-
3 | Yesetsani Kuchotsa Mtima Wachidani M’maganizo MwanuNsanja ya Olonda (Yogawira)—2022 | Na. 1
-
-
Baibulo Limati:
“Sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.”—AROMA 12:2.
Zimene Lembali Limatanthauza:
Mulungu amadziwa bwino zimene timaganiza. (Yeremiya 17:10) Choncho pali zambiri zomwe tiyenera kuchita kuwonjezera pa kupewa kulankhula kapenanso kuchita zinthu zosonyeza kuti tili ndi mtima wachidani. Chidani chimayambira mumtima ndiponso m’maganizo athu ndiye n’chifukwa chake tiyenera kuthetseratu chidani mumtima komanso m’maganizo mwathu. Tikachita zimenezi m’pamenedi ‘tingasandulike’ komanso kuthetsa chidani.
-