli tero, kukhulupirira mu kukhalako kwa Mlengi sikuli kokwanira. Kuti tiyankhe mafunso onena za iye ndi zolinga zake, tikafunikira vumbulutso lochokera kwa wosawoneka ameneyu, Mulungu wanzeru zonse. Ndipo tiri nalo! Kuti? Mu Baibulo. Koma, ambiri salingalira magwero amenewo a chidziwitso kukhala odalinka monga chilengedwe chowona ndi maso chotizinga ife.

Komabe, pali chitsimikiziro chochuluka, chitsimikiziro chokhutiritsa, chakuti Baibulo liri bukhu louziridwa ndi Mulungu. Mwachitsanzo, kugwirizana komwe kuli pakati pa alembi ake​—chifupifupi 40 a iwo, akumalemba mkati mwa zaka mazana 16—​chiri chitsimikiziro cha Mlembi m’modzi, Yehova Mulungu. Nthawi ndi nthawi, zopeza za sayansi yowona ndi zofukulidwa za zinthu zofotseredwa kale zatsimikiziranso Baibulo kukhala lowonadi ndi lodalirika. Mwachitsanzo, wodziwa za mlengalenga Robert Jastrow analemba kuti: “Tsatanetsatane wake amasiyana, koma mbali zofunika kwambiri mu nkhani za kudziwa za mlengalenga ndi baibulo za Genesis ziri zofanana: Ndandanda ya zochitika zotsogolera ku munthu zinayambika mwadzidzidzi ndipo mwamphamvu pa nyengo yeniyeni mu nthawi, mkuwoneka kwa kuwala ndi mphamvu.”

Talingalirani kokha chitsanzo chimodzi cha mmene odziwa za zofotseredwa zakale anatsimikizirira mbiri ya Baibulo. Pa 2 Mafumu 18: 13-15, timawerenga kuti: “Chaka chakhumi ndi zinayi cha Mfumu Hezekiya, Sanakeribu mfumu ya Asuri anakwerera midzi yonse ya malinga ya Yuda, nailanda.” Panthawi imeneyo “mfumu ya Asuri anaikira Hezekiya mfumu ya Ayuda matalente mazana atatu a siliva ndi matalente makumi atatu a golidi.” Mkutsimikizira, mkati mwa zaka za zana la 19 katswiri wodziwa za zinthu zofotseredwa kale A. H. Layard anapeza chomwe chitchedwa Prism ya Mfumu Sanakeribu. Malemba ake ozokotedwa amawerenga: “Koma ponena za Hezekiya Myuda, amene sanagonjere ku goli langa, mizinda yake ya malinga, 46 yamphamvu, . . . ndinaigwira ndi kuitenga. . . Ndinawonjezera pa chopereka chakale, ndikukhazikitsa pa iye monga chopereka chawo cha pachaka, msonkho . . . matalente 30 a golidi ndi matalente 800 a siliva.” Kugwirizana kodabwitsa ku mbiri ya Baibulo, kusiyana kokha mu unyinji wa msonkho wa siliva!

“Zidina” Zina Zomangira Chikhulupiriro

Zowonekera kwambiri “Zidina” zomangira ziri izo zokongoletsedwa ndi kukwaniritsidwa kwa maulosi a Baibulo. Ulosi uli kuneneratu za chinthu chodzachitika mtsogolo. Pamene chinthu choterocho chichitika, chimatsimikizira choneneratucho kukhala chowona. Maulosi oterowo ali osafikira kuthekera kwa munthu, ndipo Baibulo molondola limanena: “Pakuti ndi kale lonse ulosi sunadza ndi chifuniro cha munthu, koma anthu analankhula kuchokera kwa Mulungu pamene anagwidwa ndi mzimu woyera.” (2 Petro 1:21, NW) Kuyang’ana pa ochepa a maulosi oterowo a Baibulo motsimikizirika chiri cholimbikitsa chikhulupiriro.

Chifupifupi 732 B. C.E., Yesaya ananeneratu za kugwa kwa Babulo pamanja a Amedi ndi a Peresiya, ngakhale kupereka dzina la wogonjetsayo, Koresi. Mozizwitsa, ulosi umenewu unaperekedwa zaka 200 Koresi asanatenge Babulo! M’mbali yake, ulosiwo umalankhula za Yehova monga “Amene ati kwa nyanja yakuya, ‘iphwa, ndipo ndidzaumitsa nyanja zako.’ ” Chinanenedweratu kuti Mulungu ‘adzatsegula pamaso pa Koresi zitseko ndipo zipata sizidzatsekedwa.’ “Ndidzathyola zitseko zamkuwa, ndi kudula pakati akapichi achitsulo,” anatero Yehova, “ndipo ndidzakupatsa iwe chuma cha mumdima.” (Yesaya 44:24-45:3) Kodi ndimotani mmene ulosi umenewu unakwaniritsidwira?

Zinachitika pa usiku wa phwando lakuledzera kwa Babulo ndi akalonga ake. Mosazindikiridwa ndi pansi pa kuphimbidwa ndi mdima, gulu lankhondo la Koresi linagwira ntchito molimbika kupatutsa madzi a Mtsinje wa Firate, womwe unadutsa kupyola pakati pa mzinda. Ichi chinatheketsa asilikari ankhondo kulowa mu Babulo kudzera mgombe la mtsinje. Zipata za mtsinje molekerera zinasiyidwa zotseguka mkati mwa phwandolo. Chotero, Amedi ndi a Peresiya analibe vuto mkutenga Babulo ndi chuma chake. Ulosi wa Yesaya unakwaniritsidwa m’tsatanetsatane wake wonse.

Yehova Mulungu anawonanso kukhala choyenera kumupanga Yesu Kristu maziko achidwi a maulosi ambiri onenera tsatanetsatane wakubadwa kwake, moyo wake, utumiki wake, ndi imfa, ena a iwo analembedwa zaka mazana pasadakhale. Mwachitsanzo, chinanenedweratu kuti iye adzabadwira mu fuko la Yuda la banja la Davide (Genesis 49:10; Yesaya 11:1, 2), ndipo m’mudzi wa Betelehemu. (Mika 5:2) Woyanjana naye wake mmodzi akakhala wosakhulupirika ndipo akampereka iye ndi zidutswa 30 za siliva. (Masalmo 41:9; Zekariya 11:12) Maele akapangidwa pa zovala zake. (Masalmo 22:18) Iye akalasidwa, koma palibe ngakhale limodzi la mafupa ake likasweka. (Zekariya 12:10; Masalmo 34:20) Danieli 9:24-27 linaneneratu zakubwera kwa Yesu monga Mesiya, kapena Kristu, pambuyo pa zaka za milungu 69, nyengo ya zaka 483 kuchokera mu 455 B. C.E. kufikira ubatizo wa Yesu mu 29 C.E. Thekala “mlungu” (zaka 31/2) pambuyo pake, mu 33 C.E. Yesu “anadulidwa” mu imfa monga kunanenedweratu. Tsatanetsatane wina wa ulosiwo unakwaniritsidwanso.

Izi ziri kokha “zidina” zochepa zomwe zingagwiritsiridwe ntchito kumanga chikhulupiriro chomwe chingasunthe mapiri. Kudzisonkhanitsa zonse za izo pamodzi ndi kuziika izo m’malo ake kumatenga nthawi, kuyesetsa, ndi kupirira. Koma icho chachitika. John, wokhala mu Santos, Brazil, angatsimikizire kuti icho chingachitike. Zaka zingapo zapita, iye anali wosiyana kulinga ku chipembedzo, analibe chikhulupiriro mu Baibulo, ngakhale kuti anakhulupirira kuti Mulungu alipo. John anavomereza ku maulendo a m’modzi wa Mboni za Yehova. Pomalizira kukambitsirana kwa mlungu ndi mlungu kunamukhutiritsa John kuti Baibulo silinali bukhu wamba, ndipo iye potsirizira pake “analandira ilo, osati monga mawu a anthu, koma, monga mmene ilo mowona liri, monga mawu a Mulungu.” (1 Atesalonika 2:13) Chinatenga nthawi, koma maphunziro a Baibulo opitirira anamuthandiza John kumvetsetsa chifuno cha Mulungu kulinga ku mtundu wa anthu. Pomalizira, mu 1970 iye anabatizidwa monga m’modzi wa Mboni za Yehova. Tsopano, monga mkulu wosankhidwa wa mpingo, iye akuthandiza ena kumangirira ndi kusunga chikhulupiriro chawo.

Kodi mukufuna thandizo m’kumangirira chikhulupiriro chanu? Ngati ndi tero, kumbukirani kuti “chikhulupiriro chimatsatira chinthu chomvedwa. Ndipo kenaka chinthu chomvedwa chiri kupyolera mwa mawu a Kristu.”(Aroma 10:17) Mboni za Yehova zoposa 3, 000, 000 mokangalika zikubukitsa “mawu onena za Kristu” ndi Ufumu wa Mulungu m’maiko oposa 200. Izo zidzakhala zosangalala kukuthandizani inu kuphunzira zochuluka ponena za Mawu a Mulungu kupyolera mu kukambitsirana kwaulere kwa Baibulo.

Khalani otsimikiza kuti nthawi imene mudzapereka kumvetsera ku “chinthu chomvedwa” idzakhala nthawi yowonongedwa bwino. Ingakuthandizeni inu kumangirira chikhulupiriro chomwe chimasuntha mapiri. Ichi, kenaka, chidzatsogolera ku moyo wosatha, “pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wa kukhulupirira iye asatayike koma akhale nawo moyo wosatha.”​—Yohane 3:16.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 7]

“ZIDINA”Zomangira Chikhulupiriro

Yamikirani zinthu zime ne Yehova anazipanga

Landirani Baibulo monga Mawu a Mulungu

Dziwani mmene phunziro la zinthu zofotseredwa kale ndi mbiri yakale zimatsimikizirira mbiri ya Baibulo

Santhulani kukwamritsidwa kwa maulosi a Baibulo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena