Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 7/8 tsamba 12-13
  • Kodi Ayuda Ndiwo Anthu Osankhidwa a Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ayuda Ndiwo Anthu Osankhidwa a Mulungu?
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Fanizo Lamphamvu
  • “Otsalira” Okha Akhala Okhulupirika
  • “Amene Sanakhala Anthu Anga” Akhala “Anthu Anga”
  • Anabadwira mu Mtundu Wosankhika wa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Hoseya
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Ulosi wa Hoseya Umatithandiza Kuyenda ndi Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 7/8 tsamba 12-13

Lingaliro la Baibulo

Kodi Ayuda Ndiwo Anthu Osankhidwa a Mulungu?

KUKHAZIKITSIDWA kwa kwawo kwa Ayuda mu 1948 kudali chochitika chopweteka kwa akatswiri a maphunziro achipembedzo a Chikristu Chadziko. Kwa zaka mazana ambiri adaphunzitsa kuti Ayuda anaweruzidwa kuyendayenda m’dziko lapansi chifukwa chakuti anachimwira Kristu, ndipo tsopano “Myuda woyendayendayo” sakayendayendanso.

Monga momwe zochitika zaposachedwapa za ku Middle East zikupitirizira kusumika chisamaliro pa anthu Achiyuda, mafunso akubuka pa nkhani zomwe kwa nthaŵi yaitali zinalingaliridwa kuti zinathetsedwa. Kodi Ayuda adakali anthu osankhidwa a Mulungu? Kodi Mulungu akusonyeza tsopano chiyanjo chapadera kwa Ayuda?

Zaka mazana angapo apitawo, Mulungu anauza Aisrayeli kuti: ‘Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mawu anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa chapadera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa; ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika.’ (Eksodo 19:5, 6) Mitundu yonse inali ya Mulungu, koma Aisrayeli akanakhala chuma chake chapadera, ndipo potsirizira pake kutumikira monga ansembe m’malo mwa anthu.

Koma kodi unansi wapadera umenewu ndi Mulungu unali wopanda malire? Ayi! Mulungu adati: ‘Ngati mudzamvera mawu anga . . . ndidzakuyesani chuma changa chapadera.’ Chotero kupitiriza kwawo kukhala ndi unansi wapadera ndi Mulungu kunali ndi polekezera, kodalira pa kupitiriza kwawo kukhala okhulupirika kwa iye.

Fanizo Lamphamvu

Ichi chinamveketsedwa ndi zochitika za m’zaka za zana lachisanu ndi chitatu B.C.E., m’masiku a mneneri Hoseya. Mosasamala kanthu za kulandira chiyanjo chapadera monga anthu osankhidwa a Mulungu, Aisrayeli ambiri analeka kulambira kowona kwa Yehova. Kodi Yehova anachitaponji? ‘Sindidzachitiranso chifundo nyumba ya Israyeli, kuti ndiwakhululukire konse. . . . Inu sindinu anthu anga, ndipo Ine sindine wanu.’ (Hoseya 1:6, 9) Motero, Aisrayeli opatuka amenewo sakanakhalanso m’chiyanjo cha Mulungu. Otsalira okhulupirika okha ndiwo amene tsiku lina akakhala ndi mwaŵi wa kubwezeretsedwa ndi kukumana ndi madalitso aumulungu.—Hoseya 1:10.

Mowonadi ku ulosi umenewu, Mulungu analola Aisrayeli kutengedwa andende ndi adani awo ndipo kachisi wawo anawonongedwa, kusonyeza mwamphamvu kutayika kwa unansi wawo wovomerezeka ndi iye. Otsalira okhulupirika okha a Aisrayeli (panthaŵiyo odziŵika monga Ayuda) anabwerera kuchokera ku ndende mu 537 B.C.E. ndikumanganso kachisi wa Yehova, kachiŵirinso kusangalala ndi chiyanjo cha Yehova monga anthu ake osankhidwa.

“Otsalira” Okha Akhala Okhulupirika

Komabe, m’zaka mazana zomwe zinatsatira, Ayuda anagwidwa ndi chisonkhezero cha nthanthi Zachigiriki—monga ngati chiphunzitso cha Plato cha kusafa kwa moyo—zokhala ndi ziyambukiro zoipa ku kulambira kwawo. Kulambira kumeneko sikukakhala kozikidwa pa ziphunzitso za Mose ndi aneneri Achihebri.

Kodi Yehova akapitirizabe kuwona Ayuda kukhala anthu ake osankhidwa? Pozindikira kuti ambiri anapatuka ku kulambira kwabwino kwa Yehova, Yesu anati: ‘Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.’ (Mateyu 21:43) Polephera kulabadira chenjezo limenelo, ambiri anapitiriza kupatuka ndi kukana Yesu monga wodzozedwa wa Yehova. Chifukwa chake, sipanapite nthaŵi yaitali kuti Mulungu alole kachisi womangidwansoyo kuwonongedwa mu 70 C.E. (Mateyu 23:37, 38) Kodi ichi chinatanthauza kuti Mulungu tsopano anali kukana Ayuda onse?

Monga Paulo, mtumwi Wachiyuda wa Kristu, analongosola kuti: ‘Mulungu sanataya anthu ake amene Iye anawadziŵiratu. . . . Choteronso nthawi yatsopano chiripo chotsalira monga mwa kusankha kwa chisomo.’ (Aroma 11:2, 5) Monga momwe ambiri angaitanidwire ku phwando la ukwati koma ochepera okha ndiwo amapezekako, Mulungu adaitana mtundu wonse Wachiyuda kulowa unansi wapadera ndi iye, koma otsalira okha a ameneŵa ndiwo anasungabe unansi wathithithi wapadera umenewo mwa kukhulupirika kwawo. Kuleza mtima kwa Mulungu kudalidi kusonyezedwa kwa chisomo!

“Amene Sanakhala Anthu Anga” Akhala “Anthu Anga”

Wotsalira Wachiyuda wokhulupirika ameneyu anagwirizana ndi osakhala Ayuda amenenso anafuna kutumikira Mulungu. Ngakhale kuti makolo awo sadali mu unansi wapadera ndi iye, Yehova anali wofunitsitsa tsopano kulandira okhulupirika ameneŵa osakhala Ayuda kukhala anthu ake. Pozindikira chimenechi, Paulo adalemba kuti: ‘Ngati Mulungu . . . anatiitana [ife], si a mwa Ayuda okha okha, komanso a mwa anthu amitundu [osakhala Ayuda]? Monga atinso mwa Hoseya, Amene sanakhala anthu anga, ndidzawatcha anthu anga.’—Aroma 9:22-25.

Motero, onse aŵiri Ayuda ndi osakhala Ayuda akanakhala anthu osankhidwa a Mulungu, ndi chiyembekezo cha kutumikira monga ansembe m’malo mwa mtundu wonse wa anthu. Polankhula za alambiri okhulupirika a chiyambi cha mtundu wosiyana, mtumwi Wachikristu Petro, Myuda wachibadwa, analemba kuti: ‘Inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, . . . inu amene kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu.’ (1 Petro 2:9, 10) Umenewu ndiwo “mtundu,” anthu okhala ndi mikhalidwe yaumulungu, umene Yesu anati ukabala ‘zipatso za ufumu wa Mulungu’ ndi umene ukasangalala ndi unansi wapadera ndi Yehova.—Mateyu 21:43.

Mulungu anali kufuna mkhalidwe wokhulupirika ndi wolungama m’kusankha kwake oyembekezera kukhala ansembe ameneŵa, osati chibadwa chapadera. Monga mmene Petro anadziŵitsira: ‘Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.’—Machitidwe 10:34, 35.

Chotero, Mulungu samapereka konse chiyanjo chapadera kwa munthu aliyense pamaziko a kubadwa kwake. Iye amapatsa anthu a mtundu uliwonse mwaŵi wakumangirira unansi ndi iye. Lolani kuti tisonyeze kuti ndife ofuna kukhala anthu a Mulungu mwa kukhulupirika kwathu ndi mkhalidwe.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena